Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

 Zochitika Padzikoli

Apolisi ku China alimbikitsa ntchito yogwira mbava zimene zimaba anthu. Atagwira ntchitoyi kwa chaka chimodzi ndi theka, “apolisiwa apulumutsa azimayi okwana 10,621 komanso ana okwana 5,896 omwe anabedwa.” Pa nthawiyi apolisi anagwira anthu okwana 15,673 omwe amawaganizira kuti ndi amene amaba anthu.—CHINA DAILY, CHINA.

“Zaka ziwiri zapitazi aphunzitsi oposa 1,000 ku Kenya achotsedwa ntchito chifukwa chogwiririra atsikana a pasukulu imene amaphunzitsa. . . . boma linakhazikitsa foni yaulere yoti anthu aziimba akaona zoterezi zikuchitika . . . ndipo anapeza kuti vutoli ndi lalikulu kwambiri kuposa mmene ankaganizira poyamba.”—DAILY NATION, KENYA.

Kafukufuku wina wasonyeza kuti, anthu 75 pa 100 aliwonse amene amagwiritsa ntchito makina osintha khungu lawo kuti azioneka ngati apsa ndi dzuwa, amadwala khansa ya pakhungu. Anthu amene amagwiritsa ntchito makina amenewa kwa maola opitirira 50 ndi amene amakhala pa ngozi yodwala khansayi, mwina kuwirikiza katatu.—CANCER EPIDEMIOLOGY, BIOMARKERS & PREVENTION, U.S.A.

“Pa atsikana 100 aliwonse a ku Canada amene akuyembekezera kulowa m’banja, ndi atsikana 8 okha amene ananena kuti si bwino kugonana musanakwatirane,” ndipo “mabanja 74 pa 100 aliwonse, anayamba kukhalira limodzi asanakwatirane.”—WEDDINGBELLS, CANADA.

Madzi Oipa Akupha Anthu Ambiri

Malinga ndi lipoti la bungwe la United Nations, “anthu ambiri akumwalira chifukwa chomwa madzi oipa ndipo chiwerengero cha anthu amenewa n’chochuluka kwambiri kuposa cha amene amafa pa nkhondo kapena pa zinthu zina zachiwawa.” Bungweli linanena kuti tsiku lililonse zinthu zoipa zokwana matani 2 miliyoni zochokera ku mafakitale komanso ku zimbudzi, zikumatayidwa m’mitsinje ndi m’nyanja ndipo zoipa zimenezi zikuyambitsa matenda komanso zikuwononga chilengedwe. Akuti pa masekondi 20 aliwonse, mwana mmodzi wa zaka zosapitirira zisanu amamwalira chifukwa chakumwa madzi oipa. Achim Steiner, yemwe ndi mkulu wa nthambi ya bungwe la United Nations Loona za Chilengedwe, ananena kuti: “Ngati tikufuna kuti tikhale ndi moyo wathanzi, . . . tiyenera kuthandizana n’kupeza njira zabwino zotayira zinthu zoipa.”

Kuimba Kukuthandiza Anthu Odwala Sitiroko

Anthu ambiri amene anasiya kulankhula chifukwa cha sitiroko, aona kuti kuimba kukuwathandiza kuti ayambirenso kulankhula bwinobwino. Madokotala aubongo akulimbikitsa anthu odwala sitiroko kuti aziimba. Akumawauza kuti aziimba chilichonse chimene akuganiza kapena chimene akufuna kunena. Zimenezi zathandiza anthu ambiri odwala sitiroko kuti ayambirenso kulankhula bwinobwino. Magazini ya Wall Street inanena kuti pomatha milungu 15, “wodwala amakhala atasiya kuimba n’kuyamba kulankhula bwinobwino.”

“Ana Ambiri Masiku Ano Akumaonera M’kalasi”

Bungwe lina Loona za Maphunziro ku Canada, linanena kuti pakafukufuku wina yemwe anafunsa ana 20,000 a m’chaka choyamba kuyunivesite, ana 73 pa 100 alionse “ananena kuti anaonerapo kamodzi kapena kangapo pa nthawi imene anali kusekondale.” Yunivesite ina inanena kuti pakati pa chaka cha 2003 ndi 2006, chiwerengero cha ana obera mayeso chinawonjezereka ndi 81 peresenti. Dr. Paul Cappon, yemwe ndi pulezidenti wa bungweli, ananena kuti: “Kuchuluka kwa zipangizo zamakono monga Intaneti ndi zipangizo zina, kwachititsa kuti vuto loonera m’kalasi liwonjezeke.”