Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zinayi Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Malo Amenewa

Mfundo Zinayi Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Malo Amenewa

 Mfundo Zinayi Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Malo Amenewa

Monga mmene zilili ndi Intaneti yonse, malo ochezera a pa Intaneti alinso ndi kuipa kwake. * Choncho mungachite bwino kuganizira mfundo zotsatirazi.

1 Kodi Kucheza ndi Anthu pa Intaneti Kumakhudza Bwanji Zinthu Zanga Zachinsinsi?

“Pakachuluka mawu sipalephera kukhala zolakwa, koma wodziwa kulamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru.”—Miyambo 10:19.

Zimene muyenera kudziwa. Popanda kusamala, zinthu monga dzina lanu, kumene mumakhala, zithunzi zanu ndiponso mauthenga amene mumatumizira anzanu zikhoza kuchititsa kuti anthu amaganizo olakwika adziwe zinthu zambiri zachinsinsi zokhudza inuyo. Anthu akhoza kudziwa kumene mumakhala, kumene mumagwira ntchito, sukulu imene mumaphunzira komanso akhoza kudziwa ngati muli pakhomo kapena ngati mwachokapo. Mwachitsanzo, kungolemba pamalo anu ochezera a pa Intaneti kuti “Mawa tikupita ku tchuthi” kungachititse akuba kuti adziwe kuti mwachoka, n’kudzakuberani.

Komanso zinthu zina ngati adiresi yanu ya imelo, tsiku limene munabadwa kapena nambala yanu ya foni, zingachititse kuti anthu ena akuchiteni zachipongwe kapena kukuberani mosavuta. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri amalemba zinthu ngati zimenezi pamalo awo ochezera a pa Intaneti.

Anthu amaiwala kuti zimene amalemba pa Intaneti zimaonedwa ndi anthu ambiri. Ngakhale atasankha kuti zimene amalemba zizionedwa ndi anzawo okha, anzawowo akhoza kuzitumizanso kwa anthu ena. Kunena zoona, muyenera kudziwa kuti chilichonse chimene mumaika pamalo ochezera a pa Intaneti chikhoza kuonedwa kapena kutumizidwanso kwa anthu ena.

Zimene mungachite. Dziwani bwino mmene mungagwiritsire ntchito malo amenewa kuti anthu ena asamaone zimene mumalemba. Muzionetsetsa kuti amene amaona zimene mumalemba komanso zithunzi zanu ndi okhawo amene mumawakhulupirira.

Komanso dziwani kuti zimene mumalemba zimaonedwa ndi anthu ambiri kuposa amene inuyo mumafuna. Nthawi ndi nthawi muzionanso zimene mwaika pamalo anu a pa Intaneti ndipo muzidzifunsa ngati anthu ena amaganizo oipa angagwiritse ntchito zinthuzo kuti abe zinthu zanu zachinsinsi. Muzipewa kulemba zinthu zimene zingachititse kuti anzanu adziwe zinsinsi zanu zonse komanso muzipewa kuulula zinsinsi za anthu ena. (Miyambo 11:13) Ngati mukufuna kumuuza mnzanu zinthu zachinsinsi ndi bwino kugwiritsa njira ina yolankhulirana. Mtsikana wina, dzina lake Cameron, anati: “Kulankhulana pafoni kuli bwinoko chifukwa anthu ambiri sadziwa zimene mukukambirana.”

Mfundo yofunika. Mayi wina anafotokoza kuti: “Ngati utamachita zinthu mosamala ukhoza kumagwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti popanda anthu ena kudziwa zinthu zako zachinsinsi. Kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti kulibe vuto kwenikweni pokhapokha ngati ukuchita zinthu mosasamala.”

2 Kodi Kucheza ndi Anthu pa Intaneti Sikungawononge Nthawi Yanga?

“Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.

