Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Kodi Zinangochitika Zokha?

Chikumbu Chodziwa Komwe Kukuyaka Moto

Chikumbu Chodziwa Komwe Kukuyaka Moto

Nthawi zambiri kutchire kukamayaka moto zinyama zambiri zimathawa. Koma pali chikumbu chinachake chakuda chomwe chimapita komwe kuli motoko. N’chifukwa chiyani chimachita zimenezi? N’chifukwa choti mitengo imene yangopsa kumene imakhala malo abwino oti chikumbuchi chiikire mazira. Komanso chifukwa chakuti nyama zambiri zimene zimadya chikumbuchi zimakhala zitathawa, chikumbucho chimapeza mwayi wokudya ndi kuikira mazira popanda chosokoneza. Koma kodi chimadziwa bwanji kumene kuli moto?

Taganizirani izi: Pafupi ndi miyendo yapakati pa chikumbuchi pali kachiwalo kena kamene kamachithandiza kudziwa kumene nkhalango ikupsa. Zimenezi zimachititsa kuti chiyambe kulowera kumene kukuyaka motoko.

Koma chikumbuchi chilinso ndi tinyanga tomwe timathandiza kuti chidziwe komwe kukuyaka moto. Mitengo imene zikumbu zimakonda kuikira mazira ikamapsa, imatulutsa fungo ndipo zikumbuzo zimadziwa kumene kukuchokera kafungoko mothandizidwa ndi tinyangato. Akatswiri ofufuza amanena kuti tinyanga ta chikumbu timatha kununkhiza mtengo womwe ukufuka utsi ngakhale uli pamtunda wa pafupifupi kilomita imodzi. Chifukwa cha zinthu ziwiri zimenezi, chikumbu chimatha kudziwa kumene nkhalango ikuyaka, ngakhale chitakhala pamtunda wa makilomita oposa 48.

Akatswiri akufufuza mmene tiziwalo timeneti ta chikumbu timagwirira ntchito n’cholinga choti apange zipangizo zamakono zothandiza kudziwa ngati pamalo payamba kuyaka moto. Zipangizo zimene zilipo panopa zimafunika kukhala pamalo ozizira kuti zizitha kudziwa ngati moto wayamba. Koma asayansi akufuna kuti apange zipangizo zotha kukhala pamalo otentha potengera mmene kachikumbu kamachitira. Akatswiri akuganiza kuti zimene tinyanga ta chikumbuchi timachita ziwathandiza kupanga zipangizo zotha kusiyanitsa utsi umene umatuluka nkhalango ikamapsa ndi utsi wa zinthu zina.

Akatswiri amagoma ndi mmene chikumbuchi chimapezera malo oti chiikire mazira. Katswiri wina wofufuza zikumbu pa yunivesite ya Cornell, ku United States, dzina lake E. Rich­ard Hoebeke, ananena kuti: “Ndimadabwa ndi mmene zikumbuzi zimadziwira malo oyenera kuikira mazira. Kunena zoona anthufe timadziwa zochepa zokhudza zikumbu zotha kudziwa komwe kukuyaka moto.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti chikumbu chizitha kudziwa komwe kukuyaka moto, kapena ndi umboni wakuti alipo winawake amene anachilenga?