Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Akhristu Oona Amadedwa?

N’chifukwa Chiyani Akhristu Oona Amadedwa?

 Zimene Baibulo Limanena

N’chifukwa Chiyani Akhristu Oona Amadedwa?

“Anthu adzakuperekani ku chisautso ndipo adzakuphani. Mitundu yonse idzadana nanu chifukwa cha dzina langa.”—MATEYU 24:9.

YESU ananena mawu amenewa patatsala masiku ochepa kuti aphedwe. Ndiye tsiku loti aphedwa mawa, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.” (Yohane 15:20, 21) Koma kodi n’chifukwa chiyani anthu amazunza Akhristu omwe amayesetsa kumvera Yesu ndi kum’tsanzira? Zimenezi n’zovuta kumvetsa chifukwatu Yesu anali munthu wabwino kwambiri amene ankalimbikitsa anthu osauka komanso kupereka chiyembekezo kwa anthu oponderezedwa.

Baibulo limatchula zifukwa zimene zimachititsa kuti Akhristu azidedwa. Tikaunika bwinobwino zifukwa zimenezi, timamvetsa chifukwa chake masiku ano Akhristu amazunzidwa ngati mmene iye anazunzidwira.

Kusadziwa

Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Nthawi ikubwera pamene aliyense wakupha inu adzaganiza kuti wachita utumiki wopatulika kwa Mulungu. Koma adzachita zimenezi chifukwa sanadziwe Atate kapena ine.” (Yohane 16:2, 3) Kunena zoona, anthu ambiri amene ankazunza Akhristu oona ankaona kuti akutumikira Mulungu amenenso Yesu ankamutumikira, kungoti iwo ankapusitsidwa ndi zipembedzo zonyenga komanso miyambo yachabechabe. Iwo analidi ‘odzipereka potumikira Mulungu, koma sankamudziwa molondola.’ (Aroma 10:2) Mmodzi mwa anthu amenewa anali Saulo wa ku Tariso, amene pambuyo pake anadzakhala mtumwi Paulo.

Saulo anali m’gulu la ndale komanso la Chiyuda la mphamvu kwambiri limene linkatsutsa Chikhristu, la Afarisi. Pambuyo pake iye ananena kuti: “Kale ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe. . . Ndinali wosadziwa ndi wopanda chikhulupiriro.” (1 Timoteyo 1:12, 13) Komabe, ataphunzira choonadi chokhudza Mulungu ndi Mwana wake, iye anasintha moyo wake nthawi yomweyo.

Masiku anonso kuli anthu ambirimbiri amene kale ankazunza Akhristu. Ndipo ena mwa anthu amenewa, ngati mmene zinalili ndi Saulo, ali m’gulu la anthu amene amazunzidwa. Komabe iwo sabwezera choipa mosinthana ndi choipa, chifukwa amatsatira malangizo a Yesu akuti: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.” (Mateyu 5:44) Mboni za Yehova zimayesetsa kutsatira mawu amenewa ndipo zimayembekeza kuti ena mwa anthu amene amawazunzawo adzasintha ngati mmene anasinthira Saulo.

Nsanje

Anthu ambiri amene anazunza Yesu anachita zimenezo chifukwa cha nsanje. Ndipotu bwanamkubwa wa Aroma, Pontiyo Pilato, “anadziwa kuti ansembe aakulu anamupereka [Yesu] chifukwa cha kaduka.” (Maliko 15:9, 10) Kodi n’chifukwa chiyani atsogoleri achipembedzo achiyuda ankamuchitira Yesu nsanje? Chifukwa chimodzi chinali chakuti Yesu ankakondedwa ndi anthu wamba, amene ankanyozedwa ndi atsogoleri a zipembedzo. Afarisi ankadandaula kuti: “Dziko lonse lakhamukira kwa iye.” (Yohane 12:19) Nthawi inanso anthu odana ndi Chikhristu ataona kuti anthu akumvetsera zimene ophunzira a Yesu ankalalikira, iwo “anachita nsanje” ndipo anayamba kuzunza Akhristuwo.—Machitidwe 13:45, 50.

Anthu ena ankanyansidwa akamaona atumiki a Mulungu ali ndi makhalidwe abwino. Mtumwi Petulo anauza Akhristu anzake kuti: “Chifukwa chakuti simukupitiriza kuthamanga nawo limodzi m’chithaphwi cha makhalidwe oipa, anthu a  m’dzikoli sakumvetsa, choncho amakunyozani.” (1 Petulo 4:4) Masiku anonso anthu ena amadana ndi Akhristu oona chifukwa cha makhalidwe awo abwino. Koma sikuti Akhristu oona amapewa makhalidwe oipa n’cholinga choti azidzionetsera kuti ndi apamwamba kapena olungama kwambiri. Chifukwatu kuchita zimenezo n’kosemphana ndi Chikhristu, chimene chimaphunzitsa kuti anthu onse ndi ochimwa, ofunika kuchitiridwa chifundo ndi Mulungu.—Aroma 3:23.

‘Sali Mbali ya Dziko’

Baibulo limati: “Musamakonde dziko kapena zinthu za m’dziko.” (1 Yohane 2:15) Kodi dziko limene mtumwi Yohane ankanena limatanthauza chiyani? Dziko limeneli limaimira anthu otalikirana ndi Mulungu komanso amene amagonjera Satana. Iye ndi “mulungu wa nthawi ino.”—2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19.

N’zomvetsa chisoni kuti anthu amene amakonda dziko komanso njira zake amazunza anthu amene amayesetsa kutsatira zimene Baibulo limaphunzitsa. Yesu anauza atumwi ake kuti: “Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake. Koma popeza simuli mbali ya dzikoli, koma ine ndinakusankhani kuchokera m’dziko, pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.”—Yohane 15:19.

N’zomvetsa chisoni kuti anthu amadana ndi atumiki a Yehova chifukwa chakuti iwo sakonda dziko la Satana lodzaza ndi chinyengo, kupanda chilungamo, ndiponso chiwawa. N’zoona kuti pali anthu ambiri a mtima wabwino amene amafuna kusintha dzikoli kuti likhale labwino kwambiri, koma sangathe kuchotsa wolamulira wa dzikoli. Ndi Yehova Mulungu yekha amene ali ndi mphamvu zochotsa Satana ndipo chiwonongeko chake chidzakhala choopsa ngati cha moto.—Chivumbulutso 20:10, 14.

Mfundo imeneyi ndi imodzi mwa mfundo za mtengo wapatali za ‘uthenga wabwino wa ufumu’ zimene Mboni za Yehova zimalalikira padziko lonse. (Mateyu 24:14) Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha, wolamulidwa ndi Khristu, umene udzabweretse mtendere padziko lapansi. (Mateyu 6:9, 10) Choncho, iwo adzapitiriza kulalikira za Ufumu umenewu, chifukwa amaona kuti kuyanjidwa ndi Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa kuyanjidwa ndi anthu.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● N’chifukwa chiyani Saulo wa ku Tariso ankazunza otsatira a Khristu?1 Timoteyo 1:12, 13.

● Kodi adani a Yesu ankamuda chifukwa chiyani?—Maliko 15:9, 10.

● Kodi Akhristu oona amaliona bwanji dzikoli?—1 Yohane 2:15.

[Chithunzi patsamba 21]

Mu 1945, Mboni za Yehova zinamenyedwa ndi gulu lachiwawa ku Quebec, m’dziko la Canada chifukwa cholalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu

[Mawu a Chithunzi]

Courtesy Canada Wide