Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Matenda a Chingwangwa Avuta Kwambiri

Matenda a Chingwangwa Avuta Kwambiri

 Matenda a Chingwangwa Avuta Kwambiri

“Akuluakulu a zaumoyo a mumzinda wa Morelos . . . , mogwirizana ndi bungwe la zaumoyo la tawuni ya Emiliano Zapata, akupereka satifiketi iyi ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova . . . chifukwa chakuti [a Mboni] amagwira ntchito mogwirizana poonetsetsa kuti malo awo ndi osamalidwa bwino, n’cholinga choti udzudzu umene umayambitsa matenda a chingwangwa usamaswane.”

AKULUAKULU a boma ku Mexico ali ndi chifukwa chomveka chodera nkhawa za udzudzu umene umayambitsa matenda a chingwangwa chifukwa matendawa ndi oopsa kwambiri. M’chaka cha 2010 chokha, anthu pafupifupi 57,000 anadwala matendawa ku Mexico. Koma dzikolo ndi limodzi chabe pa mayiko oposa 100 komwe matendawa ndi ofala. Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse likuganiza kuti padziko lonse anthu oposa 50 miliyoni amadwala matendawa chaka chilichonse, ndipo pafupifupi anthu awiri pa anthu asanu alionse a padziko lapansi akhoza kudwala matendawa mosavuta. N’chifukwa chake akuluakulu a zaumoyo ayambitsa ntchito yolimbana ndi udzudzu umene umafalitsa matendawa.

Matenda a chingwangwa amafala m’madera otentha kwambiri, makamaka m’nyengo ya mvula kapena kukachitika masoka achilengedwe monga mphepo yamkuntho kapena madzi osefukira. Izi zili choncho chifukwa chakuti udzudzu umene umafalitsa matendawa umaikira mazira ake m’malo amene madzi sakuyenda. * Popeza kuti anthu a ku South America ndiponso a kufupi ndi nyanja ya Caribbean amakhala ndi zitsime zowaka ndi simenti pakhomo pawo, akatswiri a zaumoyo amawalimbikitsa kuti azivindikira zitsimezo. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti udzudzu usamaswane m’zitsimemo. Anthu amapewanso kuswana kwa udzudzu umenewu poonetsetsa kuti pakhomo pawo palibe zinthu zomwe zingasunge madzi monga matayala, zitini, miphika ya maluwa kapena mabeseni.

Zizindikiro za Matendawa Ndiponso Kulimbana Nawo Kwake

Nthawi zambiri anthu sazindikira msanga matenda a chingwangwa chifukwa zizindikiro zake zimafanana ndi za chimfine. Koma malinga ndi Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse, ngati mukuona zizindikiro monga kumva kuzizira, tizilonda tapakhungu, maso kupweteka, kuphwanya thupi ndiponso kumva kupweteka kwambiri m’mafupa, n’kutheka kuti muli ndi matendawa. Munthu angasonyeze zizindikiro zimenezi kwa masiku asanu kapena 7.

Panopa matendawa alibe mankhwala enieni, koma nthawi zambiri munthu akapezeka ndi matendawa amalangizidwa kuti azigona mokwanira komanso azimwa madzi ambiri ndi zakumwa zina. Komabe pamafunika kumusamalira wodwalayo mwapadera ngati wayamba kutuluka magazi m’mphuno ndi mkamwa kapena ngati magazi ake ayamba kuyenda pang’onopang’ono kuposa nthawi zonse. Zizindikiro zoopsazi zingayambe kuonekera pambuyo poti zizindikiro zoyamba zija zatha ndipo wodwalayo amaoneka ngati akuchira. Kodi wodwalayo amamva bwanji pa nthawi imeneyi? Iye amamva kupweteka kwambiri m’mimba, amasanza pafupifupi, amatuluka  magazi m’mphuno ndi m’kamwa, amatulutsa chimbudzi chakuda, ndipo thupi lake limakhala ndi matuza ooneka ofiirira. Komanso wodwalayo amanyong’onyeka, amamva ludzu kwambiri, khungu lake limayererako ndipo limazizira kwambiri, komanso magazi ake amayenda pang’onopang’ono.

Dziwani kuti mankhwala amene amapha mabakiteriya sachiritsa matendawa chifukwa matendawa amayambitsidwa ndi mavailasi. Ndiponso, ndi nzeru kupewa mankhwala ena monga aspirin ndi ibuprofen chifukwa amachititsa kuti wodwala azitaya magazi ambiri. Mavailasi amene amayambitsa matenda a chingwangwa alipo a mitundu inayi, choncho n’zotheka kudwala matendawa maulendo angapo.

Mukapezeka ndi matendawa, muzigona mokwanira komanso kumwa madzi ambiri ndi zakumwa zina. Komanso muzigona m’masikito kuti udzudzu usakulumeni n’kufalitsa matendawa kwa anthu ena.

Kuti munthu apewe kulumidwa ndi udzudzu wofalitsa matendawa, ayenera kuvala zovala zazitali manja, mathalauza kapena madiresi m’malo mwa zovala zazifupi komanso ayenera kudzola mafuta othamangitsa udzudzu. Ngakhale kuti udzudzu wofalitsa matendawa ungakulumeni nthawi ina iliyonse, nthawi zambiri umakonda kuluma dzuwa likangotuluka kumene komanso likamalowa. Kugona m’masikito onyikidwa m’mankhwala n’kothandizanso kwambiri.

N’kutheka kuti m’tsogolomu katemera wa matenda a chingwangwa adzapezeka. Ngakhale atapanda kupezeka, dziwani kuti Ufumu wa Mulungu udzathetseretu matenda onse. Nthawi idzafika pamene Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Udzudzu umene umafalitsa matenda a chingwangwa nthawi zambiri umauluka pafupi ndi pamene waikira mazira ake.

[Chithunzi patsamba 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Malo Amene Udzudzu Umakonda Kuswana

1. Matayala akutha

2. Malata otchinjirizira madzi a mvula

3. Miphika ya maluwa

4. Mabeseni

5. Zitini zakale

Mmene Mungapewere Kulumidwa ndi Udzudzu

a. Muzivala zovala zazitali manja, mathalauza ndi madiresi. Komanso muzidzola mafuta othamangitsa udzudzu

b. Muzigona m’masikito

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Source: Courtesy Marcos Teixeira de Freitas