Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amasamalira Nyama?

Kodi Mulungu Amasamalira Nyama?

 Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mulungu Amasamalira Nyama?

MOYO wa nyama zambiri uli pa ngozi. Asayansi ambiri akuti mitundu ya nyama zina ikutha mofulumira kwambiri. Komanso nyama zambiri zikusowa pokhala chifukwa anthu akuwononga nkhalango. Vutoli lafika poipa kwambiri chifukwa chakuti anthu akuchitira nkhanza ziweto komanso pali makampani ambiri opha nyama n’kumagulitsa.

Komabe anthu ena amaona kuti mavuto amenewa ndi osapeweka. Koma kodi zimenezi n’zimene Mulungu anafuna kuchokera pachiyambi? Kodi Mulungu amakhudzidwa anthu akamazunza nyama? Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Mulungu amasamalira nyama?

Mulungu Wakhala Akusamalira Nyama Kuyambira Pachiyambi

Mulungu anasangalala atamaliza kulenga nsomba, mbalame, ndi nyama. Baibulo limanena kuti iye “anaona kuti zili bwino.” (Genesis 1:21, 25) Nyama zonse, zazikulu ndi zazing’ono zomwe, zinkakondedwa ndi Mlengi. Mulungu anazilenga ndi ‘nzeru zachibadwa’ n’kuzipatsa malo abwino kwambiri okhala. Wolemba Baibulo wina anafotokoza bwino zimenezi, kuti: “Zonsezi zimayembekezera inu kuti muzipatse chakudya pa nyengo yake. Zimalandira zimene mwazipatsa. Mumatambasula dzanja lanu ndipo zimakhutira ndi zinthu zabwino.”—Miyambo 30:24; Salimo 104:24, 25, 27, 28.

N’zoona kuti Mulungu anafuna kuti Adamu azilamulira nyama. Mulungu sanapatse nyama nzeru zotha kuganiza kapena kuchita zinthu zauzimu ngati anthu. (2 Petulo 2:12; Yuda 19) Mosiyana ndi zimenezi, Adamu analengedwa mwapamwamba kwambiri, chifukwa analengedwa “m’chifanizo cha Mulungu.” Choncho, iye ankatha kusonyeza makhalidwe a Mlengi wake, Yehova. (Genesis 1:27; Salimo 83:18) Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti anthu ali ndi ulamuliro wochitira nyama chilichonse chimene akufuna.

Mwachitsanzo, Adamu anapatsa nyama zosiyanasiyana mayina chifukwa chakuti Mulungu anamupatsa mwayi wochita zimenezi. Ndipotu Yehova anamuthandiza Adamu chifukwa “anayamba kuzibweretsa kwa munthuyo, kuti [chamoyo] chilichonse achitche dzina.” (Genesis 2:19) Choncho, kuti Adamu akwanitse kusamalira nyamazo anafunika kutsatira malangizo a Mlengi.

Mulungu Safuna Kuti Nyama Zizizunzidwa

N’zomvetsa chisoni kuti Adamu anapandukira Mlengi wake ndipo zimenezi zinachititsa kuti moyo padziko lapansi usokonekere kwambiri. Komabe, Mlengi anafotokoza momveka bwino mmene anthu ayenera kuchitira ndi nyama. Ngakhale kuti anthu analoledwa kuti azidya nyama ndi kuzigwiritsa ntchito pa zinthu zina, Mulungu sanaloleze kuti anthu azichitira nkhanza nyama. Baibulo limati: “Wolungama amasamalira moyo wa chiweto chake, koma chisamaliro cha anthu oipa n’chankhanza.”—Miyambo 12:10.

Mulungu anapatsa mtundu wa Isiraeli malamulo a mmene angasamalire nyama. Mwachitsanzo, pa tsiku la Sabata, nyama zinkakhalanso ndi mwayi wopuma. (Ekisodo 23:12) Ngakhale kuti anthu sankaloledwa kugwira ntchito pa tsiku lopatulika limeneli, n’zochititsa chidwi kuti ankaloledwa kupulumutsa nyama ngati yakumana ndi vuto linalake. (Luka 14:5) Mulungu analamulanso kuti ng’ombe ziziloledwa kudya pamene zikugwira ntchito, komanso kuti nyama zisamagwiritsidwe ntchito mopitirira malire. (Ekisodo 23:5; Deuteronomo  25:4) Mulungu analamulanso kuti ng’ombe ndi bulu asamazimangirire pa goli limodzi. (Deuteronomo 22:10) Choncho, n’zoonekeratu kuti Mulungu amafuna kuti nyama zizikondedwa ndi kusamalidwa.

Ngakhale kuti anthu ambiri amachitira nkhanza nyama, Mulungu amazichitira chisoni. Mneneri Yona atalephera kuchitira chifundo anthu a ku Nineve, amene Mulungu sanafune kuwawononga chifukwa chakuti analapa, Yehova anati: “Kodi ine sindikuyenera kumvera chisoni mzinda waukulu wa Nineve, mmene muli anthu oposa 120,000, omwe sadziwa kusiyanitsa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere? Kodi sindiyenera kumveranso chisoni ziweto zambiri zimene zili mmenemo?” (Yona 4:11) Nkhani imeneyi ikusonyeza kuti Mlengi wathu amamvera chisoni nyama.

M’tsogolomu Nyama Zidzakhala Pamtendere

Mulungu sasangalala akaona nyama zikuzunzidwa. Mwana wake wokondedwa, Yesu, ananena kuti ngakhale mpheta imodzi ikagwa pansi, Yehova amadziwa. (Mateyu 10:29) Mosiyana ndi Yehova, anthu sadziwa bwinobwino mmene zochita zawo zingakhudzire nyama. Choncho kuti anthu azisamalira bwino nyama, ayenera kuphunzitsidwa ndiponso kusintha kaganizidwe kawo.

N’zosangalatsa kuti Baibulo limanena kuti kutsogoloku Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira, “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.” (Yesaya 11:9) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu adzaphunzitsidwa bwino kwambiri za mmene angasamalire chilengedwe. Ndipo Mulungu adzaonetsetsa kuti nyama ndi anthu akukhala mwamtendere mogwirizana ndi zimene iye ankafuna pachiyambi.

Baibulo limafotokoza mmene dziko lidzasinthire. Limanena kuti: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa wamphongo kwa kanthawi, ndipo kambuku adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi. Mwana wa ng’ombe, mkango wamphamvu ndi nyama yodyetsedwa bwino zidzakhala pamodzi, ndipo kamnyamata kakang’ono kadzakhala mtsogoleri wawo. Ng’ombe ndi chimbalangondo zidzadyera pamodzi. Ana awo adzagona pansi pamodzi. Ngakhale mkango udzadya udzu ngati ng’ombe yamphongo. Mwana woyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndipo mwana woleka kuyamwa adzapisa dzanja lake kudzenje la njoka yapoizoni.” Kunena zoona, tikuyembekezera zinthu zabwino kwambiri kutsogoloku.—Yesaya 11:6-8.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi Mulungu amamva bwanji anthu akamazunza nyama?—Miyambo 12:10; Mateyu 10:29.

● Kodi zidzatheka kuti nyama ndi anthu azikhala pamodzi mwamtendere?—Yesaya 11:6-9.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Kuti anthu azisamalira bwino nyama, ayenera kuphunzitsidwa ndiponso kusintha kaganizidwe kawo

[Mawu a Chithunzi patsamba 11]

La Voz de Galicia/Fotógrafo: Víctor Mejuto