Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zojambula Zosangalatsa za Tingatinga

Zojambula Zosangalatsa za Tingatinga

 Zojambula Zosangalatsa za Tingatinga

“ZOJAMBULA za Tingatinga zimakumbutsa anthu za zithunzi zimene ankajambula ali ana. N’zoseketsa, zosangalatsa komanso zokongola kwambiri.” Mawu amenewa ananenedwa ndi Daniel Augusta, yemwe ndi mkulu wa bungwe la anthu ojambula zithunzi za Tingatinga. Zithunzi za Tingatinga zimasonyeza moyo, chikhalidwe komanso nyama za ku Africa, makamaka za ku Tanzania komwe lusoli linayambira.

Zithunzi za Tingatinga amazitchula ndi dzinali chifukwa amene anayambitsa kuzijambula anali Edward Said Tingatinga. Iye anabadwa m’chaka cha 1932, kum’mwera kwa dziko la Tanzania. Kuyambira ali wamng’ono, iye ankachita chidwi kwambiri ndi nyama zakutchire komanso zinthu zina zachilengedwe zopezeka kumudzi kumene ankakhala. Ali ndi zaka za m’ma 20, anachoka kumudzi kwawo n’kupita kutawuni kukafunafuna ntchito. Kenako, Edward anapita ku Dar es Salaam, likulu la dziko la Tanzania, komwe analembedwa ntchito yobzala ndi kusamalira maluwa. Madzulo akaweruka, ankakonda kuimba ndiponso kuvina. Edward anali munthu waluso pa zoimbaimba komanso zovinavina, moti anafika potchuka kwambiri.

Chaka cha 1968 chinali chosaiwalika pa moyo wake chifukwa anayamba kugwira ntchito m’boma. Ankagwira ntchito ya ulonda kuchipatala cha boma cha Muhimbili, ku Dar es Salaam. Akugwira ntchitoyi, Edward ankakhala ndi nthawi yoganizira zinthu zosiyanasiyana zimene anaona ali mwana, choncho anayamba kujambula zithunzi zosiyanasiyana zimene panopa zimadziwika ndi dzina lake. Popeza zinali zovuta kupeza mabulashi, penti ndi zinthu zina zabwino zogwirizana kwambiri ndi ntchito yake, Edward ankangogwiritsa ntchito zinthu wamba zimene zinkapezeka m’timashopu ta m’deralo. Penti imene ankagwiritsa ntchito inali yofanana ndi imene amapaka njinga ndipo zithunzi zake zinkakhala zowala kwambiri.

Zithunzi zimene Edward ankajambula sizinkakhala ndi zinthu zambiri. Iye ankangopeza chinthu choti ajambulepo chithunzi chakecho n’kuchipaka penti ya mtundu umodzi kapena mitundu iwiri. Kenako amajambulapo chithunzi  chowala kwambiri chosonyeza nyama imodzi yokha basi ya ku Africa.

Edward ankaphunzitsa luso lakeli anthu ena monga abale ake ndi anzake, ndipo pasanapite nthawi yaitali anthu amenewa anachititsa kuti luso limeneli lifike patali.

Zithunzi za Tingatinga zoyambirira zenizeni zinkajambulidwa ndi penti yowala kwambiri, komanso sizinkakhala zogometsa moti bwanji. Koma patapita zaka, lusoli linapita patsogolo kwambiri. Masiku ano chithunzi chilichonse chimajambulidwa ndi mitundu yosiyanasiyana ya penti komanso chimasonyeza zinthu zambiri monga nyama ndi zinthu zina zosiyanasiyana za ku Africa. Zimatha kusonyezanso anthu ali kumsika, kuchipatala kapena kumudzi.

Sasowa Zojambula

Anthu amene amajambula zithunzi za Tingatinga sasowa zojambula. Iwo amajambula nyama za mtundu uliwonse za ku Africa monga agwape, njati, njovu, akadyansonga, mvuwu, mikango, anyani, mbizi ndi nyama zina. Amajambulanso mbalame, nsomba, mitengo ndi maluwa osiyanasiyana. Zithunzi zimene amajambula zimakhala zokongola kwabasi. Nthawi zambiri pazithunzizi amasonyezaponso phiri la Kirimanjaro, lomwe ndi lalitali kwambiri ku Africa konse, ndipo limapezeka kumpoto chakum’mawa kwa dziko la Tanzania.

Kungoyambira pamene lusoli linayamba, zithunzi za Tingatinga zathandiza anthu aluso a ku Africa kujambula zinthu zakumtima kwawo, kwinaku akupeza ndalama zowathandiza pa moyo wawo. Panopa ku Dar es Salaam kuli bungwe la anthu ojambula zithunzi za Tingatinga. Ena mwa anthu ojambulawa akupitirizabe kujambula zithunzizi pogwiritsa ntchito penti yofanana ndi imene Tingatinga ankagwiritsa ntchito. Edward Tingatinga anamwalira m’chaka cha 1972, koma akanakhala kuti ali moyo, akanasangalala kwambiri kuona mmene luso lake lapitira patsogolo.