Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ndine wolephera?

Kodi ndine wolephera?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi ndine wolephera?

“Ndikadziyerekezera ndi mnzanga winawake, ndinkaona kuti ndine wolephera. Zinkaoneka kuti iye sankavutika kuchita chinthu chilichonse. Zimenezi zinkandichititsa kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo vuto langa ndi chiyani?’ Maganizo amenewa ankandivutitsa kwambiri.”—Anatero Annette. *

KODI nthawi zina mumadziona kuti ndinu wolephera moti simungathe kuchita chinachake chaphindu? Kodi zinthu zina zimene anthu amanena zimakuchititsani kuti muzidziderera? Kodi mumaopa kuchita zinthu zinazake chifukwa chakuti m’mbuyomu munayamba mwayesapo n’kulephera? Ngati ndi choncho, kodi mungatani kuti musamangoganizira za kulephera kwanu?

Mungachite bwino kwambiri kupeza yankho la funso lomalizali chifukwa anthufe sitingathe kuchita zinthu zonse popanda kulakwitsa chinachake. (Aroma 3:23) Koma anthu amene zimawayendera bwino ndi amene sagonja akalephera kuchita chinachake. Iwo amadziwa chimene chawalepheretsa ndipo amayeseranso kachiwiri. Ndipo ulendo wachiwiriwu amakwanitsa kuchita zinthuzo. Ndiye tiyeni tione zimene mungachite pa zinthu zitatu izi: Maganizo ooperatu kuti simungakwanitse kuchita chinachake, kudziyerekezera ndi ena ndiponso kulephera kwenikweni.

KUOPERATU KUTI SIMUNGAKWANITSE. Mukuganiza kuti zinthu siziyenda bwino ngakhale pang’ono, ndipo simukufuna n’kuyesa komwe kuchita chinachake, chifukwa mukuona kuti simungakwanitse.

Dziwani pamene pali vuto. Chongani chonchi ✔ zinthu zomwe inuyo mumafuna mutazichita koma mumaona kuti simungazikwanitse ngakhale mutayesa bwanji.

◯ Kufotokoza molimba mtima zimene mumakhulupirira kwa anzanu akusukulu

◯ Kufunsira ntchito

◯ Kulankhula pagulu

◯ Kuchita nawo masewera enaake

◯ Kuphunzira kuimba ndi pakamwa kapena kugwiritsa ntchito chida choimbira

◯ Zina ․․․․․

Ganizirani bwinobwino. Onani zinthu zimene mwachonga, ndipo kenako ganizirani zimene zingachitike mutayesa kuchita zinthuzo. Ndiyeno yankhani mafunso awa:

‘Kodi ndikufuna zinthu zitayenda bwanji?’

․․․․․

‘Kodi ndikuopa kuti chichitike n’chiyani?’

․․․․․

Tsopano lembani chifukwa chimodzi chimene muyenera kuchitira chinthucho, ngakhale kuti mukuopa kuti mungalephere.

․․․․․

Chitsanzo cha m’Baibulo. Mose atatumidwa ndi Mulungu kuti akatsogolere mtundu wa Isiraeli, chimene anaganiza poyambirira chinali chakuti zinthu sizikayenda bwino. Iye anafunsa Mulungu kuti: “Bwanji ngati sakandikhulupirira ndi kumvera mawu anga?” Kenako anayamba kunena za mavuto ake kuti: “Ine sinditha kulankhula, kuyambira kalekale, . . . Pakuti ndimalankhula movutikira.” Ngakhale pamene Yehova anamulonjeza kuti amuthandiza, Mose anapempha kuti: “Chonde, tumizani wina aliyense amene mungam’tumize.” (Ekisodo 4:1, 10, 13) Koma pamapeto pake, Mose analola ntchito imene Mulungu anamupatsa, ndipo tikudziwa zimene zinachitika. Mothandizidwa ndi Mulungu, iye anatsogolera mtundu wa Isiraeli kwa zaka 40.

Zimene mungachite. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse.” (Mlaliki 9:10) Choncho, m’malo moopa kuti simungakwanitse kuchita zinazake, dziperekeni ndi mtima wanu wonse kuchita zinthuzo. Mungachite bwino kuganizira zimene munachita bwino ngakhale kuti poyamba munkaona kuti simungakwanitse. Ganizirani zimene munaphunzira pa zimene zinachitikazo. Ganizirani mmene zimenezi zingakuthandizireni kuthetsa mantha alionse amene muli nawo, omwe angakulepheretseni kuchita zinazake.

Zokuthandizani: Ngati zingatheke, pemphani makolo kapena munthu wina wachikulire kuti akuthandizeni kuchotsa mantha. *

KUDZIYEREKEZERA NDI ENA. Ngati munthu wina wachita bwino kwambiri zinthu zinazake, inuyo mungamadzione kuti ndinu wolephera.

Dziwani pamene pali vuto. Kodi mumadziyerekezera ndi ndani, ndipo kodi ndi zinthu zotani zimene munthuyo wachita bwino kwambiri zimene zikukupangitsani inuyo kudziona kuti ndinu wolephera?

․․․․․

Ganizirani bwinobwino. Kodi kuchita bwino kwa munthuyo ndi umboni wosonyezadi kuti inuyo ndi wolephera? Lembani m’munsimu zinthu zimene zangochitika kumene, monga mayeso a kusukulu, amene inuyo munachita bwino koma mnzanu wina anachita bwino kwambiri.

