Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Muthandize Odwala Matenda Oda Nkhawa?

Kodi Mungatani Kuti Muthandize Odwala Matenda Oda Nkhawa?

 Kodi Mungatani Kuti Muthandize Odwala Matenda Oda Nkhawa?

“Nthawi zina mtima wanga umagunda kwambiri ndipo kenako ndimayamba kumva kuzizira. Zikatero ndimayamba kutuluka thukuta komanso ndimakanika kupuma, ndimachita mantha, kuda nkhawa ndiponso ndimasokonezeka maganizo.”—Anatero Isabella, wazaka zam’ma 40, yemwe ali ndi matenda oda nkhawa.

MUNTHU yemwe ali ndi matenda oda nkhawa amachita mantha ndi zinthu zimene zachitika kapena zimene akuganiza kuti zichitika. N’kutheka kuti inuyo munachitapo mantha chifukwa cha galu wolusa amene ankafuna kukulumani. Komabe, manthawo ayenera kuti anatha galuyo atakusiyani. Koma munthu amene akudwala matenda oda nkhawa amakhala ndi mantha osiyana kwambiri ndi amenewa.

Munthu amene ali ndi matenda oda nkhawa amangokhalira kuda nkhawa ngakhale palibe chifukwa chilichonse chodera nkhawa. Malinga ndi zimene bungwe lina la za umoyo ku America linanena, “chaka chilichonse . . . anthu okwana 40 miliyoni a ku America, azaka zoyambira 18 kupita m’tsogolo, amadwala matenda oda nkhawa.” (National Institute of Mental Health) Matenda oda nkhawa ngati amene Isabella uja akudwala amayambitsa mavuto ambiri.

Komanso abale ake a munthu wodwalayo amavutika kwambiri. Koma nkhani yosangalatsa ndi yakuti mankhwala a matendawa alipo. Magazini ina imene inatulutsidwa ndi bungwe talitchula lija inanena kuti: “Masiku ano chithandizo cha matenda oda nkhawa chilipo ndipo akatswiri asayansi akutulukira njira zinanso zothandizira anthu odwala matendawa kuti azikhala osangalala.”

 Abale ake a wodwalayo komanso anzake angamuthandize. Komano kodi mungamuthandize bwanji?

Mmene Mungawathandizire

Muziwamvetsa: Monica yemwe amadwala matenda oda nkhawa ndiponso amachita mantha kwambiri, anafotokoza za mavuto amene amakumana nawo. Iye ananena kuti: “Ndimaona kuti anthu ambiri samvetsa mmene ndimamvera.”

Chifukwa cha zimenezi, anthu odwala matendawa amaopa kuuza ena za mavuto awo chifukwa amaganiza kuti ngakhale awauze sawamvera. Zimenezi zimachititsanso kuti azingodziimba mlandu komanso kuti azingokhalira kuda nkhawa. Choncho ndi bwino kuti anzake komanso abale ake a wodwalayo azimumvetsa.

Fufuzani kuti mudziwe zambiri za matendawa: Mfundo iyi ndi yothandiza kwambiri makamaka kwa anthu amene akusamalira anthu odwala matendawa monga achibale kapena anzake.

Muziwalimbikitsa: Mtumwi Paulo, yemwe anali m’mishonale, analimbikitsa akhristu anzake a mumzinda wa Tesalonika ku Girisi kuti: “Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukuchitira.” (1 Atesalonika 5:11) Kuti tilimbikitse anthu ena, tiyenera kusamala kwambiri ndi zimene timalankhula komanso mmene timazilankhulira. Tiyenera kuchita zinthu zosonyeza kuti timakondadi wodwalayo ndipo tizipewa kunena zinthu zimene zingamukhumudwitse.

Mwachitsanzo, ganizirani za anthu atatu omwe ankanena kuti ndi anzake a Yobu. Mwina mungakumbukire kuti anthu amenewa ankanena kuti Yobu akukumana ndi mavuto chifukwa chobisa machimo enaake.

Choncho, muzisamala ndi zimene mumalankhula kwa munthu amene akudwala matenda oda nkhawa. Muzimumvetsera akamalankhula. Muziganizira muli inuyo. Akamalankhula musamathamangire kumuganizira zinthu zolakwika. Anzake a Yobu anachita zimenezi ndipo zotsatira zake zinali zakuti anakhala ‘otonthoza otopetsa.’ M’malo momuthandiza anangomuwonjezera nkhawa.—Yobu 16:2.