 Zimene muyenera kudziwa. Kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti kukhoza kukudyerani nthawi yanu komanso kukulepheretsani kuchita zinthu zofunika kwambiri. Mayi wina, dzina lake Kay, anati: “Ukakhala ndi anthu ambiri ocheza nawo, umawononganso nthawi yambiri ndipo nthawi zonse umangofuna uzicheza nawo.” Tamvani zimene anthu ena amene poyamba ankakonda kwambiri kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti ananena.

“Munthu ukayamba kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti umazolowera kwambiri moti zimakhala zovuta kusiya.”—Anatero Elise.

“Anthu amachita zinthu zambiri pamalo ochezera a pa Intaneti monga kusewera magemu, kuyankha mafunso, kumvera nyimbo komanso kuona zimene anzawo onse alemba.”—Anatero Blaine.

“Umati ukakhala pamalo ochezera a pa Intaneti umaiwala kuti pali zinthu zina zofunika kuchita moti umangozindikira kuti amayi abwera n’kumakufunsa chifukwa chimene sunatsukire mbale.”—Anatero Analise.

“Ndinkati ndikakhala kusukulu ndinkangofuna kuweruka mwachangu kuti ndikaone zimene anzanga andiyankha. Ndikafika kunyumba ndinkafunika ndiyankhenso aliyense amene wandilembera uthenga komanso kuona zithunzi zatsopano zimene anzanga aika. Ndikamagwiritsa ntchito Intaneti ndinkakhala wolusa moti sindinkafuna kuti wina andisokoneze. Koma pali anzanga ena omwe nthawi zonse amangokhalira kucheza ndi anthu pa Intaneti ngakhale akapita kokacheza kapena pakati pa usiku.”—Anatero Megan.

Zimene mungachite. Nthawi ndi ndalama. Mumafunika kuigwiritsa ntchito mwanzeru m’malo moiwononga mwachisawawa. Choyamba, lembani nthawi imene mukuona kuti ndi yokwanira kucheza ndi anthu pa Intaneti. Kenako pakatha mwezi, onaninso mmene mwagwiritsira ntchito nthawi yanu. Ngati pangafunike kusintha, sinthani.

Ngati ndinu kholo ndipo mwana wanu amathera nthawi yaitali akucheza pa Intaneti, fufuzani kuti mudziwe chomwe chikumuchititsa. Mwachitsanzo, Nancy E. Willard analemba m’buku lake (Cyber-Safe Kids, Cyber-Savvy Teens) kuti nthawi zambiri munthu akamathera nthawi yaitali akucheza ndi anthu pa Intaneti, amakhala kuti ali ndi nkhawa komanso amadziona kuti ndi wachabechabe. Iye anati: “Achinyamata ambiri amafuna azionedwa kuti ndi ofunika ndipo amaona kuti anthu angamawaone kuti ndi ofunika akakhala ndi anzawo ambiri komanso akamacheza nawo pafupipafupi.”

Koma simuyenera kulola kuti kugwiritsa ntchito Intaneti kapena malo alionse ochezera a pa Intaneti kuzikulepheretsani kucheza ndi abale anu. Don Tapscott analemba m’buku lake (Grown Up Digital) kuti: “Anthu amatha kumacheza ngakhale ali kutali pogwiritsa ntchito Intaneti, koma Intaneti yomweyo imathanso kulepheretsa anthu okhala nyumba imodzi kucheza.”

Mfundo yofunika. Mtsikana wina dzina lake Emily ananena kuti: “Ndikuona kuti kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti ndi njira yabwino kwambiri yochezera ndi anthu. Koma monga mmene zilili ndi china chilichonse, umafunika kudziwa malire.”

3 Kodi Kucheza ndi Anthu pa Intaneti Sikungawononge Mbiri Yanga?

“Ndi bwino kukhala ndi mbiri yabwino kusiyana ndi kukhala ndi siliva ndi golide.”—Miyambo 22:1. “Contemporary English Version.”

