Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku Lapadera Limene Lapulumuka Mavuto Ambiri

Buku Lapadera Limene Lapulumuka Mavuto Ambiri

 Buku Lapadera Limene Lapulumuka Mavuto Ambiri

“Palibe buku linanso limene lakumana ndi mavuto ambiri kuposa Baibulo. Anthu ayesetsa kugwiritsa ntchito mphamvu, nzeru, komanso luso lawo polankhula kuti Baibulo lisamapezekenso, koma alephera.”

KODI n’chifukwa chiyani muyenera kuchita chidwi ndi Baibulo? Chifukwa choyamba n’chakuti Baibulo limati uthenga wake unalembedwa ndi Mulungu kuti uthandize anthu. (2 Timoteyo 3:16) Ngati zimenezi zili zoona, ndiye kuti muyenera kuliwerenga kuti mudziwe uthenga wofunika umene uli m’Baibulo.

Chifukwa china chimene tiyenera kuwerengera Baibulo n’chakuti, ndi buku lakale kwambiri lomwe lamasuliridwa ndi kufalitsidwa m’zinenero zambiri kuposa buku lililonse. Baibulo ndi buku limene lakhala likuyenda malonda kwambiri kuyambira kalekale ndipo mpaka pano, Mabaibulo ambiri amagulitsidwa chaka chilichonse kuposa buku lina lililonse.

Chochititsa chidwi kwambiri n’chakuti Baibulo lilipobe mpaka pano ngakhale kuti anthu ena akhala akulimbana nalo kwambiri kuyambira kalekale. Katswiri wina wa maphunziro a zaumulungu wa zaka za m’ma 1800, dzina lake Albert Barnes, anati: “Palibe buku linanso limene lakumana ndi mavuto ambiri kuposa Baibulo. Anthu ayesetsa kugwiritsa ntchito mphamvu, nzeru, komanso luso lawo polankhula kuti Baibulo lisamapezekenso, koma alephera.”

Barnes ananenanso kuti anthu amachita chidwi ndi chinthu chilichonse chimene chapulumuka zokhoma zambiri. Iye anati: “Palibe gulu la asilikali limene lalimbana ndi adani ambiri kuposa Baibulo. Baibulo lili ngati khoma limene lakhala likuwomberedwa ndi asilikali kwa zaka zambiri koma osagwa. Lili ngatinso mwala umene wakhala ukumenyedwa ndi madzi amphamvu kwa nthawi yaitali koma osasuntha.”

Mabuku ambiri akale anatayika, kuwonongedwa, kapena kungoiwalika. Koma Baibulo lapulumuka zokhoma zambiri. Anthu ambiri alimenyera nkhondo kuti lizipezeka ndi anthu wamba, mpaka kufika poika moyo wawo pachiswe. Koma anthu enanso ambiri akhala akulanda anthu Mabaibulo n’kumawawotcha komanso kuwotcha anthu opezeka nalo.

Kodi n’chifukwa chiyani anthu ena amalikonda kwambiri Baibulo, pamene enanso amadana nalo kwambiri? Kodi kwenikweni Baibulo lapulumuka zokhoma zotani? Kodi ndi anthu ati amene ayesetsa kulimbana nalo kuti lisamapezeke? N’chiyani chachititsa kuti bukuli lipulumuke zonsezi? Ndipo kodi uthenga wake ndi wofunika bwanji kwa inuyo? Mafunso amenewa ayankhidwa m’nkhani zotsatira.

[Tchati/Zithunzi pamasamba 2, 3]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MBIRI YA BAIBULO

 1513 B.C.E. Kulembedwa kwa Baibulo m’chinenero cha

mpaka 98 C.E. Chiheberi, Chialamu, ndi Chigiriki

100 Linayamba kulembedwa pamipukutu yokhala ngati mabuku

405 Jerome analimasulira m’Chilatini

1380 Wycliffe analimasulira kuchoka m’Chilatini

kupititsa m’Chingelezi

1455 Gutenberg anayamba kusindikiza Baibulo pogwiritsa

ntchito makina

1525 Tyndale analimasulira m’Chingelezi

1938 Linasindikizidwa m’zinenero zoposa 1,000

2011 Likupezeka m’zinenero zoposa 2,500