Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

 Zochitika Padzikoli

Akatswiri a ku Canada ndi ku United States atafufuza zinthu zokwana 5,296 zolembedwa kuti “zosawononga chilengedwe,” anapeza kuti panalibe umboni wotsimikizira kuti zinthu 95 pa 100 zilizonse zinalidi “zosawononga chilengedwe.”—TIME, U.S.A.

Anthu oona za chitetezo pabwalo la ndege la Bangkok, ataunika chikwama cha mayi wina, “anaganiza kuti mayiyo wabisa chinachake.” Anthuwo atatsegula chikwamacho, anapeza kuti munali kamwana ka nyalugwe. Kamwanako kanali katagona chifukwa kanapatsidwa mankhwala ogonetsa tulo.​—WORLD WILDLIFE FUND, THAILAND.

M’nkhalango ya Amazon Muli Zamoyo Zambiri

Nkhalango yozungulira mtsinje wa Amazon ndi imodzi mwa nkhalango zimene zili ndi zamoyo zambiri padziko lonse. Bungwe lina loona za nyama zakuthengo padziko lonse linanena kuti pa zaka 10 zapitazi, asayansi apeza kuti m’derali muli mitundu yosiyanasiyana yopitirira 1,200 ya nyama ndiponso zomera. Zimenezi zikutanthauza kuti pa masiku atatu alionse, amatulukira mtundu watsopano wa zamoyo. Akuti m’derali mumapezeka mitundu yosiyanasiyana ya nsomba, achule, mbalame, njoka, ng’ona ndi zina zotero. Sarah Hutchison, yemwe ndi mkulu wa bungweli ku Brazil, anati: “Tikutulukirabe zamoyo zatsopano m’nkhalangoyi, ndipotu chiwerengero cha zamoyo chimene tikupezachi sichikuphatikizapo mitundu yambirimbiri ya tizilombo.”

Anthu Ambiri Akupanikizika ndi Ntchito

Munthu mmodzi pa anthu asanu alionse a ku Finland, amalephera kugwira bwino ntchito chifukwa choiwalaiwala komanso kulephera kuika maganizo onse pa ntchito. Lipoti la bungwe lina la ku Finland loona za umoyo wa anthu apantchito linanena kuti, vuto lopanikizika ndi ntchito likukhudza kwambiri anthu azaka 35 kapena kucheperapo. Izi n’zodabwitsa chifukwa anthu azaka zimenezi amayenera kukhala amphamvu. Zina mwa zinthu zimene zikuchititsa vuto limeneli ndi kupita patsogolo kwa makompyuta komanso kusinthasintha kwa malangizo ogwirira ntchito. Pulofesa Kiti Müller ananena kuti: “Anthu ambiri amaona kuti amapatsidwa malangizo ambirimbiri ogwirira ntchito yawo, moti sadziwa bwinobwino malangizo oyenera kuwatsatira.” Nyuzipepala ya Helsinki Times inati: “Munthu akapanikizika kwa nthawi yaitali, thupi lake limazolowera, ndipo kenako sadziwanso kuti akupanikizika. Amadzadziwa akadzadwala.”

Masewera Achiwawa a pa Kompyuta Amapangitsa Anthu Kukhala Olusa

Kodi munthu akachita masewera achiwawa a pa kompyuta, amakhala nthawi yaitali bwanji ali wolusa? Akatswiri ena anasankha anyamata ndi atsikana apasukulu kuti ena achite masewera achiwawa a pa kompyuta ndipo ena achite masewera opanda chiwawa kwa mphindi 20. Atamaliza masewerawo, akatswiriwo anauza theka la gulu lililonse kuti liziganizira za masewera amene linachitawo. Kenako tsiku lotsatira, akatswiriwo anapatsa anyamata ndi atsikanawo zochita zina. Iwo anawauza kuti apikisane ndi munthu amene amaoneka kuti ndi wovuta m’filimu, ndipo amene apambane amulanga mnzakeyo pomusokosera kwambiri m’makutu. Zotsatira zake zinali zakuti, anyamata amene anauzidwa kuti aganizire za masewera achiwawawo anayamba kuchita zinthu zachiwawa. Koma akatswiriwo anapeza kuti atsikana, amene mwachibadwa amadana ndi masewera achiwawa, sanasinthe kwenikweni n’kuyamba kuchita zinthu zachiwawa.