 Zimene muyenera kudziwa. Zimene mungalembe pamalo ochezera a pa Intaneti zingapangitse anthu kuganiza kuti muli ndi khalidwe linalake loipa ndipo zingakhale zovuta kuti anthu asiye kuganiza choncho. (Miyambo 20:11; Mateyu 7:17) Koma anthu ambiri sadziwa kwenikweni kuopsa kogwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti. Mtsikana wina, dzina lake Raquel, ananena kuti: “Zikuoneka kuti anthu akamacheza ndi anzawo pa Intaneti amalephera kuganiza bwino. Amatha kunena zinthu zimene sanganene atamacheza pamasom’pamaso. Ena sazindikira kuti akangoika zinthu zolakwika pa Intaneti ngakhale kamodzi kokha, akhoza kuwononga mbiri yawo.”

Kuwononga mbiri yanu chifukwa chogwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti kungakubweretsereni mavuto aakulu. Buku lina linanena kuti: “Anthu ambiri achotsedwapo ntchito kapena akanidwapo kulembedwa ntchito chifukwa cha zimene anaika pamalo awo ochezera a pa Intaneti.”

Zimene mungachite. Onaninso malo anu ochezera a pa Intaneti ndipo dzifunseni ngati anthu ena amaona kuti mumalembapo zoyenera. Mungadzifunse mafunso ngati awa: ‘Kodi ndingakonde kuti anthu azindiona chonchi? Ngati munthu wina ataona zithunzi zimene ndaika pamalo anga ochezera a pa Intaneti anganene kuti ndine munthu wotani? Kodi sangaganize kuti ndimakonda kukopa amuna kapena akazi? Kodi sangaganize kuti ndimangokonda zosangalala basi? Ngati ena ataganiza choncho, kodi ndingakonde kuti anthu ena, mwachitsanzo, amene akufuna kundilemba ntchito, azindiona choncho? Kodi zithunzi zimene ndimaika pa Intaneti zikugwirizanadi ndi mfundo zimene ndimayendera?’

Ngati ndinu wachinyamata, mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndingamve bwanji ngati makolo anga, aphunzitsi kapena munthu wina wachikulire ataona malo anga ochezera a pa Intaneti? Kodi sindingachite manyazi ataona zimene ndimalemba kapena zimene ndimaika?’

Mfundo yofunika. Pa nkhani ya mbiri yanu, muzikumbukira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”—Agalatiya 6:7.

4 Kodi Kucheza ndi Anthu pa Intaneti Kumachititsa Kuti Ndizicheza ndi Anthu Otani?

“Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”—Miyambo 13:20.

 Zimene muyenera kuchita. Anthu amene mumacheza nawo angachititse kuti musinthe mmene mumaganizira komanso zochita zanu. (1 Akorinto 15:33) N’chifukwa chake ndi nzeru kusankha bwino anthu ocheza nawo pa Intaneti. Anthu ena amangolola kuti munthu aliyense, ngakhale amene sakumudziwa, akhale mnzawo. Anthu ena amadzazindikira mochedwa kuti anzawo ena ali ndi makhalidwe oipa. Tamvani zimene ena ananena.

“Ngati munthu akungolola aliyense kuti akhale mnzake, akhoza kupeza nazo mavuto.”—Anatero Analise.

“Anzanga ena amalola kuti anthu ena akhale anzawo ngakhale kuti safuna kucheza nawo. Iwo amachita zimenezi chifukwa choopa kuwakhumudwitsa.”—Anatero Lianne.

“Munthu aliyense amafunika kusamala akamacheza ndi anthu pa Intaneti monganso mmene zimakhalira ukamacheza ndi anthu pamasom’pamaso.”—Anatero Alexis.

Zimene mungachite. Khazikitsani mfundo yoti muzitsatira. Mwachitsanzo, anthu ena amaonetsetsa kuti asamangocheza ndi aliyense. * Tamvani zimene ena ananena:

“Ndimalola anthu kuti akhale anzanga ngati ndikuwadziwa bwino, osati chifukwa chakuti tinaonanapo basi.”—Anatero Jean.

“Anthu amene ndimalola kuti akhale anzanga ndi okhawo amene ndikuwadziwa kuyambira kale. Sindilola anthu amene sindikuwadziwa.”—Anatero Monique.

