Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhumba N’zofunika Kwambiri Kwathu Kuno

Nkhumba N’zofunika Kwambiri Kwathu Kuno

 Nkhumba N’zofunika Kwambiri Kwathu Kuno

MTSIKANA wina wa zaka 17, dzina lake Enmarie Kani, yemwe amachokera m’dera lina lamapiri ku Papua New Guinea, anati: “Kwathu kuno nkhumba ndi chinthu chofunika kwambiri moti timafunika kuisamalira. Tsiku lina bambo anga anagula kankhumba kakang’ono ndipo anandipatsa kuti ndizikasamalira. Ndinasangalala kwambiri komabe ndinkada nkhawa kuti kakhoza kufa chifukwa kanali kakang’ono kwambiri.”

Kodi Enmarie ankasamalira bwanji kankhumbako? Ndipo n’chifukwa chiyani anthu a m’madera akumidzi ya ku Papua New Guinea amaona kuti nkhumba ndi ndalama? Tamvani zimene Enmarie anauza mtolankhani wa Galamukani!

Kodi umakhala kuti?

Ndimakhala m’mudzi wina womwe uli m’chigawo cha Western Highlands. Ndimakhala ndi makolo anga komanso azibale anga anayi ndipo nyumba yathu ndi yaudzu. Mudzi wathu uli m’mphepete mwa mtsinje womwe umakadutsa m’mapiri komanso m’nkhalango. M’mudzi wonsewo tilimo anthu pafupifupi 50 ndipo aliyense m’mudzimo ndi m’bale wanga.

Anthu ambiri m’mudzi mwathu ndi alimi ndipo kwathu tili ndi munda waukulu womwe timalimamo ndiwo zamasamba, mbatata, maungu,  nkhaka, khofi ndi mbewu zina. Ineyo ndimakonda kulima ndiwo zamasamba komanso kugwira ntchito zina monga kukonza m’nyumba, kuchapa komanso kusamalira nkhumba yathu.

Kodi nkhumba imeneyi umaisamalira bwanji?

Mmene bambo anga ankagula kankhumbaka, kanali kakang’ono moti ndinkatha kukanyamula m’manja. Tsiku lililonse ndinkakapatsa mbatata yokanyakanya n’kuisakaniza ndi nsomba zogaya, madzi, mchere ndi madzi a mzimbe. Kukamazizira usiku, ndinkakaika musaka n’kukakoleka kudenga pafupi ndi pamene takoleza moto. Ndikatero, ine ndinkagona pafupi ndi pamene ndakoleka kankhumbako. Zimenezi zinathandiza kuti kankhumbako kakule komanso kuti kakhale kathanzi.

Kankhumbaka sindinakapatse dzina, ndinkangokaitana kuti Nkhumba basi. Ndinkakasamalira kwambiri ngati kamwana kanga moti ndinkakadyetsa, kukasambitsa komanso ndinkasewera nako. Nakonso kankandikonda moti kankangotsatira kulikonse.

Nkhumbayi itakula, ndinaiphunzitsa kuchita zinthu zina zomwe timachitabe mpaka pano. M’mawa uliwonse ndimaimangirira chingwe n’kupita nayo kumunda wathu wa ndiwo zamasamba, womwe timayenda mphindi 15. Tikafika ndimaimangirira kumtengo kuti izifukulafukula ndi mlomo wake pofunafuna mizu ya mitengo ndi nyongolotsi. Zimenezi zimathandiza kuti nthaka izikhala yachonde. Madzulo ndimabwerera nayo kunyumba, ndisanaitsekere m’khola ndimaipatsa mbatata zophika ndi zosaphika zomwe.

 N’chifukwa chiyani anthu a m’dera lanu amaona kuti nkhumba ndi zofunika kwambiri?

