Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Takwanitsa Kumanga Nyumba za Ufumu 1,000 M’Malawi

Takwanitsa Kumanga Nyumba za Ufumu 1,000 M’Malawi

 Takwanitsa Kumanga Nyumba za Ufumu 1,000 M’Malawi

“SINDINKALOTA n’komwe kuti zimenezi zingachitike ku Malawi kuno,” anatero Augustine. Iye ankanena za ntchito yaikulu yomanga Nyumba za Ufumu, zomwe ndi malo amene Mboni za Yehova zimalambirira. Malawi ndi dziko laling’ono lomwe lili kum’mwera chakum’mawa kwa Africa ndipo mu 1993, m’dzikoli munali Mboni za Yehova 30,000. Mbonizi zinalibe malo abwino olambirira komanso kuphunzirira Baibulo.

Koma panopa zinthu zasintha kwambiri. M’mwezi wa September mu 2010, Mboni za Yehova ku Blantyre zinamaliza ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu yomwe inachititsa kuti chiwerengero cha Nyumba za Ufumu m’Malawi chifike pa 1,000. * Koma kodi zinatheka bwanji kuti chiwerengero cha Mboni za Yehova chifike 30,000, ntchito yomanga Nyumba za Ufumu isanayambe? Ndipo ntchitoyi itayamba, anakwanitsa bwanji kumanga Nyumba za Ufumu 1,000 m’kanthawi kochepa, m’dziko limenenso anthu ambiri ndi osauka? Nangano ntchito imeneyi yakhudza bwanji Mboni za Yehova komanso anthu ena?

Inali Nthawi Yovuta

Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, Mboni za Yehova, zomwe pa nthawiyo zinkadziwika kuti Ophunzira Baibulo, zinayamba kuphunzitsa choonadi cha m’Baibulo m’Malawi. Pofika mu 1967, chiwerengero cha Mboni za Yehova chinali pafupifupi 17,000. Mofanana ndi Akhristu a m’nthawi ya atumwi, Mboni za Yehova m’dziko limeneli zinkadziwika kuti zimamvera malamulo komanso zimalemekeza akuluakulu aboma. Komanso sizinkalowelera ndale.—Yohane 18:36; Machitidwe 5:29.

Koma chomvetsa chisoni n’chakuti, pofika m’ma 1965, a boma anayamba kudana ndi Mboni za Yehova chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Choncho, mu 1967, boma linaika lamulo loletsa chipembedzo cha Mboni za Yehova. Kenako, a Mboni za Yehova ambiri anachotsedwa ntchito ndipo magulu ena a chipani anayamba kulanda ndiponso kuwononga katundu wawo. Chifukwa chakuti ankazunzidwa kwambiri komanso poopa kuti boma likhoza kuwapha onse, a Mboni za Yehova ambiri anathawira ku Mozambique ndi ku Zambia.

Patapita nthawi, zinthu zinayamba kusintha moti pofika chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1990, Mboni za Yehova zambiri zinayamba kubwerera ku Malawi. Kenako, Mboni za Yehova zinasangalala kwambiri boma litachotsa lamulo loletsa chipembedzo cha Mboni za Yehova pa August 12, 1993. Pa nthawiyi n’kuti Mboni za Yehova zitaletsedwa kwa zaka 26. Komabe zinakumananso ndi vuto lina. Panali Mboni za Yehova zoposa 30,000 m’mipingo yokwana 583 koma panalibe malo abwino olambirira. Ndiyeno kodi akanatani?

Ankakondana Kwambiri

M’kati mwa zaka 6 boma litachotsa lamulo loletsa Mboni za Yehova, a Mboni anagwira ntchito yotamandika kwambiri pomanga Nyumba za Ufumu ndi ndalama zochepa zimene ankapeza. Koma vuto linali lakuti chiwerengero cha Mboni za Yehova chinkakula mofulumira kwambiri kuposa chiwerengero cha Nyumba za Ufumu. Ndiye kodi panafunika kuchita chiyani kuti vutoli lithe? Mfundo ya  m’Baibulo ya pa 2 Akorinto 8:14 inagwira ntchito. Lembali limasonyeza kuti Akhristu a m’madera ena akhoza kuthandiza Akhristu anzawo omwe akufunika thandizo. Potsatira mfundo imeneyi, mu 1999, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linakhazikitsa ntchito yapadera yomanga Nyumba za Ufumu m’mayiko osauka. Chifukwa cha thandizo limeneli, ntchito yomanga Nyumba za Ufumu m’Malawi inapita patsogolo kwambiri. *

Poyamba, a Mboni za Yehova ankachitira misonkhano yawo m’makalasi, m’zisakasa kapenanso pansi pa mitengo. Koma panopa, anthu m’mipingo yokwana 1,230, amakumana kuti alambire Mulungu komanso kuphunzira Baibulo m’Nyumba za Ufumu zabwino. Mboni za Yehova za m’Malawi zimayamikira kwambiri thandizo la abale ndi alongo awo auzimu padziko lonse.

