Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anthu Akuvutika Chonchi?

N’chifukwa Chiyani Anthu Akuvutika Chonchi?

 N’chifukwa Chiyani Anthu Akuvutika Chonchi?

ATSOGOLERI achipembedzo amene amati amadziwa yankho la funso limeneli, amaphunzitsa kuti mavuto amene anthu amakumana nawo ndi chilango chochokera kwa Mulungu. Mwachitsanzo, posachedwapa ku Haiti kutachitika chivomezi, m’busa wina anauza anthu a m’tchalitchi chake kuti chivomezicho chinali ngati uthenga wochokera kwa Mulungu. Anthu ena sadziwa bwinobwino chimene chimachititsa mavuto. Mwachitsanzo, pulofesa wina wa maphunziro a zachipembedzo ku America ananena kuti anthu ambiri amati: “Palibe angadziwe chifukwa chimene Mulungu amachititsira mavuto ndipo anthufe tilibe ufulu wodziwa zimenezi. Ife kwathu n’kungokhala ndi chikhulupiriro basi.”

Kodi ndi zoona kuti Mulungu ndiye amachititsa kuti anthu azivutika? Baibulo limayankha mosapita m’mbali kuti ayi. Pamene Yehova Mulungu analenga anthu oyambirira, analibe cholinga choti anthuwo azidzavutika. Komabe, anthu awiri oyambirirawo anapandukira ulamuliro wa Mulungu n’cholinga choti azidzisankhira okha chabwino ndi choipa. Pamapeto pake iwo anakolola zimene anafesa. Ngakhale masiku ano anthufe timavutika chifukwa cha kusamvera kwawo. Koma sikuti Mulungu ndi amene anayambitsa kuti anthu azivutika. Baibulo limati: “Munthu akakhala pa mayesero asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yakobo 1:13) Ngakhale atumiki a Mulungu amakumana ndi mavuto ndipo zitsanzo zotsatirazi zikusonyeza zimenezi.

● Mneneri Elisa anadwala matenda amene pamapeto pake anafa nawo.—2 Mafumu 13:14

● Mtumwi Paulo analemba kuti iye ndi atumiki anzake anali ‘anjala ndi aludzu ndi ausiwa komanso ankazunzidwa ndi kusowa pokhala.’—1 Akorinto 4:11.

● Mkhristu wina dzina lake Epafurodito anadwala komanso ‘anavutika maganizo.’—Afilipi 2:25, 26.

Koma palibe paliponse m’Baibulo pamene timawerenga kuti anthu amenewa ankalangidwa ndi Mulungu chifukwa cha machimo amene anachita. Baibulo limatiuza kuti si Mulungu amene amachititsa kuti anthu azikumana ndi mavuto. Koma sizokhazo. Limafotokozanso zinthu zitatu zimene zimachititsa kuti anthu azikumana ndi mavuto.

 Zosankha Zathu

Baibulo limati: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.” (Agalatiya 6:7) Munthu amene amasuta fodya, kuyendetsa galimoto mosasamala komanso kugwiritsa ntchito ndalama mosasamala amapeza mavuto.

Nthawi zina timavutika chifukwa cha zosankha za anthu ena odzikonda. Ndipotu zinthu zoipa kwambiri zimene zimachitika padzikoli zimachitidwa ndi anthu. Mwachitsanzo, anthu anachita zankhanza kwambiri pa nthawi ya ulamuliro wa Nazi ku Germany. Ndipo masiku ano anthu amachitira ana nkhanza zosaneneka. Ena amagwiritsa ntchito ufulu wawo molakwika, ndipo zimenezi zimachititsa kuti anthu ena azivutika.

Zinthu Zongotigwera

Kale kwambiri m’nthawi ya atumwi, nsanja inayake yaikulu ya ku Yerusalemu inagwa n’kupha anthu 18. Ponena za anthu amene anaphedwawo, Yesu anafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti iwo anali ochimwa kwambiri kuposa anthu onse okhala mu Yerusalemu? Ndithudi ayi.” (Luka 13:4, 5) Yesu ankadziwa kuti anthuwo sanafe chifukwa chakuti Mulungu amawalanga. Iye ankadziwa zimene Mawu a Mulungu anali atanena kale kuti: “Nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.” (Mlaliki 9:11) Anthu ambiri amakumana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa chakuti ali pamalo olakwika komanso panthawi yolakwika kapena chifukwa chakuti anthu ena analakwitsa zinazake. Mwachitsanzo malipoti amasonyeza kuti anthu amene amanyalanyaza machenjezo komanso amene amamanga nyumba zosalimba m’madera amene mumachitika zivomezi kapena masoka ena achilengedwe, ndi amene amavutika kwambiri.

“Wolamulira wa Dzikoli”

Baibulo limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (Yohane 12:31; 1 Yohane 5:19) “Woipayo” ndi Satana Mdyerekezi, yemwe m’Baibulo amamufotokoza kuti ndi mzimu wamphamvu, “wolamulira wa mpweya.” Satana ndi amene amalimbikitsa mzimu womwe ‘tsopano ukugwira ntchito mwa ana a kusamvera.’ (Aefeso 2:2) Mfundo imeneyi ndi yoona, chifukwa zinthu zina zimene anthu amachita zimakhala zoopsa kwambiri, moti zimavuta kukhulupirira kuti anthu paokha angachite zimenezo.

Komabe, kodi zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu alibe nazo kanthu akamaona anthu akuvutika? Kodi iye azingolekerera zimenezi kuchitika mpaka kalekale?