Anthu a m’dera lathu amakonda kunena kuti: “Nkhumba ndi ndalama, ndipo ndalama ndi nkhumba.” Kale anthu asanayambe kugwiritsa ntchito ndalama ankagwiritsa ntchito nkhumba pogula kapena pogulitsa zinthu ndipo amachitabe zimenezi mpaka pano. Mwachitsanzo, nthawi ina kampani yogulitsa magalimoto inkapereka nkhumba kwa aliyense amene wagula galimoto ku kampaniyo. Komanso anthu akamazengana milandu amakonda kulipiritsana ndalama kapena nkhumba ndipo amuna ambiri akafuna kukwatira amapereka nkhumba ngati malowolo kwawo kwa mkazi.

Ndiye kuti mukadya nkhumba mumakhala ngati mwawononga ndalama eti?

Eya. N’chifukwa chake timadya nkhumba pa zochitika zina ngati pa maliro. Komabe anthu a mitundu ina amadya nkhumba zambiri pa maphwando amene amakonza, pofuna kusonyeza kuti ali ndi chuma komanso pofuna kuyamikira zimene anzawo anawachitira nthawi ina.

Kodi nkhumba zanuzo mukufuna kudzapanga nazo chiyani?

Mwachita bwino kunena kuti “nkhumba zanuzo” chifukwa panopa nkhumba ija inaswa ana ndipo posachedwapa tinagulitsa mwana mmodzi pamtengo wa madola 40. Popeza kuti ndife a Mboni za Yehova, tinagwiritsa ntchito ndalamayo ngati thiransipoti ya ku msonkhano, womwe unachitikira m’tawuni ya Banz. Mwina bambo adzagulitsanso ana ena a nkhumbawo kuti agulire zinthu zina pa banja pathu.

Bwanji osamaweta nkhumba zambiri kuti muzipezanso ndalama zambiri?

Cholinga chathu poweta nkhumba sikuti timafuna kulemera koma timangofuna kuti tizipeza zinthu zofunika monga chakudya, zovala ndi malo okhala. Banja lathu limakonda kulambira Yehova Mulungu. Mwachitsanzo timakonda kupita ku misonkhano, kuthandiza anthu ena kuti aphunzire za Mulungu, kuwapatsa zosowa zawo komanso kuchitira zinthu limodzi monga banja. Banja lathu ndilogwirizana ndipo timasangalala ndi zochepa zomwe tili nazo.

Ineyo ndimagwira maganyu olima komanso kusamalira nkhumba. Koma ntchito yanga yaikulu ndi yolalikira komanso kuphunzitsa anthu ena choonadi cha m’Baibulo. Yesu analamula otsatira ake kuti azilalikira n’chifukwa chake mlungu uliwonse ndimakhala wotanganidwa kugwira ntchito imeneyi. (Mateyu 28:19, 20) Ndimafuna kuti mtsogolo muno ndizidzagwira ntchito ku ofesi ya Mboni za Yehova, yomwe ili ku Port Moresby, komwe amamasulira mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo m’zinenero zosiyanasiyana. Komabe ngati zimenezi zidzalephereke, ndidzakhalabe osangalala chifukwa ndidzapitirizabe kutumikira Yehova komanso kukonda kwambiri kuchita zinthu zogwirizana ndi kulambira Mulungu. Ndikuthokoza kwambiri chifukwa cha zinthu zofunika zimene ndimapeza tikagulitsa nkhumba.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 12]

DZIWANI IZI

● Pa chilumba cha New Guinea, pali nkhumba pafupifupi 2 miliyoni. Zimenezi zikutanthauza kuti pa anthu atatu alionse mmodzi ali ndi nkhumba.

● Anthu ambiri kumidzi amaweta nkhumba.

[Mapu patsamba 10]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

INDONESIA

PAPUA NEW GUINEA

AUSTRALIA

INDONESIA

PAPUA NEW GUINEA

PORT MORESBY

WESTERN HIGHLANDS

AUSTRALIA

[Chithunzi pamasamba 10, 11]

Ulendo wa kumunda

[Chithunzi patsamba 11]

Akusambitsa nkhumba

[Chithunzi patsamba 11]

Akusewera nayo