Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinapeza Chinthu Chamtengo Wapatali

Ndinapeza Chinthu Chamtengo Wapatali

 Ndinapeza Chinthu Chamtengo Wapatali

Yosimbidwa ndi Murat Ibatullin

Mu 1987, unduna wa zaumoyo m’dziko la Russia unanditumiza ku Uganda. Ndinasayinirana ndi boma kukagwira ntchito yaudokotala m’dzikoli kwa zaka zinayi. Koma ndinalibe cholinga chobwereranso ku Russia. Ndinkangofuna kuti ndikakazolowera ntchitoyi, ndidzapite kukagwira ntchito kumayiko monga Australia, Canada, ndi United States. Koma pofika m’chaka cha 1991, ndinasintha maganizo ndipo ndinabwereranso ku Russia. Dikirani ndikufotokozereni mmene zinakhalira.

NDINABADWA m’chaka cha 1953 mumzinda wa Kazan’, womwe ndi likulu la dziko la Tatarstan ku Russia. Makolo anga ndi a mtundu wa Chitata, ndipo anthu ambiri a mtundu umenewu ndi Asilamu. Ndimakumbukira kuti ndili mwana, ndinkaona agogo anga atagwada pansi n’kumapemphera kwa Allah. Ana awo, kuphatikizapo makolo anga, ankatithamangitsa m’nyumbamo kuti tisawasokoneze agogowo. Komabe makolo anga ankachita manyazi ndi zochita za agogowo chifukwa iwowo sankakonda zopemphera. Iwo anali achikomyunizimu ndipo sankakhulupirira kuti kuli Mulungu.

Ndili ndi zaka zinayi, ndinadwala poliyo. Umenewu unali mliri wa poliyo womaliza ku Soviet Union. Ndikamaganizira za kale langa, chomwe chimabwera m’maganizo ndi maulendo akuchipatala basi. Ndimakumbukira kuti agogo anga aamuna ankandipempherera kuti ndichire. Ndinkafunitsitsa kukhala ndi thanzi labwino ngati ana ena, choncho ndinkasewera nawo mpira ndi masewera ena, ngakhale kuti ndinali wolemala mwendo umodzi.

Pamene ndinkakula, ndinayamba kulakalaka zodzakhala dokotala. Sindinkakonda zopemphera, koma sikuti ndinkatsutsa zoti kuli Mulungu. Kungoti sindinkaganizako za Mulungu. Pa nthawi imeneyi, sindinkagwirizana ndi mfundo zachikomyunizimu ndipo nthawi zambiri ndinkakangana ndi bambo anga komanso bambo anga aang’ono. Bambo aang’onowa ankaphunzitsa filosofe ku yunivesite, ndipo bambo anga ankagwira ntchito m’gulu la apolisi achinsinsi, lomwe linkadziwika kuti KGB. Nditamaliza maphunziro audokotala, ndinali ndi cholinga chokhala dokotala waluso kwambiri wochita opaleshoni ya ubongo  komanso ndinali ndi cholinga chosamukira ku dziko lina.

Kufunafuna Moyo Wabwino

Kenako ndinachita maphunziro okhudza khansa ya mu ubongo ndipo ndinamaliza maphunzirowa mu 1984. Mu 1987, boma linanditumiza ku Uganda kukagwira ntchito kuchipatala chachikulu cha Mulago. Ndinapita m’dziko lokongolali ndi mkazi wanga Dilbar komanso ana athu awiri, Rustem ndi Alisa. Pa nthawiyi n’kuti Rustem ali ndi zaka 7 ndipo Alisa ali ndi zaka 4. Ntchito yanga pachipatalachi sinali yophweka. Nthawi zina ndinkachita opaleshoni anthu a HIV. Komanso nthawi zambiri ndinkayenda m’zipatala zosiyanasiyana chifukwa m’dzikoli munali madokotala awiri okha ochita opaleshoni ya ubongo.

