Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

 Zoti Banja Likambirane

Kodi N’chiyani Chikusoweka Pachithunzipa?

Werengani Genesis 13:5-17. Kenako yang’anani chithunzichi. Tchulani zinthu zimene zikusowekapo. Lembani mayankho anu m’munsimu. Malizitsani kujambula chithunzichi polumikiza timadonthoto, ndipo chikongoletseni ndi chekeni.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

[Chithunzi]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

KAMBIRANANI:

Kodi Loti ndi Abulahamu komanso abusa awo anasemphana maganizo pa nkhani yotani? Ngakhale kuti anali ndi ufulu wochita zimene akufuna chifukwa cha udindo wake, kodi Abulahamu anatani kuti akhazikitse mtendere?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Genesis 13:7-9.

Kodi Abulahamu anasungira Loti chakukhosi?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Genesis 14:12-16.

Kodi Abulahamu anadalitsidwa bwanji chifukwa cha makhalidwe ake abwino?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Genesis 13:14-17.

Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakonda mtendere?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Akorinto 13:4, 5; Yakobo 3:13-18.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Popanda kulankhula chilichonse, munthu mmodzi azichita zinthu zoyerekezera kuti ndi munthu winawake wa m’Baibulo. Ndipo ena onse anene kuti munthu akumuyerekezerayo ndi ndani.

 Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 5 ABULAHAMU

MAFUNSO

A. Kodi Abulahamu anali ndi zaka zingati pamene Isaki ankabadwa?

B. Kodi Yehova analonjeza Abulahamu chiyani?

C. Lembani mawu oyenerera m’mipatayi. Chifukwa cha chikhulupiriro ndi ntchito zake, Abulahamu anakhala ․․․․․.

[Tchati]

4026 B.C.E. 1 C.E. 98 C.E.

Kulengedwa Anakhala ndi moyo Baibulo linamalizidwa

kwa Adamu cha m’ma 1900 B.C.E. kulembedwa

[Mapu]

Anachoka ku Uri kupita ku Kanani

Uri

Harana

KANANI

ABULAHAMU

ANALI NDANI?

Munthu wokhulupirika amene anachoka mumzinda wolemera wa Uri n’kupita kumene Yehova anamuuza kuti apite, ngakhale kuti sankadziwa kumene ankapitako. (Aheberi 11:8-10) Nthawi zonse ankaphunzitsa ana ake kuti ‘aziyenda m’njira ya Yehova ndi kuchita chilungamo.’ (Genesis 18:19) Baibulo limanena kuti iye ndi ‘tate wa onse okhala ndi chikhulupiriro.’—Aroma 4:11.

MAYANKHO

A. Anali ndi zaka 100.—Genesis 21:5.

B. Kudzera mwa mbewu yake, mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso.—Genesis 22:16-18.

C. “Bwenzi la Yehova.”—Yakobo 2:21-24.

Anthu ndi Mayiko

3. Mayina athu ndi Rahela ndi Andrei. Tonsefe tili ndi zaka 7 ndipo timakhala m’dziko la Romania. Kodi mukudziwa kuti ku Romania kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 38,600; 68,300 kapena 83,600?

4. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko, ndipo kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi dziko la Romania.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba 11

 MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31

1. Ng’ombe.

2. Nkhosa.

3. 38,600.

4. C.