Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupsa Mtima Kumabweretsa Mavuto

Kupsa Mtima Kumabweretsa Mavuto

Kupsa Mtima Kumabweretsa Mavuto

Munthu wina yemwe anaitanitsa chakudya palesitilanti ina anakwiya kwambiri chifukwa choona kuti chakudyacho chikuchedwa. Iye analowa m’lesitilantimo n’kuopseza munthu wogwira ntchito m’menemo. Anamukwenya n’kumukankhira kukauntala ndipo anam’menya khofi. Kenako munthu wolusayo anangonyamula chakudya chake n’kutuluka.

ALIYENSE amapsa mtima nthawi zina. Ndipotu kupsa mtima kuli m’gulu la zinthu zimene anthufe timachita mwachibadwa monga kukonda ena, kuda nkhawa, kumva chisoni komanso kuchita mantha. Nthawi zina kupsa mtima kumathandiza. Mwachitsanzo, kupsa mtima kungachititse kuti munthu achite zinazake molimba mtima kuti athane ndi mavuto.

Koma monga mmene taonera kumayambiriro kwa nkhaniyi, kupsa mtima kuli ndi kuipa kwake. Mwachitsanzo, anthu amene sachedwa kupsa mtima akaputidwa amalankhula mokalipa, mwinanso kumenya munthu kumene. Mkwiyo umalamulira zochita zawo m’malo moti iwo aziulamulira. Kupsa mtima mosadziletsa n’koopsa chifukwa kumabweretsa mavuto. *

Anthu amene sachedwa kupsa mtima amakumana ndi mavuto pamoyo wawo omwenso amakhudza anthu ena. Anthu oterewa amapsa mtima kwambiri ngakhale pa zinthu zazing’ono ndipo akhoza kuchita zinthu zoopsa kwambiri. Taganizirani zitsanzo zotsatirazi:

Munthu wina amene ankayenda mumsewu ndi anzake anawomberedwa pakhosi chifukwa chakuti chikwama cha mnzake wina chinagunda mwangozi munthu wina amenenso ankayenda mumsewumo.

Mnyamata wina wazaka 19 anamenya mpaka kupha mwana wa miyezi 11 wa chibwenzi chake. Mnyamatayu ankachita masewera enaake achiwawa a pakompyuta ndipo anapsa mtima chifukwa chakuti mwanayo anamudodometsa, zimene zinachititsa kuti alephere masewerawo.

Zinthu ngati zimenezi zikuchitika padziko lonse lapansi ndipo chiwerengero cha anthu amene ali ndi vuto lopsa mtima chikuwonjezereka. Komano n’chifukwa chiyani anthu ambiri ali ndi vuto lopsa mtima masiku ano?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Kabuku kena konena za kupsa mtima kamafotokoza kuti munthu amene amapsa mtima mosadziletsa amakumana ndi mavuto ambiri pamoyo wake ndipo zimenezi zimachititsa kuti azilephera kuganiza bwino, azingokhala wokhumudwa komanso asamakhale mwamtendere ndi anthu ena.—Boiling Point—Problem Anger and What We Can Do About It.

[Bokosi patsamba 3]

Kupsa mtima kuli m’gulu la zinthu zimene anthufe timasonyeza mwachibadwa. Nthawi zina kupsa mtima kungakhale koyenera. Koma nkhani zino zikufotokoza kupsa mtima kosayenera komwe kungatibweretsere mavuto ifeyo komanso anthu ena.