Tsiku lina ndili ndi mkazi wanga Dilbar, tinaona Baibulo la Chirasha pamalo ogulitsira mabuku. Tinagula Mabaibulo angapo n’cholinga choti enawo tiwatumizire anzathu ku Soviet Union, chifukwa pa nthawi imeneyi zinali zovuta kupeza Baibulo kwathuko. Tinawerenga machaputala angapo koma palibe chimene tinkamva. Kenako tinangosiya kuliwerenga.

Kwa zaka zitatu, tinalowa m’matchalitchi osiyanasiyana ku Uganda ndipo cholinga chathu chinali kudziwa zikhulupiriro za anthu akumeneko. Komanso ndinaganiza zophunzira Koran m’chinenero cha Chiarabu, moti ineyo ndi mwana wanga Rustem tinakalowa sukulu yophunzitsa chinenerochi. Patapita miyezi ingapo, tinkatha kulankhula Chiarabu bwinobwino.

Chapanthawi yomweyi, tinadziwana ndi mmishonale wina wophunzitsa Baibulo, Heinz Wertholz ndi mkazi wake Marianne, yemwenso anali mmishonale. Heinz anali wa ku Germany ndipo Marianne anali wa ku Austria. Tsiku loyamba limene tinakumana nawo sitinakambirane chilichonse chokhudza chipembedzo. Tinangocheza nawo ngati azungu anzathu basi amene takumana nawo ku Africa. Titawafunsa kuti atiuze chimene anabwerera ku Uganda, anafotokoza kuti anali amishonale a Mboni za Yehova ndipo anabwera kudzaphunzitsa anthu Baibulo.

Pa nthawiyi ndinakumbukira kuti pamene ndinkaphunzira filosofe payunivesite inayake ku Russia, ndinaphunzitsidwa kuti Mboni za Yehova ndi kagulu kachipembedzo komwe anthu ake amapha ana awo ndi kumwa magazi a anawo. Ndinauza Heinz ndi Marianne zimenezi chifukwa sindinkakhulupirira kuti iwo angamagwirizane ndi nkhanza zoterezi. Iwo anatipatsa kabuku kakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi ndipo tinawerenga machaputala ambiri a bukuli m’maola ochepa chabe. Nditamufunsa mkazi wanga kuti akumva bwanji, anandiuza kuti akusangalala ndi zomwe akuwerengazo ndiponso kuti zamukhudza mtima kwambiri. Ndinamuuza kuti inenso ndikumva chimodzimodzi.

Zimenezi zinachititsa kuti tikhale ndi chidwi chodzachezanso ndi Heinz ndiponso Marianne. Titakumana nawonso tinakambirana nkhani zambiri. Zimene tinakambirana zokhudza Baibulo zinatikhudza mtima kwambiri. Tinayamba kukambirana zimene tinkaphunzirazo ndi anzathu ena. Ena mwa anthuwa anali kazembe wa dziko la Russia, nthumwi za dziko la Russia ndi mayiko ena, komanso mkulu woimira dziko la Vatican. Mkuluyu anatidabwitsa kwambiri chifukwa ankanena kuti Chipangano Chakale ndi “nthano chabe.”

Kubwerera Kwathu ku Russia

Patatsala mwezi umodzi kuti tibwerere ku Russia mu 1991, ine ndi Dilbar tinaganiza zokhala Mboni za Yehova. Tinaganiza kuti tikakangofika ku Kazan’, tikapitiriza kusonkhana ndi Mboni za Yehova. Koma tinakhumudwa kwambiri kuti kwa miyezi itatu tinalephera kupeza Nyumba ya Ufumu komanso sitinapeze ngakhale wa Mboni mmodzi. Choncho tinaganiza zoyamba kulalikira nyumba ndi nyumba monga mmene Mboni  za Yehova padziko lonse lapansi zimachitira, ngakhale kuti tinkalalikira tokha. N’kupita kwa nthawi tinkaphunzitsa Baibulo anthu angapo, kuphatikizapo mayi wina amene kenako anakhala wa Mboni za Yehova.

