Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

 Zoti Banja Likambirane

Kodi Chithunzichi Chalakwika Pati?

Werengani Yohane 2:13-17. Tchulani zinthu zinayi zimene zalakwika pachithunzichi. Lembani mayankho anu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo malizitsani kujambula zithunzizi pozikongoletsa ndi chekeni.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

4. ․․․․․

KAMBIRANANI:

N’chifukwa chiyani Yesu anathamangitsa anthu amenewa m’kachisi?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Maliko 11:17.

N’chifukwa chiyani anthuwa samayenera kuchita malonda m’kachisi?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Akorinto 2:17.

Kuti tisangalatse Yehova, kodi tiyenera kupewa kumutumikira ndi maganizo otani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Mateyu 22:36-40; 1 Petulo 5:2.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Pezani kapepala ndipo ana anu alembepo kapena kujambulapo chinthu chinachake chimene angachite, chosonyeza kuti amakonda Yehova komanso anthu ndi mtima wonse. Kenako anawo aonetse anthu a m’banjamo kapepalako ndipo kambiranani nthawi imene mungachitire chinthucho limodzi.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 16 TIMOTEYO

MAFUNSO

A. Lembani mawu amene akusowekapo. Mayi ake a Timoteyo, a ․․․․․, komanso agogo ake aakazi, a ․․․․․ anamuphunzitsa “malemba oyera” kuyambira ali ․․․․․.

B. Kodi Timoteyo ali wachinyamata anavomera kuchita chiyani?

C. Ponena za Timoteyo, Paulo anati: “Monga mwana ndi bambo ake . . . ”

[Tchati]

4026 B.C.E. Kulengedwa kwa Adamu

Anakhala ndi moyo m’zaka zapakati pa 1 C.E. ndi 100 C.E.

1 C.E.

98 C.E. Baibulo linamalizidwa kulembedwa

[Mapu]

Ankakhala ku Lusitara koma abale a ku Ikoniyo ankadziwa za khalidwe lake labwino

Lusitara

Ikoniyo

Yerusalemu

TIMOTEYO

ANALI NDANI?

Ngakhale kuti bambo ake anali wosakhulupirira, iye ‘anakhala chitsanzo kwa okhulupirika m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, ndi pa khalidwe loyera.’ (1 Timoteyo 4:12) Anagwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo akuti: “Ukhale ndi chizolowezi chochita zinthu zokuthandiza kuti ukhalebe wodzipereka kwa Mulungu.” (1 Timoteyo 4:7) Timoteyo anathandiza mtumwi Paulo pa utumiki wake kwa zaka pafupifupi 15.

MAYANKHO

A. Yunike, Loisi, mwana.—2 Timoteyo 1:5; 3:14, 15.

B. Kuyenda komanso kutumikira limodzi ndi Paulo.—Machitidwe 16:1-5.

C.“. .  watumikira monga kapolo limodzi ndi ine kupititsa patsogolo uthenga wabwino.”—Afilipi 2:22.

Anthu ndi Mayiko

5. Mayina athu ndi Gabriela ndi Raul ndipo tili ndi zaka 6 ndi 9. Timakhala ku Brazil. Kodi mukudziwa kuti ku Brazil kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 467,000; 607,000 kapena 720,000?

6. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ifeyo timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Brazil.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Nkhani zina zakuti “Zoti Banja Likambirane” mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba  25

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 Ndi 31

1. Yesu anagwiritsa ntchito chikwapu osati lupanga.

2. Anthu ankagulitsa ng’ombe ndi nkhosa osati nkhumba.

3. Anthu ankagulitsa nkhunda osati akadzidzi.

4. Anthu osinthitsa ndalama anali ndi ndalama zachitsulo osati zamapepala.

5. 720,000.

6. C.