Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nzeru Zothandiza Munthu Kukhala ndi Thanzi Labwino

Nzeru Zothandiza Munthu Kukhala ndi Thanzi Labwino

 Nzeru Zothandiza Munthu Kukhala ndi Thanzi Labwino

“Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu.”—MIYAMBO 14:30.

“Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa.”—MIYAMBO 17:22.

● Mawu anzeru amenewa ananenedwa ndi mfumu Solomo ya ku Isiraeli zaka 3,000 zapitazo. * Koma kodi ndi oonadi? Kodi akatswiri azachipatala amati chiyani?

Posiyanitsa munthu amene ali ndi mtima wodekha ndi amene sachedwa kupsa mtima, magazini ina ya zachipatala ya ku America (Journal of the American College of Cardiology), inati: “Kafukufuku waposachedwapa akusonyeza kuti anthu amene sachedwa kupsa mtima komanso amene amakonda kusunga mkwiyo, nthawi zambiri amadwala matenda a mtima.” Magaziniyo inapitiriza kuti: “Mankhwala abwino a matenda a mtima amaphatikizapo kupewa kupsa mtima ndi kusunga mkwiyo osati kungochita masewera olimbitsa thupi kapena kumwa mankhwala akuchipatala.” Mwachidule, tingati anthu amene ali ndi mtima wodekha amakhala ndi thanzi labwino, mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena.

Komanso anthu omwe nthawi zambiri amakhala osangalala amapewa matenda a mtima. Dokotala wina wa ku Scotland, dzina lake Derek Cox, ananena pa wailesi ya BBC kuti: “Anthu amene amakhala osangalala, m’tsogolo sadzadwaladwala kuyerekeza ndi anthu amene sasangalala.” Iye ananenanso kuti: “Nthawi zambiri anthu amene amakhala osangalala sadwala matenda a mtima ndiponso ofa ziwalo.”

Kodi zinatheka bwanji kuti Solomo, komanso anthu ena amene analemba Baibulo, alembe zinthu zanzeru zomwe n’zothandiza mpaka pano? Yankho lake n’losavuta. Baibulo limati: “Mulungu anapitiriza kupatsa Solomo nzeru zopanda malire.” (1 Mafumu 4:29) Chinthu chinanso chochititsa chidwi n’chakuti, nzeru zimenezi zinalembedwa mosavuta kumva kuti aliyense apindule nazo. Komanso nzeru zimenezi n’zaulere.

Mungachite bwino kumawerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Anthu mamiliyoni ambiri amene amawerenga Baibulo tsiku ndi tsiku apindula kwambiri. Iwo azindikira kuti mawu awa ndi oona: “Nzeru zikalowa mumtima mwako, ndipo kudziwa zinthu kukakhala kosangalatsa m’moyo wako, kuganiza bwino kudzakuyang’anira, ndipo kuzindikira kudzakuteteza.” (Miyambo 2:10, 11) Choncho, kuwerenga Baibulo n’kofunika kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Baibulo likamanena za “mtima” nthawi zambiri limatanthauza umunthu wathu.