Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumene Ndinadziwira Yemwe Adzathetse Kupanda Chilungamo

Kumene Ndinadziwira Yemwe Adzathetse Kupanda Chilungamo

 Kumene Ndinadziwira Yemwe Adzathetse Kupanda Chilungamo

Yosimbidwa ndi Ursula Menne

Kungoyambira ndili mwana, ndinkafunitsitsa kuona munthu aliyense akuchitiridwa zinthu zachilungamo. Koma pamapeto pake zimenezi zinachititsa kuti nditsekeredwe m’ndende. Ndipo kundendeko n’kumene ndinadziwa bwino chifukwa chake padzikoli palibe chilungamo. Dikirani ndikufotokozereni zambiri.

NDINABADWIRA m’tawuni yotchedwa Halle, m’dziko la Germany, m’chaka cha 1922. Tawuniyi ndi yakale kwambiri moti ili ndi mbiri ya zaka 1,200. Tawuni ya Halle ili kum’mwera chakum’mawa kwa mzinda wa Berlin, ndipo kuchokera mumzindawu munthu amayenda ulendo wautali makilomita 200. Kalelo, tawuni imeneyi inali imodzi mwa matawuni a ku Germany omwe munali anthu ambiri Achipulotesitanti. Mchemwali wanga Käthe anabadwa m’chaka cha 1923. Bambo anga ankagwira ntchito ya usilikali pamene mayi anga anali woimba.

Ndinatengera kwa bambo mtima woganizira anthu ovutika. Iwo atasiya ntchito ya usilikali, anagula shopu n’kutsegula sitolo. Makasitomala awo ambiri anali anthu osauka, choncho ankawapatsa zinthu pa ngongole. Koma chifundo chimenechi chinachititsa kuti bizinezi yawo igwe. Ndikanakhala wina, ndikanaphunzira pa zimene bambo anakumana nazo, kuti n’zovuta anthufe kuthetsa mavuto monga kuponderezana ndi zinthu zina zopanda chilungamo. Koma mwana ndi mwana, palibe chomwe ndinaphunzirapo.

Ndinatengeranso luso la mayi anga ndipo anaphunzitsa ineyo ndi Käthe kuimba ndiponso kuvina. Ndinali mwana wosangalala kwambiri, ndipo ine ndi mchemwali wanga tinkaona kuti tili ndi tsogolo labwino. Koma m’chaka cha 1939, zinthu zinasintha.

Chiyambi cha Mavuto

Nditamaliza maphunziro anga a kusekondale, ndinapita kusukulu yophunzitsa kuvina. Ndili kusukuluyi, ndinaphunzira luso lotha kuvina mogwedeza thupi lonse mwaukatswiri kwambiri. Mphunzitsi wa luso limeneli anali Mary Wigman. Pophunzitsa, ankajambula zithunzi zosonyeza anthu akuvina mogometsa. Zithunzi zake zinkatha kusonyeza mmene ovinawo akumvera. M’kupita kwa nthawi, nanenso ndinaphunzira luso la zojambulajambula. Choncho, chakumayambiriro kwa unyamata wanga, zinthu zinali bwino kwambiri. Inali nthawi yosangalatsa komanso yophunzira zinthu zatsopano. Koma kenako zinthu zinasokonekera. M’chaka cha 1939, nkhondo yachiwiri yapadziko lonse inayamba ndipo m’chaka cha 1941, bambo anga anamwalira ndi chifuwa chachikulu.

Kunena zoona, nkhondo si yabwino. Ngakhale kuti pamene nkhondo inkayamba n’kuti ndili ndi zaka 17 zokha, ndinkatha kuona kuti zinthu zaipa kwambiri. Anthu omwe poyamba anali abwinobwino anayamba kutsatira mfundo zankhanza za chipani cha Nazi. Kenako anthu anayamba kusankhana mitundu ndiponso kuphana. M’dera limene ndinkakhala, anthu achiwembu anaphulitsa bomba, moti nyumba yathu inasakazidwa kwambiri. Pa nthawi ya nkhondo imeneyi, abale anga ambiri ndithu anaphedwa.

Nkhondo itatha mu 1945, ineyo, mayi anga komanso mchemwali wanga Käthe, tinkakhalabe m’tawuni ya Halle. Apa n’kuti nditakwatiwa komanso ndili ndi mwana wamkazi. Komabe, banja lathu silinkayenda bwino, choncho ine ndi mwamuna wanga  tinapatukana. Popeza kuti tsopano ndinalibe munthu wondithandiza ndiponso wosamalira mwana wanga, ndinayamba kugwira ntchito ya zojambulajambula komanso kuyenda m’malo osiyanasiyana kukavina.

Pa nthawi imeneyi, dziko la Germany linagawidwa zigawo zinayi, ndipo tawuni yathu inali m’chigawo cholamuliridwa ndi Soviet Union. Choncho, tonse tinafunika kuzolowera ulamuliro wa chikomyunizimu. M’chaka cha 1949, chigawo chimene tinkakhala, chomwe chimadziwika kuti East Germany, chinakhala choima pachoka, ndipo chinayamba kudziwika ndi dzina lakuti German Democratic Republic (GDR).

