Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

 Zochitika Padzikoli

M’dziko la Georgia, lomwe lili kum’mwera chakum’mawa kwa Europe, “chiwerengero cha mabanja amene akutha chawonjezereka kwambiri m’zaka 10 zapitazi.” Ambiri mwa mabanja amene akutha ndi a achinyamata osapitirira zaka 20.—FINANCIAL, GEORGIA.

Ku Ireland, ana 17 pa 100 alionse, azaka zapakati pa 11 ndi 16, “anaperekapo dzina lawo kwa anthu osawadziwa pa Intaneti.” Ndipo ana 10 pa 100 alionse anatumizapo “adiresi yawo ya pa Intaneti, nambala ya foni kapena zithunzi zawo kwa anthu osawadziwa.”—THE IRISH SOCIETY FOR THE PREVENTION OF CRUELTY TO CHILDREN.

Nthawi zambiri anthu ndi amene amayatsa moto umene umawononga nkhalango zambiri. Nkhalango zochepa zokha ndi zimene zimapsa ndi moto woyamba wokha.—PRESSEPORTAL, GERMANY.

Akuti “munthu mmodzi pa anthu 10 alionse ku America [kuyambira a zaka 12] anavomera kuti amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo monga cocaine, heroin ndi chamba.”—USA TODAY, U.S.A.

Anthu Odziletsa Amakhala Osangalala

Magazini ya Time inanena kuti: “Akatswiri ofufuza apeza kuti achinyamata amene amalephera kudziletsa, akakula amadwaladwala, amakhala ndi mavuto a zachuma komanso amadzachita zinthu zophwanya malamulo.” Akatswiriwa anafufuza anthu oposa 1,000 kuyambira atangobadwa mpaka atakwanitsa zaka 32. Iwo anapeza kuti, “ambiri mwa ana amene ankalephera kudziletsa, amene ankafuna kuti zimene akufuna zichitike nthawi yomweyo komanso amene sankachedwa kukhumudwa, ankakumana ndi mavuto atakula. Ena mwa mavutowa ndi kudwaladwala, mavuto a zachuma, kuchita zinthu zophwanya malamulo komanso mabanja awo anatha kapena anali ndi ana apathengo.” Koma magaziniyi inanenanso kuti: “Ngakhale zili choncho, anthu akhoza kuphunzira kudziletsa. Ana amene amaphunzitsidwa kudziletsa ndi makolo awo kapena kusukulu amadzakhala athanzi komanso osangalala akakula.”

Njira Yatsopano Yolangira Madalaivala

Apolisi ku India apeza njira yatsopano yolangira madalaivala amene aphwanya malamulo. Akawagwira, akumawagwiritsa ntchito imene apolisi apansewu amachita. Iwo akuchita zimenezo kuti madalaivalawo adziwe mmene apolisi amavutikira madalaivala akamaphwanya malamulo. Choncho m’malo momangouza madalaivala amene aphwanya malamulo kuti aime n’kuwalipiritsa, apolisi a mu mzinda wa Gurgaon, womwe uli kumpoto chakumadzulo kwa India, akumati akagwira dalaivala, akumamuuza kuti agwire ndi apolisiwo ntchito yolondolera magalimoto kwa mphindi 30 kapena kuposerapo. Madalaivala ena akuona kuti zimenezi zawathandiza kuti aziyenda bwino pamsewu komanso asinthe mmene amaonera ntchito ya apolisi apamsewu. Wachiwiri kwa mkulu wa apolisi, dzina lake Bharti Arora, ananena kuti: “Tsiku lililonse timagwira madalaivala 1,000 ophwanya malamulo, zimene zikutanthauza kuti timakhala ndi apolisi owonjezera okwana 1,000 tsiku lililonse.”