․․․․․

Tsopano lembani chifukwa chake munachita bwino kulemba nawo mayesowo.

․․․․․

Chitsanzo cha m’Baibulo. Kaini ‘anapsa mtima’ ataona kuti Yehova wasangalala kwambiri ndi nsembe ya m’bale wake Abele. Yehova anachenjeza Kaini chifukwa cha nsanje yake, koma ananenanso mawu osonyeza kuti Kaini akhoza kuchita zinthu zabwino ngati atafuna. Yehova anamufunsa kuti: “Ukasintha n’kuchita chabwino, sindikuyanja kodi?” *Genesis 4:6, 7.

Zimene mungachite. M’malo ‘moyambitsa mpikisano,’ ngakhale mumtima mwanu chabe, muzivomereza kuti anthu ena akhoza kuchita bwino kuposa inuyo. (Agalatiya 5:26; Aroma 12:15) Komabe muyeneranso kumaganizira zinthu zimene mumaposa anthu ena. Koma muzisamala kuti zimenezi zisamakuchititseni kuyamba kunyada. Baibulo limati: “Aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera ndi munthu wina.”Agalatiya 6:4.

KULEPHERA KWENIKWENI. Mukuganizira zinthu zimene munalephera m’mbuyomu ndipo mukuona kuti ngakhale mutayesetsa bwanji simungakwanitse.

Dziwani pamene pali vuto. Kodi ndi chinthu chiti pa zinthu zimene mwalephera kuchita bwino chimene chimakufoolani kwambiri?

․․․․

Ganizirani bwinobwino. Kodi chinthu chimenechi chikusonyezadi kuti ndinu munthu wolephera? Mwachitsanzo, ngati mwachita chinthu chinachake cholakwika, kodi zikutanthauza kuti simungathenso kuchita bwino zinthu? Kapena kodi zimenezi sizikungosonyeza kuti mukufunikira kuthandizidwa? Ngati mutagwa mukuchita masewera enaake, mungafune kuti munthu wina akuthandizeni kudzuka, si choncho? Bwanji osachitanso zomwezo ngati mutachita chinthu chinachake cholakwika? Lembani pansipa dzina la munthu amene mungafune kuti akuthandizeni pa vuto lanulo. *

․․․․

Chitsanzo cha m’Baibulo. Nthawi zina, mtumwi Paulo ankakhumudwa chifukwa cha zinthu zimene sankachita bwino. Iye analemba kuti: “Munthu wovutika ine!” (Aroma 7:24) Koma zikuoneka kuti Paulo sanalole kuti zinthu zimene ankalakwitsazo zimuchititse kuganiza kuti ndi wolephera. Iye analemba kuti: “Ndamenya nkhondo yabwino. Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake. Ndasunga chikhulupiriro.”—2 Timoteyo 4:7.

Zimene mungachite. M’malo momangoganizira zinthu zimene mumalakwitsa, muziganiziranso zinthu zimene mumachita bwino. Yehova amaganizira zimene mumachita bwino. Baibulo limati: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.”—Aheberi 6:10; Salimo 110:3.

Kumbukirani izi: Palibe munthu wangwiro. Munthu aliyense amalakwitsa chinachake. Ngati mutati musamagonje mukalephera zinazake, ndiye kuti mwaphunzira khalidwe labwino kwambiri limene lingadzakuthandizeni m’tsogolo. Lemba la Miyambo 24:16 limati: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.” N’zimene inuyo muyenera kuchita.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha mayina ena m’nkhaniyi.

^ ndime 23 Ngati mukufuna kudziwa zambiri, onani Galamukani! ya May 2010, tsamba 26 mpaka 28.

^ ndime 31 Kaini sanafune kumvera malangizo a Yehova. Zimene zinamuchitikira zikutiphunzitsa kuti si bwino kuchitira nsanje munthu wina ngati wachita bwino pa zinthu zinazake.—Afilipi 2:3.

^ ndime 36 Ngati Mkhristu wachita tchimo, ayenera kuuza akulu kuti amuthandize.—Yakobo 5:14, 16.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

“Mukamakonda kuchita zinthu zokhazo zimene sizikuvutani, osayesako kuchita zinthu zatsopano, ndiye kuti mukumanidwa zinazake.”

“Mungaphunzire pa zinthu zimene mumalakwitsa n’kuyamba kuchita bwino, kapena mungamangoganizira zimene mumalakwitsazo n’kumalephera kuchita zinthu zatsopano. Zimangodalira kuti mwasankha kuchita zotani.”

“Ndikadziwa kuti ndilephera chinachake, ndimangonena nthabwala n’kumaseka, m’malo moda nazo nkhawa kwambiri. Mukamayembekezera kuti muzichita bwino chilichonse, simungakhale wosangalala.”

[Zithunzi]

Andrea

Trenton

Naomi

[Bokosi patsamba 28]

FUNSANI MAKOLO ANU

Kodi muli wamng’ono ngati ineyo, ndi zinthu ziti zimene simunkachita bwino? N’chiyani chinakuthandizani kuti musamakhumudwe nazo kwambiri? Kodi panopa mumakhumudwa mukalephera kuchita zinthu zinazake?

․․․․․

[Chithunzi patsamba 28]

Munthu akagwa, amafunika kudzuka, ndipo nthawi zina angafunikire munthu wina kuti amuthandize