Chinthu china chomwe chinathandiza kwambiri kuti a Mboni m’dzikoli amange nyumba zambiri zolambiriramo m’kanthawi kochepa n’chakuti, ankangofuna kukhala ndi Nyumba za Ufumu zabwino, koma osati zoti anthu azigoma nazo. Cholinga chawo chinali kumanga nyumba zimene zingachititse anthu kulemekeza Mulungu komanso zomwe anthu angasonkhanemo n’kumaphunzira Baibulo.

Anthu Enanso Amapindula ndi Nyumba za Ufumuzi

Poyamba, anthu ena ankanyoza a Mboni za Yehova chifukwa chakuti analibe malo abwino olambirira, moti Mboni zina zinkachita manyazi kuitanira anthu ku misonkhano yawo. Choncho, Mboni za Yehova zinasangalala kwambiri kukhala ndi Nyumba za Ufumu zooneka bwino. Tsopano zinali zosavuta kuitanira anthu ku misonkhano yawo. Mwachitsanzo, atamaliza kumanga Nyumba ya Ufumu yatsopano pa mpingo wina, tsiku lotsegulira Nyumba ya Ufumuyo panafika anthu 698.

Anthu ambiri a Mboni za Yehova komanso anthu ena ananena kuti sankalota n’komwe kuti m’dera lawo mungadzamangidwe nyumba yokongola komanso yolimba ngati imeneyo. Augustine, amene tamutchula poyamba uja, ananena kuti amakumbukira kuti mpingo wina unkachitira misonkhano yake pansi pa mtengo. Iye anafotokoza kuti: “M’nyengo yopanda mvula, zonse zinkayenda bwino. Koma mvula ikayamba tinkakhala pa mavuto aakulu.” Ngati inuyo munapitako m’dera limene kumagwa mvula yamphamvu, mukudziwa bwino zimene Augustine akutanthauza.

Komanso Augustine amakumbukira zimene zinachitika nthawi ina atapita ku mpingo wa Chimwanje. Iye anafotokoza kuti: “Tinkachitira misonkhano yathu m’kanyumba kamitengo kofolera ndi udzu. Koma sitinkadziwa kuti kudenga la kanyumbako kuli kangaude winawake wamkulu komanso woopsa kwambiri. Ndili mkati mokamba nkhani, mwadzidzidzi kangaude uja anagwa pafupi ndi phazi langa. Nthawi yomweyo ndinamva munthu wina amene ankamvetsera nkhaniyo akundiuza kuti, ‘Chipheni! Chipheni!’ Ndinachiphadi, chifukwa  ndikanazengereza mwina bwenzi pano nditafa chifukwa cholumidwa ndi kangaundeyu.” Panopa mpingowu uli ndi Nyumba ya Ufumu yatsopano moti anthu sakumananso ndi mavuto ngati amenewa.

“N’zosiririka Kwambiri”

Kumangidwa kwa Nyumba za Ufumu m’dzikoli kwachititsa kuti anthu ambiri kuphatikizapo mafumu, azisirira komanso kulemekeza kwambiri Mboni za Yehova. Mwachitsanzo, tamvani zimene anthu ena ananena:

✔ “Kumangidwa kwa malo atsopano opempherera amenewa, komanso chikondi ndi mgwirizano umene a Mboni za Yehova amasonyeza n’zosiririka kwambiri ndipo matchalitchi ena ayenera kutengera chitsanzo chimenechi.”—Inatero mfumu ina ya m’dera la Chabwenzi.

✔ “Chinthu chapadera kwambiri chomwe ndimasirira kwa Mboni za Yehova ndi mgwirizano wawo. Ifeyo kutchalitchi kwathu tinayamba kalekale kumanga tchalitchi zaka 10 zapitazo, koma mpaka pano tidakalimbana nayobe kumanga. Sizikudziwika ngati idzathe n’komwe. Ndikufuna kukuthokozani kwambiri chifukwa chomanga nyumba yokongola imeneyi m’dera lathu lino.”—Anatero a nyakwawa a Chigwenembe.

✔ “Anthu inu mumagwira ntchito mochititsa chidwi kwambiri chifukwa mumagwira ntchito mofulumira, koma sikuti mumangochita zinthu mwamgwazo. Muyenera kuti ndinu anthu ogwirizana kwambiri.”—Inatero mfumu Chiuzira.

Ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi yodziwika kwambiri ngakhale kwa anthu amene analemba buku lotanthauzira mawu la Chichewa/Chinyanja—English Dictionary. Mwachitsanzo ponena za Mboni za Yehova, bukuli linanena kuti: “Mboni za Yehova zamanga matchalitchi ambiri [kutanthauza Nyumba za Ufumu].”

“Tikungoona Ngati Kutulo”

Pa January 30, 2011, anthu a mumpingo wa Manyowe ku Blantyre anatsegulira Nyumba ya Ufumu yatsopano yomwe ndi ya nambala 1,000 kumangidwa ku Malawi. Munthu wina wa mumpingowu anati: “Sitinkadziwa kuti tingakhale ndi Nyumba ya Ufumu ngati imeneyi. Tikungoona ngati kutulo ndithu.”

Mtsikana wina wa mumpingowu anati: “Pa nthawi imene Nyumba ya Ufumu imeneyi inkamangidwa ndinkabwera tsiku lililonse kudzagwira nawo ntchito. Ndimasangalala kuti ndinali ndi mwayi wogwira nawo ntchito yomanga malo abwino olambiriramo m’dera lathu.”

Mmodzi wa akulu mumpingowu anati: “Poyamba akuluakulu a mumzindawu ankakana kutipatsa chilolezo chomanga Nyumba ya Ufumu. Kangapo konse iwo anakana kusaina makalata otiloleza. Koma mfumu ya m’dera lathu, mayi Liness Chikaoneka, anayesetsa mwakhama kupempha akuluakuluwo kuti atisainire.”

Tsiku lina mayi Chikaoneka anaperekeza mmodzi wa akulu a mpingo wa Manyowe kuti akasainitse mapepalawo. Mayiwa anauza akuluakulu abomawo kuti: “Ndikufuna kuti a Mboni za Yehova amange Nyumba ya Ufumu m’mudzi mwanga. Anthu a Mboni ndi anthu abwino komanso amatsatira malamulo moti palibe amene anabwerapo kwa ine kudzadandaula za anthu amenewa.” Pamapeto pake mmodzi wa akuluakulu abomawo anasaina mapepalawo.

Pa nthawi yotsegulira Nyumba ya Ufumu imeneyi, mayi Chikaoneka anasangalala kwambiri. Iwo anati: “Ndasangalala ndipo ndikunyadira kwambiri kukhala ndi nyumba yokongola imeneyi m’mudzi mwanga muno.”

M’dziko lonse la Malawi, Mboni za Yehova komanso anthu ena akupitirizabe kuyamikira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Chifukwa cha khama lawo komanso mtima wawo wodzipereka, a Mboni za Yehova m’Malawi achepetsa kwambiri vuto losowa Nyumba za Ufumu, poyerekeza ndi mmene zinalili mu 1993. N’zoona kuti m’dzikoli mukufunikabe Nyumba za Ufumu zina chifukwa anthu akupitirizabe kumvetsera ‘uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu’ ndipo mipingo ikuwonjezerekabe. (Mateyu 24:14) Choncho, a Mboni za Yehova m’dzikoli amathokoza a Mboni anzawo padziko lonse chifukwa cha thandizo lawo komanso ndalama zimene amapereka kuti ntchitoyi itheke. *

Koma koposa zonse, a Mboni za Yehova ku Malawi amayamikira kwambiri Mulungu wawo Yehova. Zimene a Mboniwa amanena poyamikira zimafanana ndi zimene munthu wina amene analemba nawo masalimo ananena. Iye anati: “Mitundu yonse imene munapanga idzabwera kwa inu, ndipo idzagwada pamaso panu, inu Yehova, ndi kulemekeza dzina lanu. Pakuti inu ndinu wamkulu ndipo mukuchita zinthu zodabwitsa.”—Salimo 86:9, 10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Panopa chiwerengero cha Nyumba za Ufumu chapitirira 1,030.

^ ndime 9 Kuyambira m’chaka cha 1999, Mboni za Yehova padziko lonse zamanga Nyumba za Ufumu zokwana 23,786 m’mayiko osauka okwana 151.

^ ndime 28 Padziko lonse, ntchito ya Mboni za Yehova imayendetsedwa ndi ndalama zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo.

[Chithunzi patsamba 24]

Ntchito yomanga Nyumba za Ufumu isanayambe, misonkhano inkachitikira m’malo ngati awa

[Chithunzi patsamba 24]

Masiku ano mipingo yambiri imasonkhana mu Nyumba za Ufumu ngati iyi