Mmene Zinthu Zinalili mu Ulamuliro wa Chikomyunizimu

Mayi anga anadwala matenda aakulu ndipo ndinkafunika kuwasamalira. Choncho, ndinayamba kugwira ntchito ya mu ofesi m’boma. Pa nthawi imeneyi, ndinadziwana ndi ana asukulu omwe ankachita zinthu zosonyeza kukwiya ndi nkhanza zimene boma linkachita. Mwachitsanzo, boma linalamula kuti mwana wina wasukulu asaloledwe kupita kuyunivesite chifukwa chakuti bambo ake m’mbuyomo anali a chipani cha Nazi. Mwana ameneyu sanali wachilendo kwa ine, chifukwa nthawi zambiri tinkaimbira limodzi. Ndinkadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani akuzunza munthu wosalakwa?’ Ndinkaona kuti n’kulakwa kulanga mwana chifukwa cha zochita za bambo ake. Pang’ono ndi pang’ono, ndinayamba kugwirizana kwambiri ndi ana asukulu oukira aja. Ndinkachita nawo zionetsero zosonyeza kukwiya, moti tsiku lina, ndinamata zikalata zambirimbiri panja pa nyumba imene munali ofesi ya bwalo loweruzira milandu.

Ntchito yomwe ndinkagwira m’boma inali ya usekilitale, ndipo mwa zina ndinkataipa makalata a bungwe la boma lokhazikitsa mtendere. Koma ena mwa makalata amenewa anawonjezera mkwiyo wanga. Mwachitsanzo, nthawi inayake akuluakulu a bungweli anakonza zotumiza makalata olimbikitsa mfundo za chikomyunizimu kwa munthu wina wokalamba yemwe ankakhala ku West Germany. Iwo ankafuna kuti akuluakulu a boma akaona makalatawa, ayambe kuganiza kuti iye akugwirizana ndi dziko la East Germany, zomwe zikanamuika pa mavuto aakulu. Ndinakwiya kwambiri ndi kupanda chilungamo kumeneku, moti sindinatumize makalatawo. Ndinangowabisa pamalo enaake mu ofesi mwanga.

Ndinathandizidwa ndi “Munthu Woopsa Kwambiri”

Mu June 1951, anthu awiri analowa mu ofesi yanga n’kundiuza kuti: “Tabwera kudzakumanga.” Anthuwa anandimangadi, ndipo ananditengera kundende inayake yomwe inkadziwika kuti Ng’ombe Yofiira (Roter Ochse). Patatha chaka chimodzi, anandiweruza kuti ndili ndi mlandu woukira boma. Mwana wasukulu wina ndi amene anandineneza kwa apolisi achinsinsi. Iye anawauza kuti pa nthawi ina tinkachita zionetsero ndiponso tinkamata m’makoma mapepala odzudzula boma. Mlanduwo sunayende mwachilungamo chifukwa palibe aliyense amene analabadira zimene ndinanena, ndipo anandilamula kuti ndikhale m’ndende zaka 6. Ndili m’ndendemo ndinadwala kwambiri ndipo anandigoneka m’chipinda china pachipatala cha kundendeko pamodzi ndi azimayi ena pafupifupi 40. Azimayi ankaoneka okhumudwa kwambiri ndipo nditawaona, ndinayamba kuchita mantha moti ndinathamangira pachitseko n’kuyamba kuchimenya ndi chibakera.

Mlonda anandifunsa kuti, “Ukufuna chiyani?”

Ndinamuyankha kuti, “Munditulutsemo muno. Mundiike m’chipinda chandekha koma osati munomo.” Iye anangonyalanyaza pempho langa. Kenako ndinaona mayi wina yemwe ankaoneka wosiyana kwambiri ndi ena onsewo. Nkhope yake inkaoneka kuti alibe nkhawa mumtima mwake. Choncho, ndinapita kukakhala pafupi ndi mayiyu.

Koma ndinadabwa mayiyu akundiuza kuti, “Ngati ukufuna kukhala ndi ine, uyenera kusamala kwambiri. Anthu ena amati ndine munthu woopsa kwambiri chifukwa ndine wa Mboni za Yehova.”

Pa nthawiyi sindinkadziwa kuti boma la chikomyunizimu linkadana ndi Mboni za Yehova. Koma zimene ndinkadziwa ndi zoti ndili mwana, Ophunzira Baibulo awiri (dzina la Mboni pa nthawiyo) ankabwera kudzacheza ndi bambo. Ndipo ndinakumbukira mawu amene bambo ananena tsiku lina. Iwo anati, “Ophunzira Baibulo amaphunzitsa zinthu zoona.”