“Ndimalola anthu okhawo amene ndikuwadziwa bwino komanso amene mfundo zimene amayendera n’zofanana ndi zanga.”—Anatero Rae.

“Munthu wina yemwe sindikumudziwa akandipempha kuti ndikhale mnzake, sindimalola. Ndimaona kuti sikulakwa chifukwa ndimayendera mfundo yakuti anzanga onse azikhala anthu amene ndikuwadziwa. Ndiponso sikuti ndimacheza ndi anthu pa Intaneti pokha.”—Anatero Marie.

“Ngati mnzanga wina watumiza zithunzi zoipa kapena walemba mawu amene ndikuona kuti ndi osayenera, ndimamuchotsa pa mndandanda wa anzanga nthawi yomweyo. Ndimaona kuti sibwino ngakhale kuona zinthu zoipa zimene iye waika chifukwa kuchita zimenezi n’kucheza ndi anthu olakwika.”—Anatero Kim.

“Pa nthawi yomwe ndinali ndi malo ochezera a pa Intaneti, ndinawakonza moti zinthu zanga zisamangoonedwa ndi aliyense. Sindinkalola kuti anzawo a azinzanga aziona zinthu zimene ndalemba kapena zithunzi zimene ndaika. Ndinkachita zimenezi chifukwa sindinkadziwa bwino ngati anzawo a azinzangawo anali anthu abwino kucheza nawo. Ndinkaona kuti si bwino kucheza ndi anthu amene sindikuwadziwa komanso amene khalidwe lawo sindikulidziwa.”—Anatero Heather.

Mfundo yofunika. Dr. Gwenn Schurgin O’Keeffe analemba m’buku lake kuti: “Mfundo yofunika kwambiri imene mungaitsatire ndi kucheza ndi anthu okhawo amene mukuwadziwa komanso amene mumacheza nawo nthawi zonse, osati pa Intaneti pokha.” *CyberSafe.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Magazini ya Galamukani! siiletsa kapena kulimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito malo ena ake ochezera a pa Intaneti. Mkhristu aliyense ayenera kuonetsetsa kuti sakuphwanya malamulo a Mulungu pamene akugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti.—1 Timoteyo 1:5, 19.

^ ndime 35 M’nkhaniyi tikunena za anzanu wamba, osati anzanu ochita nawo bizinezi.

^ ndime 42 Mukafuna kuwerenga mfundo zina zokhudza malo ochezera a pa Intaneti, onani Galamukani! ya July 2011, tsamba 24 mpaka 27, ndi ya August 2011, tsamba 10 mpaka 13.

[Bokosi patsamba 8]

MUZIKUMBUKIRA KUTSEKA

Ngati mutasiya malo anu ochezera a pa Intaneti osatseka mukamaliza, anthu ena akhoza kukuikirani kapena kukulemberani zinthu zosayenera. Loya wina dzina lake Robert Wilson, ananena kuti: “Kuchita zimenezi n’kofanana ndi kusiya chikwama chanu cha ndalama kapena foni yanu yam’manja pamalo oti anthu akhoza kuba mosavuta. Munthu aliyense akhoza kulembapo chilichonse chimene akufuna pamalo anu ochezerawo.” Choncho iye anachenjeza kuti: “Muzionetsetsa kuti mukamaliza muzitseka.”

[Bokosi patsamba 8]

MUKHOZA KUDZIITANIRA MAVUTO

Magazini ina inanena kuti anthu ambiri amene amagwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti “amachita zinthu zimene zingachititse kuti anthu ena awabere kapena aziwavutitsa. Mwachitsanzo, anthu 15 pa 100 alionse amene amagwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti analemba dera limene amakhala kapena maulendo amene akufuna kupita, 34 pa 100 alionse analemba tsiku, mwezi ndi chaka chimene anabadwa, ndipo anthu 21 pa 100 alionse omwe ali ndi ana analemba mayina ndiponso zithunzi za ana awo.”—Consumer Reports.