Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Milomo Yanu Ndi “Ziwiya Zamtengo Wapatali”?

Kodi Milomo Yanu Ndi “Ziwiya Zamtengo Wapatali”?

 Kodi Milomo Yanu Ndi “Ziwiya Zamtengo Wapatali”?

● Mfumu Solomo inalemba kuti: “Pali golide komanso miyala yamtengo wapatali ya korali yambirimbiri, koma milomo yodziwa zinthu ndiyo ziwiya zamtengo wapatali.” (Miyambo 20:15) Golide wakhala akuonedwa kuti ndi chinthu cha mtengo wapatali kuyambira kalekale, ndipo m’nthawi ya Solomo miyala ya korali inkaonedwanso kuti ndi yamtengo wapatali. Koma milomo yathu ikhoza kukhala yamtengo wapatali kuposa zinthu zimenezi. Motani? Osati chifukwa chakuti ndi yooneka bwino, koma chifukwa cha zimene timalankhula.

Milomo yamtengo wapatali imanena zinthu zabwino mwachikondi ndiponso mwachifundo. “Milomo yodziwa zinthu” imanena za choonadi chokhudza Mulungu chopezeka m’Baibulo. Buku lakale limeneli ndi nkhokwe ya nzeru ndi choonadi chokhudza Mlengi wathu komanso lili ndi malangizo abwino kwambiri omwe angatithandize pa moyo wathu.—Yohane 17:17.

Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amagwiritsa ntchito milomo yawo molakwika. Iwo amanena zinthu zabodza zokhudza Mulungu. Mwachitsanzo, ena amamuimba mlandu kuti ndiye amayambitsa mavuto komanso zinthu zopanda chilungamo zimene zimachitika padzikoli, zomwe kwenikweni ndi anthu amene amaziyambitsa. Pa nkhani imeneyi, lemba la Miyambo 19:3 limati: “Kupusa kwa munthu wochokera kufumbi n’kumene kumapotoza njira yake, choncho mtima wake umakwiyira Yehova.”

Anthu ena amanyozetsa milomo yawo chifukwa cholankhula zinthu zabodza komanso miseche. Lemba la Miyambo 26:23 limati: “Milomo yonena zabwino mwachiphamaso koma mumtima muli zoipa, ili ngati siliva wokutira phale.” Mofanana ndi siliva amene akutirira chinthu chachabechabe ngati phale, “milomo yonena zabwino mwachiphamaso” imatha kubisa ‘mtima woipa.’—Miyambo 26:24-26.

Koma Mulungu sangalephere kuona zinthu zoipa zimenezi. Iye amaona zimene zili mumtima mwathu. N’chifukwa chake Yesu Khristu anati: “Yeretsa mkati mwa kapu ndi mbale choyamba, kuti kunja kwakenso kukhale koyera.” (Mateyu 23:26) Zimene Yesu ananenazi ndi zoona. Ndipotu ngati titachotsa zinthu zoipa mumtima mwathu n’kudzazamo zinthu zauzimu, mawu amene timalankhula adzasonyeza zimenezo. Ndipo milomo yathu idzakhala “ziwiya zamtengo wapatali” pamaso pa Mulungu.

[Chithunzi patsamba 19]

Milomo ya anthu anzeru ndi “ziwiya zamtengo wapatali”