Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chisa cha Mavu Chimamangidwa Mwaluso

Chisa cha Mavu Chimamangidwa Mwaluso

Kodi Zinangochitika Zokha?

Chisa cha Mavu Chimamangidwa Mwaluso

● Mtundu wina wake mavu umene uli pachithunzichi umadziwika kuti ndi waluso kwambiri pomanga chisa. N’chifukwa chiyani?

Taganizirani izi: Mavu amenewa amamanga chisa chawo pogwiritsa ntchito timapepala tapadera kwambiri timene mavuwo amapanga okha. * Mavuwa akamamanga chisa, amasonkhanitsa timaulusi ting’onoting’ono tochokera kuzomera ndi tizinyenyeswa ta matabwa. Akatisonkhanitsa, amatafuna tinthu timeneti ndipo tikasakanikirana ndi malovu, timamata. Tikauma timakhala chisa chokhala ngati pepala lopyapyala koma lolimba kwambiri. Ndiponso m’malovu a mavuwa mumakhala zinthu zimene zimathandiza kuti mavuwa akamanga chisa, chizikhala choti dzuwa likhoza kulowa mosavuta moti mkati mwa chisacho mumatenthera bwino.

Mavuwa amamanga zisa zawo pogwiritsa ntchito mlomo. Chisacho chimamangidwa bwino kwambiri moti madzi sangalowe mkati. Chimakhala cholimba komanso ndi malo okwanira. Mavu amene amakhala m’madera amene mumagwa mvula yochuluka, amawonjezera malovu ambiri potafuna tizinthu topangira chisa. Zimenezi zimathandiza kuti madzi asamalowe m’chisacho. Komanso mavuwa amaonetsetsa kuti apeza malo abwino kwambiri amene angamangepo chisa chawo. Chisachi amachimanga mozondotsa pansi. Chodabwitsa n’chakuti mavu akamamanga chisa chawo chokhala ngati pepalachi sawononga chilengedwe pomwe anthu popanga mapepala amawononga madzi, mpweya komanso nthaka.

N’chifukwa chake akatswiri a zomangamanga komanso ofufuza zinthu akuphunzira zambiri zokhudza chisa cha mavu n’cholinga choti adzapange zinthu zomangira nyumba zopepuka, zolimba, zoti zingapindidwe mosavuta komanso zosawononga chilengedwe.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti kachilombo kakang’ono ngati kameneka, komwe ubongo wake ndi waung’ono kwambiri ngati kamchenga, kazitha kumanga chisa mwaluso chonchi? Kodi zimenezi si umboni wakuti alipo amene anakalenga?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mitundu yambiri ya mavu imamanga zisa zoterezi. Mkati mwa chisacho mumakhala timabowo tomwe mavuwo amaikiramo mazira.