Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Aliyense Amakhudzidwa ndi Zachiwawa

Aliyense Amakhudzidwa ndi Zachiwawa

 Aliyense Amakhudzidwa ndi Zachiwawa

 PAFUPIFUPI aliyense anamva, kuona kapena kuchitiridwapo zachiwawa. Nthawi zambiri tikatsegula wailesi kapena TV timamva nkhani zokhudza zachiwawa zimene zachitika. Masiku ano, anthu akuyenda mwamantha ndipo akakhala kuntchito akumaopa kuti winawake akhoza kuwachitira zachiwawa. Komanso kusukulu ana ena amachitiridwa zachiwawa ndi anzawo. Anthu ambiri amayembekezera kuti akakhala kunyumba palibe choopsa chimene chingawachitikire, komabe anthu ena makamaka azimayi akukhala mwamantha panyumba pawo pomwe. Ndipotu m’mayiko ena, azimayi 70 pa 100 alionse anadandaulapo kuti anachitiridwa zachiwawa ndi wachibale wawo kapena munthu wina amene amakhala naye.

M’mayiko ambiri anthu akuopa kuti mukhoza kuyambika ziwawa kapena zigawenga zikhoza kupha anthu. Chifukwa cha zimenezi m’mayiko ena, makamaka mayiko amene zigawenga zimakonda kupha anthu, boma linaika makamera m’malo osiyanasiyana n’cholinga choti aziona zimene zikuchitika.

Zimenezi zachititsa kuti makampani opanga makamerawa azipeza ndalama zambiri ngakhale kuti chuma sichikuyenda bwino padziko lonse. Koma kodi ndalamazi zimachokera kuti? Ndalama zimenezi ndi zimene anthu amapereka ngati misonkho ku boma. Ndipo anthu ayembekezere kuti ngati maboma atapeza njira zina zapamwamba zokhwimitsira chitetezo, misonkho imeneyi ikhoza kukwera.

Monga taonera, anthu ambiri akuvutika chifukwa cha zachiwawa. Choncho aliyense ayenera kudzifufuza mmene amaonera nkhani zachiwawa komanso mfundo zimene amayendera. Nkhani zotsatira zitithandiza kupeza mayankho a mafunso awa: Kodi zinthu ngati nyimbo ndi mafilimu zimalimbikitsa bwanji zachiwawa? Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatichititse kuti tizikonda zachiwawa? Ndipo tingazipewe bwanji?