Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Baibulo Limalimbikitsa Ukapolo?

Kodi Baibulo Limalimbikitsa Ukapolo?

 Zimene Baibulo Limanena

Kodi Baibulo Limalimbikitsa Ukapolo?

BAIBULO limanena kuti chikondi n’chofunika kwambiri. Komabe, anthu ena amadabwa kuti Baibulo lomwelo limanena za ukapolo, womwe sugwirizana ngakhale pang’ono ndi chikondi. Choncho, iwo amaganiza kuti Baibulo limalimbikitsa ukapolo.

Baibulo limasonyeza kuti kale Mulungu ankalola anthu ake kukhala ndi akapolo. (Genesis 14:14, 15) Ngakhale m’nthawi ya atumwi, Akhristu ena ankakhala ndi akapolo ndipo Akhristu enanso anali akapolo. (Filimoni 15, 16) Koma kodi zimenezi zikusonyeza kuti Baibulo limalimbikitsa anthu kukhala ndi akapolo n’kumawachitira nkhanza?

Miyambo ndi Zikhalidwe Zotsutsana ndi Baibulo

Pamene Baibulo linkalembedwa n’kuti anthu akutsatira kale miyambo ndi zikhalidwe zimene zinkatsutsana ndi mfundo za Mulungu. Ngakhale kuti Chilamulo chimene iye anapereka chinaletsa miyambo ina, Mulungu sanaletse ukapolo.

Pofotokoza zinthu zokhudza mtundu wa Isiraeli, buku lina limati: “Iwo ankakhala ngati pachibale. Sankafuna kuti papezeke munthu aliyense wosauka. Sankafunanso kuti akazi ndi ana amasiye komanso anthu osowa pokhala azizunzidwa.” Choncho, m’malo mothetsa ukapolo, Mulungu anangowapatsa Aisiraeli malamulo okhudza mmene ayenera kuchitira ndi akapolo awo. Malamulowa ankathandiza kuti akapolo asamazunzidwe.

Ukapolo M’nthawi ya Aisiraeli

Taganizirani malamulo otsatirawa amene Mulungu anapatsa Aisiraeli kudzera mwa Mose:

Wakuba munthu ndi kum’gulitsa ankafunika kuphedwa. (Ekisodo 21:16) Ngakhale kuti panali lamulo limeneli, akapolo ankapezekabe. N’zoona kuti panali zinthu zambiri zothandiza kuti munthu asakhale wosauka, komabe nthawi zina mwina chifukwa chosayendetsa bwino chuma chake, munthu ankapezeka kuti wasauka komanso ali ndi ngongole yaikulu. Munthu wotero ankadzigulitsa ngati kapolo. Nthawi zina zimenezi zikachitika, munthuyo ankatha kupeza ndalama n’kulipira kuti amasulidwe.—Levitiko 25:47-52.

Lemba la Levitiko 25:39, 40 limati: “M’bale wanu akasauka pakati panu n’kudzigulitsa kwa inu, musam’gwiritse ntchito ngati kapolo. Mum’tenge ngati waganyu, ndiponso ngati mlendo.” Lamulo limeneli linkathandiza kuti anthu osauka kwambiri azisamalidwa. Choncho, akapolo sankazunzidwa ngati mmene zakhala zikuchitikira m’mayiko ena kwa zaka zambiri.

Munthu akapezeka ndi mlandu wakuba, n’kulephera kulipira zinthu zimene wabazo mogwirizana ndi Chilamulo, ankagulitsidwa ngati kapolo n’cholinga choti apeze ndalama zolipirira mlandu wakewo. (Ekisodo 22:3) Akamaliza kulipira ngongoleyo, ankamasulidwa.

Malamulo amene Mulungu anapatsa Aisiraeli sankalola kuti akapolo azizunzidwa. Ngakhale kuti anthu amene ankakhala ndi akapolo, ankaloledwa kulangiza ndi kulanga akapolo awo, iwo ankauzidwa kuti asamachite zimenezi mopitirira muyezo. Ndipo munthu amene wapha kapolo wake ankalangidwa. (Ekisodo 21:20) Kapolo akamenyedwa ndi mbuye wake mpaka kuvulazidwa, mwina kuchotsedwa dzino kapena diso, kapoloyo ankamasulidwa.—Ekisodo 21:26, 27.

Malamulo a Mulungu sankalola kuti munthu akhale kapolo kwa zaka zoposa 6. (Ekisodo 21:2) Kapolo ankamasulidwa m’chaka cha 7 cha ukapolo wake. Komanso Chilamulo chinkanena  kuti pakatha zaka 50 zilizonse, Aisiraeli onse amene ali akapolo ayenera kumasulidwa, mosaganizira kuti akhala zaka zingati ali akapolo.—Levitiko 25:40, 41.

Ikafika nthawi yoti kapolo amasulidwe, mbuye wake ankafunikira kumupatsa zinthu. Lemba la Deuteronomo 15:13, 14 limati: “Ukam’masula ndi kumulola kuchoka, usamulole kuchoka chimanjamanja. Uzim’patsako ndithu zina mwa nkhosa zako, mbewu zochokera pamalo ako opunthira, mafuta ochokera pamalo oyengera ndi vinyo wochokera moponderamo mphesa.”

M’nthawi ya Yesu, ukapolo unali wofala kwambiri mu Ulamuliro wa Aroma. Pamene Chikhristu chinkafalikira, anthu ena amene anali akapolo komanso amene ankasunga akapolo, anamva uthenga wabwino n’kukhala Akhristu. Yesu ndi atumwi ake sankanena mu ulaliki wawo kuti ukapolo umene unalipo pa nthawiyo uyenera kutha, chifukwa analibe cholinga chosintha chikhalidwe cha anthuwo. Komabe, akapolo komanso ambuye awo ankalimbikitsidwa kuti azikondana monga abale.—Akolose 4:1; 1 Timoteyo 6:2.

Ukapolo Udzatha

Mofanana ndi nkhani zina zonse za m’Baibulo, nkhani ya ukapolo tiyenera kuimvetsa bwino. Tikaunika bwinobwino zimene Baibulo limanena, timaona kuti Mulungu amadana ndi zoti anthu azizunza anthu anzawo.

Timaonanso kuti ukapolo umene unkachitika m’nthawi ya Aisiraeli unali wosiyana ndi ukapolo umene anthu ambiri amaganiza, chifukwa nthawi imeneyo akapolo sankachitiridwa nkhanza. Ndipo Baibulo limasonyeza kuti nthawi ikadzakwana, Mulungu adzathetsa ukapolo wamtundu uliwonse. Pa nthawi imeneyo, anthu onse adzakhala pa ufulu weniweni.—Yesaya 65:21, 22.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi Baibulo limalimbikitsa kuti akapolo azichitiridwa nkhanza?—Levitiko 25:39, 40.

● Kodi Akhristu analangizidwa kuti azichitira zotani akapolo awo?—Akolose 4:1.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

Mulungu amadana ndi zoti anthu azizunza anthu anzawo

[Mawu a Chithunzi patsamba 29]

© G.M.B. Akash/Panos Pictures