Tsiku lina kunyumba kwathu kunabwera munthu wina wachikulire wa Mboni. Akuti iye anadziwa kumene timakhala kudzera kwa Mboni za ku Uganda. Kenako anthu okwana 15 tinayamba kusonkhana m’kachipinda kena kakang’ono. Tinkachezabe ndi Heinz ndi Marianne ndipo nthawi ina anabwera kudzationa ku Kazan’. Nafenso tinapita kukacheza nawo ku Bulgaria, dziko limene anatumizidwa atachoka ku Uganda. Ndipo akutumikirabe m’dziko limeneli mpaka pano.

Anthu Ambiri Kwathu Akulabadira Choonadi

Nthawi zambiri ndikapeza mpata, ndinkakambirana ndi madokotala anzanga m’zipatala zosiyanasiyana za choonadi cha m’Baibulo. Anthu ambiri amene ndinawalalikira, kuphatikizapo madokotala anzanga, panopa ndi Mboni za Yehova. Mu 1992, titangofika kumene ku Kazan’, Mboni za Yehova zinafika 45 ndipo chaka chotsatira zinalipo zoposa 100. Masiku ano ku Kazan’ kuli mipingo ya Mboni za Yehova yokwana 7, isanu ndi ya chilankhulo cha Chirasha, umodzi ndi wa chilankhulo cha Chitata ndipo winawo ndi wa chilankhulo cha manja. Komanso kuli magulu a anthu olankhula Chingelezi ndi Chiameniya.

Mu 1993 ndinapita ku msonkhano wa madokotala mu mzinda wa New York ndipo ndinali ndi mwayi wokaona likulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn. Kumeneko ndinakumana ndi Lloyd Barry, yemwe ankayang’anira ntchito ya Mboni za Yehova yolalikira padziko lonse. Ngakhale kuti anali ndi zochita zambiri, iye anapatula nthawi yocheza nane.

Tinakambirana kuti pakufunika kuyamba kumasulira mabuku athu m’chilankhulo cha Chitata. Patapita zaka zingapo, panakhazikitsidwa gulu lomasulira mabuku a Chitata. Tinasangalala kwambiri kuti kenako tinayamba kulandira magazini ya Nsanja ya Olonda, yomwe cholinga chake ndi kuthandiza anthu kuphunzira Baibulo, m’chilankhulo cha Chitata. Pasanapite nthawi yaitali, panakhazikitsidwa mpingo wa anthu olankhula Chitata.

Kuchita Opaleshoni Yosagwiritsa Ntchito Magazi

Ndimayesetsa kutsatira malamulo onse a Mulungu, kuphatikizapo lamulo lopezeka pa Machitidwe 15:20 limene limalimbikitsa atumiki a Mulungu ‘kupewa magazi.’ Vesi 29 limanena kuti atumiki a Mulungu ayenera “kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano, magazi, zopotola, ndi dama.”

Choncho Mboni za Yehova zikapita kuchipatala zimapempha madokotala kuti awapatse chithandizo popanda kuwaika magazi. Kwa nthawi ndithu ndinagwira ntchito ndi a Komiti Yolankhulana ndi Achipatala ya Mboni za Yehova ku Kazan’. * Mu 1997, mwana wina wa chaka chimodzi dzina lake Pavel, amene ankakhala ndi makolo ake mumzinda wa Novosibirsk, anadwala kwambiri ndipo anafunika kuchitidwa opaleshoni mwamsanga. Choncho mayi ake anatipempha kuti tiwathandize kupeza madokotala amene angachite opaleshoni yopanda magazi. Pa nthawi imeneyo, ku Russia kunali madokotala ochepa amene anali okonzeka kuchita opaleshoni imeneyo, komabe tinawauza kuti tiwathandiza kupeza madokotalawo.

