Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Funso Lofunika Kwambiri Kuposa Mafunso Onse

Funso Lofunika Kwambiri Kuposa Mafunso Onse

 Funso Lofunika Kwambiri Kuposa Mafunso Onse

“WASAYANSI wina, dzina lake Francis S.  Collins, ananena kuti: “Palibe funso lofunika kwambiri limene anthu akhala akufunsa kwa nthawi yaitali kuposa lakuti, ‘Kodi Mulungu alipo?’” Yankho la funso limeneli ndi lofunika kwambiri chifukwa ngati kulibe Mulungu, ndiye kuti munthu akafa, wafa basi ndipo palibenso chiyembekezo choti adzauka. Komanso ngati kulibe Mulungu, ndiye kuti anthu akhoza kumangochita zinthu zoipa popanda kuganizira kuti Mulungu akuwaona.

Anthu ambiri amakayikira zoti kuli Mulungu chifukwa chakuti asayansi ambiri amanena kuti kulibe Mulungu. Komabe dziwani kuti zimene asayansi amenewa amakhulupirira zikhoza kukhala zolakwika kwambiri, monga mmene nkhani yotsatira isonyezere.

Koma si asayansi okha amene akusokoneza anthu. Zipembedzo zambiri padzikoli zikusokonezanso anthu powaphunzitsa zinthu zabodza zosagwirizana ndi sayansi. Mwachitsanzo, zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti Mulungu analenga dzikoli m’masiku 6 enieni, zaka masauzande angapo zapitazo, pamene Baibulo limasonyeza kuti masiku amenewa ndi ophiphiritsa.

Chifukwa chouzidwa zinthu zambirimbiri zosokoneza, anthu ambiri amasiya kufufuza umboni wotsimikizira zoti Mulungu alipo. Koma tonsefe tiyenera kudziwa zolondola pa nkhani yofunika kwambiri imeneyi. Komabe, anthu amene amati kuli Mulungu sanayambe amuonapo, komanso anthu amene amati Mulungu kulibe, sanayambe aona zinthu zikusanduka n’kukhala zinthu zamtundu wina. Choncho, kaya timati Mulungu alipo kapena kulibe, nkhani imeneyi ndi yongofunika chikhulupiriro. Ngakhale zili choncho, chikhulupiriro chathucho chiyenera kukhala ndi umboni wokwanira wotsimikizira kuti zimene timakhulupirirazo n’zoona?

Chikhulupiriro Chenicheni Chimafuna Umboni Wokwanira

Chikhulupiriro n’chofunika kwambiri pa moyo wathu. Timalola kugwira ntchito inayake chifukwa chokhulupirira kuti tilandira malipiro. Timabzala mbewu chifukwa chokhulupirira kuti mbewuzo zimera n’kukula. Timakhulupirira zimene anzathu amatiuza. Timakhulupirira malamulo a m’chilengedwe. Koma sikuti timangokhulupirira m’chimbulimbuli. Pamakhala umboni wamphamvu wotipangitsa kukhulupirira zimenezi. N’chimodzimodzinso pa nkhani ya Mulungu. Payenera kukhala umboni wotsimikizira kuti Mulungu alipo.

Palemba la Aheberi 11:1, Baibulo limati: “Chikhulupiriro ndicho . . . umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” Mwachitsanzo, tinene kuti mukuyenda m’mphepete mwa nyanja. Mwadzidzidzi mukumva chivomezi ndipo nthaka ikugwedezeka. Kenako mukuona madzi akubwera kuchokera m’nyanja kupita kumtunda. Mwamsanga mukhoza kudziwa kuti madziwo akafika kumtunda akokolola zinthu. M’chitsanzo chimenechi, chivomezi komanso kuyenda kwa madzi ndi “umboni wooneka” wa zinthu zimene zichitike posachedwa, zomwe ndi kukokoloka kwa nthaka. Chifukwa chokhulupirira kuti pamene mulipo nthaka ikokoloka, mukhoza kuthawira kumalo okwera kuti mupulumuke.

N’chimodzimodzinso ndi kukhulupirira kuti Mulungu aliko. Payenera kukhala umboni wooneka wotsimikizira kuti iye alipodi. Apa ndi pamene Mulungu angakhale weniweni ngakhale kuti sitingathe kumuona. Simufunikira kuchita kukhala katswiri wa sayansi kuti mufufuze ndi kupeza umboni wakuti Mulungu aliko. Wasayansi wina, dzina lake Vladimir Prelog, amene analandirako mphoto ya Nobel, ananena kuti: “Sikuti akatswiri asayansi amene analandirapo mphoto ya Nobel amadziwa zambiri zokhudza Mulungu, chipembedzo komanso zimene zimachitika munthu akafa, kuposa anthu ena.”

Ngati mutakhala ndi mtima wofuna kudziwa choonadi komanso ngati muli wokonzeka kusintha maganizo anu, mukhoza kudziwa zolondola zokhudza nkhani imeneyi. Koma kodi pali umboni wotani wotsimikizira kuti Mulungu alipo?

[Chithunzi patsamba 3]

Mlimi amakhulupirira kuti akabzala mbewu zimera n’kukula