Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amatiganiziradi?

Kodi Mulungu Amatiganiziradi?

Kodi Mulungu Amatiganiziradi?

PA November 1, 1755, mu mzinda wa Lisbon ku Portugal, munachitika chivomezi chachikulu. Chivomezichi chinachititsa kuti madzi asefukire komanso kuti mumzindamo muyake moto. Anthu masauzande ambiri anafa.

Ku Haiti kutachitika chivomezi m’chaka cha 2010, nyuzipepala ina ya ku Canada yotchedwa National Post inanena kuti: “Masoka onse akuluakulu amayesa chikhulupiriro chathu mwa Mulungu. Koma chivomezi chachikulu kwambiri cha ku Lisbon komanso chimene chachitika posachedwapa ku Haiti, chikuyesa kwambiri chikhulupiriro chathu kuposa masoka ena onsewo.” Nyuzipepalayo inamaliza ndikunena kuti: “Mulungu ayenera kuti walinyanyala dziko la Haiti.”

Monga Mlengi “Wamphamvuyonse,” Yehova Mulungu ali ndi mphamvu zopanda malire ndipo akhoza kuthetsa mavuto onse amene anthu amakumana nawo. (Salimo 91:1) Ndipo iye amatisamalira. Nanga tingatsimikizire bwanji kuti iye amatisamaliradi?

Zimene Tikudziwa Zokhudza Mulungu

Mulungu amamva chisoni akamaona anthu akuvutika. Aisiraeli ali ku ukapolo ku Iguputo komwe ankazunzidwa kwambiri, Mulungu anauza Mose kuti: “Ndaona nsautso ya anthu anga amene ali ku Iguputo, ndipo ndamva kulira kwawo chifukwa cha amene akuwagwiritsa ntchito mwankhanza. Zoonadi, ndikudziwa bwino zowawa zawo.” (Ekisodo 3:7) Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu amamva chisoni akamaona anthu akuvutika. Ndipo nthawi ina pamene Aisiraeli ankavutika, mneneri Yesaya analemba kuti: “Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.”—Yesaya 63:9.

“Njira zake zonse ndi zolungama.” (Deuteronomo 32:4) Chilichonse chimene Mulungu amachita chimakhala chachilungamo komanso chopanda tsankho. Posonyeza kuti Mulungu ndi wachilungamo, Baibulo limati: “Adzateteza njira ya anthu ake okhulupirika.” (Miyambo 2:8) Ndipo limanenanso kuti ‘adzabwezera masautso kwa amene akusautsa’ anthu ake olungama. (2 Atesalonika 1:6, 7) Posonyeza kuti Mulungu ndi wopanda tsankho, Baibulo limati: “Saganizira kwambiri wolemekezeka kuposa wonyozeka, chifukwa onsewo anapangidwa ndi manja ake.” (Yobu 34:19) Komanso mosiyana ndi anthu, Mulungu amadziwa njira yabwino kwambiri yothetsera mavuto amene anthu akukumana nawo. Zimene anthu amachita pofuna kuthetsa mavuto tingaziyerekezere ndi dokotala amene akugwiritsa ntchito kabandeji pochiza bala lalikulu lomwe munthu wachita kuwomberedwa ndi mfuti. Kuchita zimenezi n’kosathandiza chifukwa balalo silingapole.

Mulungu ndi “wachifundo ndi wachisomo . . . wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.” (Ekisodo 34:6) Baibulo likamanena za “chifundo,” limatanthauza kudera nkhawa munthu wina kapena kumumvera chisoni ndipo kenako n’kumuthandiza. Mawu a Chiheberi amene amamasuliridwa kuti “chisomo,” amatanthauza “kukhudzidwa mtima komanso kukhala ndi mtima wofuna kuthandiza munthu amene akuvutika.” Malinga ndi buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo, mawu akuti “kukoma mtima,” amatanthauza “kuyesetsa kuchita chinachake n’cholinga chopulumutsa munthu amene ali pamavuto.” Choncho, Yehova Mulungu akamaona anthu akuvutika, sikuti amangovutika mumtima basi, koma amachitapo kanthu chifukwa iye ndi wachifundo, wachisomo komanso wokoma mtima. Choncho, sitiyenera kukaikira zoti iye adzathetsa mavuto athu onse.

M’nkhani yapitayo tinakambirana zinthu zitatu zimene zimachititsa kuti anthu azivutika ndipo taona kuti si Mulungu amene amachititsa zimenezi. Tsopano tiyeni tikambirane zimene zimachititsa kuti zinthu zitatu zimenezi zizichitika.

Zosankha Zathu

Poyambirira penipeni Adamu ankalamulidwa ndi Mulungu koma kenako atayesedwa anasankha kupandukira Yehova. Iye sankafuna kuti azilamuliridwa ndi Mulungu. Ananyalanyaza chenjezo limene Yehova anamuuza pa Genesis 2:17 kuti akadzaphwanya lamulo lake ‘adzafa ndithu.’ Chifukwa chokana ulamuliro wabwino kwambiri wa Mulungu, uchimo ndi kupanda ungwiro zinalowa m’dziko. Baibulo limafotokoza kuti: “Uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Komabe Mulungu adzachotsa mavuto onse amene uchimo watibweretsera.

Zinthu Zongotigwera

Monga mmene taonera pamwambapa, munthu woyamba, Adamu, sanamvere malangizo ochokera kwa Mulungu, omwe cholinga chake chinali kuteteza moyo wa anthu ku zinthu zoopsa, kuphatikizapo masoka achilengedwe. Zimene anachitazi zili ngati kunyalanyaza malangizo othandiza a dokotala. Ngati wodwala sakudziwa bwinobwino kuopsa konyalanyaza malangizo amene dokotala wamupatsa, akhoza kudwala kwambiri kapena kufa kumene. Mofanana ndi zimenezi, anthu amanyalanyaza malangizo okhudza mmene angasamalire dziko lapansili ndipo n’chifukwa chake amavutika kwambiri kukachitika masoka achilengedwe. Iwo amamanga nyumba zosalimba m’madera amene mumachitika masoka achilengedwe komanso sadziwa zonse zokhudza mmene masoka achilengedwe amachitikira. Komabe Mulungu sadzalekerera kuti mavuto amenewa apitirire mpaka kalekale.

“Wolamulira wa Dzikoli”

Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu analola kuti Satana, amene anali atamupandukira, alamulire dzikoli kwa nthawi yaitali chonchi? Ena amanena kuti “nthawi zambiri munthu akatenga boma n’kuyamba kulamulira, koyambirira kwenikweni amaimba mlandu wolamulira wakale kuti ndi amene anayambitsa mavuto amene iye akukumana nawo.” Mofanana ndi zimenezi, ngati Yehova akanamuchotsa “wolamulira wa dzikoli” mwamsanga, bwenzi Satanayo akuimba mlandu Yehova monga wolamulira wakale kuti ndiye wamulepheretsa kukwaniritsa zolinga zake zabwino. (Yohane 12:31) Koma popeza Yehova anamupatsa Satana nthawi yokwanira yolamulira dzikoli, zimene ulamuliro wake wachita zikusonyezeratu kuti iye si wolamulira wabwino. Komabe funso ndi lakuti, Kodi tingatsimikizire bwanji kuti mavuto amene anthu akukumana nawo adzatha?

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi dokotala angagwiritse ntchito kabandeji pochiza bala lalikulu lomwe munthu wachita kuwomberedwa ndi mfuti?