Nthawi zonse muzimvetsera mwatcheru wodwala akamalankhula. Muzimusiya kuti anene momasuka zimene zili kukhosi kwake. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzimvetsa mmene akumvera, komanso zingathandize wodwalayo kuti azikhala mosangalala.

 [Bokosi/Chithunzi patsamba 27]

Mitundu ya Matenda Oda Nkhawa

Kudziwa mitundu ya matenda oda nkhawa n’kofunika kwambiri makamaka ngati tili ndi wachibale kapena mnzathu amene akudwala matendawa. Tiyeni tikambirane mitundu isanu ya ya matendawa.

Kuchita Mantha Kumbukirani Isabella amene tamutchula kumayambiriro kwa nkhani ino. Sikuti iye amangovutika ndi matenda okhawo. Iye anati: “Ndikadwala matendawa ndimachita mantha kuti ndidwalanso nthawi ina.” Chifukwa cha zimenezi anthu odwala matendawa amachita mantha kupita pamalo amene anakhala nthawi ina imene ankadwala matendawa. Ena amangokhala panyumba osachoka, pamene ena amalola kuchoka ngati ataperekezedwa ndi winawake amene amamudalira. Isabella anafotoza kuti: “Ngakhale kungodziwa kuti ndili ndekha kumachititsa kuti ndiyambe kudwala matendawa. Ndimaona kuti ndine wotetezeka mayi anga akakhalapo.”

Kumangoda Nkhawa ndi Zinthu Zakale Munthu yemwe amaopa kwambiri tizilombo toyambitsa matenda kapena matope angamafune kuti azingosamba m’manja nthawi zonse. Munthu winanso wodwala matendawa, dzina lake Renan, anati: “Nthawi zonse ndimangokhalira kudandaula chifukwa cha zinthu zolakwika zimene ndinachita kalekale.” Munthu yemwe ali ndi vutoli angamangonena kwa aliyense zolakwa zimene anachita. Nthawi zonse Renan amafuna munthu womulimbitsa mtima kuti aiwale zakale. Koma pali mankhwala amene akhala akumuthandiza kulimbana ndi matendawa. *

Kuchita Mantha Chifukwa cha Zoopsa Zimene Zinachitika Kale Pali anthu ena amene anakumanapo ndi zinthu zoopsa monga kumenyedwa kwambiri ndipo amangokumbukirabe zimene zinachitikazo. Anthu omwe ali ndi vutoli amangodzidzimukadzidzimuka, sachedwa kukhumudwa, sasangalala, amasiya kuchita zinthu zimene ankasangalala nazo poyamba komanso zimawavuta kusonyeza chifundo anthu amene poyamba ankawakonda kwambiri. Ena amayamba kuchita zinthu mwaukali kapenanso kuchita ndewu ndipo amayesetsa kupewa zinthu zimene zingawakumbutse zoopsa zimene anakumana nazo.

Kuopa Kukhala Pagulu Anthu ena amakhala ndi nkhawa kwambiri akakhala pagulu. Anthu amene ali ndi vutoli amachita mantha kwambiri ndipo amaganiza kuti aliyense akuona kuti chilichonse chimene akuchita n’cholakwika. Iwo akakhala ndi zochitika zinazake, amakhala ndi nkhawa kwambiri mwina kwa masiku kapena milungu yambirimbiri tsiku la zochitikazo lisanafike. Manthawa amafika poipa kwambiri moti amawalepheretsa kugwira ntchito, kuphunzira kapena kuchita zinthu za tsiku ndi tsiku. Komanso anthu amene ali ndi vutoli amalephera kupeza anthu ocheza nawo.

Kumangoda Nkhawa ndi Chilichonse Monica, amene tamutchula kale uja, ali ndi vuto limeneli. Tsiku lililonse “amangokhalira kuda nkhawa” ngakhale palibe chifukwa chilichonse chodera nkhawa. Anthu amene ali ndi vutoli amangoganiza kuti akumana ndi zoopsa ndipo amada nkhawa kwambiri ndi zinthu monga thanzi lawo, ndalama, mavuto a m’banja kapena a kuntchito. Komanso amati kukangocha amachita mantha kwambiri kuti tsikulo litha bwanji. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Galamukani! sisankhira anthu mankhwala.

^ ndime 22 Mfundo zimene zili pamwambazi zachokera m’magazini imene inatulutsidwa ndi bungwe la National Institute of Mental yomwe ndi nthambi ya unduna wa za umoyo ku America.

[Chithunzi patsamba 26]

‘Muzilimbikitsana’