Kenako tinapeza chipatala china ku Kazan’ chimene amachita opaleshoni ya mtima ndipo madokotala ake anavomera kuti amuchita opaleshoni Pavel popanda kugwiritsa ntchito magazi. Pa March 31, 1997, madokotala anamuchita opaleshoni ya mtima bwinobwino popanda kugwiritsa ntchito magazi. Pa April 3, nyuzipepala ina (Vechernyaya Kazan) inanena kuti: “Kamnyamatako  kakupeza bwino kwambiri ndipo sikakufunikiranso kumamwa mankhwala a matenda a mtima . . . Kwa nthawi yoyamba pambuyo pa miyezi 11 mayi ake a Pavel anayamba kusangalala.” Pasanapite nthawi yaitali, Pavel anachira ndipo anayamba kuyenda uku ndi uku m’chipatalamo.

Panopa Pavel ndi wathanzi ndipo akukula bwino. Amakonda kusewera mpira, kusambira ndi kuchita masewera ena. Tsopano iye ali sitandade 8 ndipo amapita kumpingo wa Mboni za Yehova wa mumzinda wa Novosibirsk limodzi ndi mayi ake. Pambuyo pa opaleshoni imeneyi, madokotala a pachipatalachi anachitanso opaleshoni anthu ambirimbiri a Mboni za Yehova omwe anali ndi vuto la mtima popanda kugwiritsa ntchito magazi. Ntchito zachipatala zapita patsogolo kwambiri ku Tatarstan ndipo nthawi zambiri akumapanga anthu opaleshoni popanda kugwiritsa ntchito magazi.

Ntchito Imene Ndikugwira Masiku Ano

Ine ndi mkazi wanga komanso anzathu ena a Mboni za Yehova, timagwira ntchito pachipatala chinachake. Pachipatalachi timagwiritsa ntchito njira zotsogola kwambiri pochiritsa odwala matenda a ubongo ndi mtima. Timachita anthu maopaleshoni osiyanasiyana popanda kugwiritsa ntchito magazi. Ndimagwira ntchito ngati dokotala wounika ubongo ndipo ndikupitirizabe kuwonjezera luso langa lochita opaleshoni yaubongo popanda kugwiritsa ntchito magazi. Ndimaphunzitsanso payunivesite yaudokotala ku Kazan’ m’dipatimenti yoona za ubongo. Ndimaphunzitsa ana a sukulu ndi madokotala ndipo ndimayesetsa kuwathandiza kudziwa ubwino wochita opaleshoni popanda kugwiritsa ntchito magazi. *

Mkazi wanga amagwira nane ntchito ngati woyeza anthu amene ali ndi mavuto osiyanasiyana m’thupi mwawo. Timasangalala ndi ntchito yathuyi chifukwa chakuti ndi yothandiza anthu. Koma ntchito imene imatisangalatsa kwambiri ndi kuphunzitsa anthu choonadi cha m’Baibulo. Timasangalala kwambiri kuuza anthu kuti posachedwapa, m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 23 Makomiti Olankhulana ndi Achipatala ndi magulu amene anakhazikitsidwa ndi Mboni za Yehova n’cholinga choti azithandiza odwala a Mboni kulankhulana ndi madokotala, makamaka pamene akufunika kupatsidwa magazi.

^ ndime 27 Padziko lonse lapansi madokotala ambiri akuona kuti chithandizo chosagwiritsa ntchito magazi ndi chabwino kwambiri. Anthu amene amaikidwa magazi amatha kutenga kachilombo ka HIV komanso kudwala matenda ena. Anthu enanso amati akalandira magazi, thupi lawo siligwirizana nawo.

[Chithunzi patsamba 12]

Ndikugwira ntchito yaudokotala ku Uganda

[Chithunzi patsamba 13]

Mu 1990, nthawi imene ine ndi mkazi wanga tinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova

[Chithunzi patsamba 14]

Ndili ndi Lloyd Barry mu 1993, nthawi imene ndinapita kukaona likulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn, mumzinda wa New York

[Chithunzi patsamba 15]

Pavel ndi mayi ake posachedwapa

[Chithunzi patsamba 15]

Ndikulalikira ndi mkazi wanga Dilbar