Ndinasangalala kwambiri mpaka kugwetsa misozi chifukwa chokumana ndi mayi ameneyu, yemwe dzina lake linali Berta Brüggemeier. Ndinamupempha kuti, “Chonde, ndiuzeniko zambiri zokhudza Yehova.” Kuyambira nthawi imeneyi, tinkakhala nthawi yaitali tikucheza ndipo nthawi zambiri tinkakambirana nkhani za m’Baibulo. Zina zimene ndinaphunzira zinali zoti Mulungu woona, Yehova, ndi Mulungu wachikondi, wachilungamo komanso wamtendere. Ndinaphunziranso kuti iye adzathetsa mavuto onse amene anthu oipa ndi ankhanza abweretsa. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena, kuti: “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. . . . Koma anthu ofatsa adzalandira  dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.

Nditatuluka M’ndende Ndinakakhala ku West Germany

Ndinatulutsidwa m’ndende m’chaka cha 1956, nditakhalamo zaka zisanu ndi miyezi ingapo. Patapita masiku asanu, ndinachoka ku German Democratic Republic kupita ku West Germany. Panthawiyi ndinali ndi ana awiri aakazi, Hannelore ndi Sabine, ndipo ndinapita nawo limodzi. Ndili kumeneku, ine ndi mwamuna wanga uja tinasudzulana ku khoti ndipo kenako ndinakumananso ndi Mboni za Yehova. Pamene ndimaphunzira Baibulo, ndiyamba kusintha zinthu zina ndi zina pa moyo wanga kuti zochita zanga zizigwirizana ndi zimene Yehova amafuna. Ndipo m’chaka cha 1958 ndinabatizidwa.

Patapita nthawi ndinakwatiwanso, koma tsopano ndi mwamuna wa Mboni za Yehova, dzina lake Klaus Menne. Ine ndi Klaus tinali ndi banja losangalala kwambiri, ndipo tinabereka ana awiri, Benjamin ndi Tabia. Koma mwatsoka, Klaus anamwalira pa ngozi yapamsewu pafupifupi zaka 20 zapitazo, ndipo kuchokera nthawi imeneyo sindinakwatiwenso. Ndimalimba mtima kudziwa kuti akufa adzauka n’kukhala ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi. (Luka 23:43; Machitidwe 24:15) Ndimasangalalanso kuona kuti ana anga onse anayi akutumikira Yehova.

Kuchokera pa zimene ndaphunzira m’Baibulo, ndadziwa kuti ndi Yehova yekha amene angachititse kuti padzikoli pakhale chilungamo chenicheni. Mosiyana ndi anthu, iye amatimvetsa bwino kwambiri. Amadziwa zonse zimene zikutichitikira komanso mmene tinakulira. Kudziwa zimenezi kwandithandiza kwambiri kuti ndizikhala ndi mtendere wamumtima, makamaka ndikamaona anthu akuchita zinthu zopanda chilungamo. Lemba la Mlaliki 5:8 limati: “Ukaona munthu wosauka akuponderezedwa ndiponso zinthu zachiwawa ndi zopanda chilungamo zikuchitika m’chigawo cha dziko, usadabwe nazo. Pakuti wamkulu kuposa amene akuchita zimenezoyo akuona, ndipo pamwamba pa akuluakuluwo palinso ena akuluakulu kuposa iwowo.” “Wamkulu” amene amaona zinthu zopanda chilungamo zikamachitika ndi Mlengi wathu. Ponena za iye, lemba la Aheberi 4:13 limati: “Kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu.”

Zimene Ndaona pa Zaka Pafupifupi 90 za Moyo Wanga

Nthawi zina anthu amandifunsa mmene moyo unalili pa nthawi ya ulamuliro wa Nazi ndi wa chikomyunizimu. Moyo unali wovuta kwambiri nthawi imeneyi. Maboma awiri onsewa, monga mmene zilili ndi maboma onse a anthu, anasonyeza kuti anthu sangakwanitse kudzilamulira okha. Baibulo limanena zoona kuti: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”—Mlaliki 8:9.

Pamene ndinali mwana sindinkadziwa zambiri, ndipo ndinkaganiza kuti anthu angabweretse ulamuliro wachilungamo. Panopa ndazindikira kuti ndi Mlengi wathu yekha amene angabweretse chilungamo chenicheni padzikoli. Iye adzachita zimenezi powononga anthu onse oipa, n’kupatsa Mwana wake, Yesu Khristu, mphamvu zolamulira dziko lapansi. Yesu adzakhala wolamulira wabwino chifukwa amaganizira anthu nthawi zonse. Ponena za Yesu, Baibulo limati: “Unakonda chilungamo ndipo unadana ndi kusamvera malamulo.” (Aheberi 1:9) Ndimathokoza kwambiri Mulungu chifukwa anandikokera kwa Mfumu yabwino ndi yachilungamo imeneyi, ndipo ndikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha mu ulamuliro wake.

[Chithunzi patsamba 23]

Ine ndi ana anga aakazi, Hannelore ndi Sabine, titangofika kumene ku West Germany

[Chithunzi patsamba 23]

Ineyo ndi mwana wanga wamwamuna, Benjamin, ndi mkazi wake, Sandra