Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mbiri ya Mtengo wa Khirisimasi

Mbiri ya Mtengo wa Khirisimasi

 Mbiri ya Mtengo wa Khirisimasi

M’MAYIKO ambiri, anthu amagwiritsa ntchito mtengo wa Khirisimasi pa zikondwerero zosiyanasiyana moti panthawi imeneyi mitengoyi imayenda malonda kwambiri. Mbiri ya mtengowu ndi yakale kwambiri.

Mwachitsanzo, m’chigawo cha Bohuslän kumadzulo kwa dziko la Sweden, komanso m’chigawo cha Østfold m’dziko la Norway, kuli zithunzi zakale kwambiri zosonyeza mitengo imeneyi zimene zinagobedwa pamiyala. M’zigawo zimenezi, mwapezeka zithunzi zoposa 75,000 m’malo okwana pafupifupi 5,000. Akatswiri ofukula zinthu zakale akuti zithunzi zimenezi zinajambulidwa pakati pa chaka cha 1,800 ndi 500 B.C.E. *

Zithunzi zochititsa chidwi zimenezi, zomwe akuti zinajambulidwa kale kwambiri Yesu asanabadwe, zimatithandiza kudziwa zikhulupiriro za anthu a m’nthawi imeneyo. Mwachitsanzo, ofufuza ena amaganiza kuti kalelo, m’mayiko amene panopa ndi Sweden ndi Norway, mitengo imeneyi inkaonedwa kuti ndi yopatulika.

N’chifukwa chiyani anthu a kumpoto kwa dziko lapansi ankagoba zithunzi za mitengo imeneyi pamiyala? Akatswiri ena amaganiza kuti iwo ankachita zimenezi mwina chifukwa chakuti pa nthawiyo mitengo imeneyi inali yosowa komanso inkaonedwa kuti ndi yapadera kwambiri. Kwa anthuwo, ziyenera kuti zinali zodabwitsa kuona mitengoyi isakuyoyoka masamba chaka chonse.

M’zikhalidwe zambiri mitengo imeneyi yakhala ikugwiritsidwa ntchito kuimira moyo wautali, kupirira komanso kusafa kwa mzimu. Mfundo imeneyi ingatithandizenso kumvetsa chifukwa chake anthu kalekalelo ankajambula zithunzi zambirimbiri za mitengo ku Bohuslän ndi Østfold pa nthawi yomwe m’maderawa munalibe mitengo yambiri.

Buku lina lomwe linalembedwa ndi bungwe lina la ku Sweden (Swedish National Heritage), linati: “Zithunzi za mitengo zojambulidwa m’miyalazi ndi umboni wakuti chigawo chakum’mwera kwa dziko la Scandinavia chinkachita nawo miyambo ya chipembedzo, ndi zinthu zina zachikhalidwe zimene zinkachitika m’madera onse a ku Ulaya ndi zigawo zina za ku Asia. Anthu a m’madera amenewa, omwe anali alimi a mbewu zosiyanasiyana ndi ziweto, anayamba kupemphera komanso kuphunzira zinthu zokhudza chilengedwe. Anthuwa ankalambira milungu yofanana ngakhale kuti mayina a milunguyo ankasiyanasiyana.”—Rock Carvings in the Borderlands.

Buku linanso limene linafalitsidwa ndi bungwe lina la ku Bohusläns, linanena kuti: “Cholinga cha anthu amene anajambula zithunzi za mitengo pamiyalapo, sichinali kusonyeza mmene moyo wa anthu unalili nthawiyo ndi zochitika za tsiku ndi tsiku. Tikukhulupirira kuti cholinga chawo chinali kusonyeza mmene anthu ankachitira popemphera  kwa milungu yawo.” Bukuli linanenanso kuti: “Zithunzi zimenezi zimasonyeza kuti anthu a m’maderawa ankakhulupirira kuti munthu akafa amakabadwanso kwinakwake, komanso ankakhulupirira zinthu zina zokhudza kubereka ndi imfa.”

Pofotokoza za zithunzi zina zochititsa chidwi, zomwe zinajambulidwa anthu a kumpoto kwa Ulaya asanayambe n’komwe kudziwa kulemba, buku lina linati: “Kupezeka kwa zithunzi zambiri zosonyeza nkhani zokhudza kugonana ndi umboni wosonyeza mmene anthu a kumpoto kwa dziko lapansili ankaonera miyambo yokhudza kubereka.”—Nationalencyklopedin.

Zikuoneka kuti miyambo yokhudza mitengo yosayoyoka masamba m’nyengo ya dzuwa inafala kwambiri moti patapita nthawi siinalinso yachilendo m’madera ambiri. Buku lina (Encyclopædia Britannica) linanena kuti: “Anthu ambiri omwe sanali Akhristu ku Ulaya ankakonda kulambira mitengo, ndipo anapitiriza kuchita zimenezi ngakhale pamene analowa Chikhristu.” Ankachita zimenezi pa miyambo yosiyanasiyana. Mwachitsanzo, “ankaika mtengo wa Khirisimasi pakhomo kapena m’nyumba m’nthawi ya zikondwerero zosiyanasiyana.”

Anthu ambiri anayamba kugwiritsa ntchito mtengo wa Khirisimasi m’chaka cha 1841, pamene banja lachifumu ku Britain linakongoletsa nyumba yawo ndi mtengowu pa chikondwerero cha Khirisimasi. Masiku ano, mtengo umene umagwiritsidwa ntchito pa Khirisimasi padziko lonse lapansi ndi wodziwika bwino, ndipo umayenda malonda kwambiri pa nyengo ya Khirisimasi. Komabe, zithunzi zimene anagoba pamiyala ku Scandinavia zija, ndi umboni wakuti mtengowu unayamba kugwiritsidwa ntchito ndi anthu achikunja.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Zithunzi zina zimene zinapezeka m’miyala ku Bohuslän zinaikidwa m’gulu la zinthu zochititsa chidwi kwambiri padziko lonse ndi bungwe la UNESCO.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Zithunzi zogobedwa pamiyala zimasonyeza kuti anthu anayamba kulambira mtengo wa Khirisimasi Khristu asanabadwe

[Zithunzi patsamba 13]

Zojambula zochita kugoba pamiyala za ku (1) Torsbo, (2) Backa, ndi (3) Lökeberg, ku Sweden

[Mawu a Chithunzi]

Courtesy Stiftelsen för dokumentation av Bohusläns hällristningar