Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Kodi Zikusiyana Pati?

Kodi mungatchule zinthu zitatu zimene zikusiyana pakati pa chithunzi A ndi chithunzi B? Lembani mayankho anu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo malizitsani zithunzizi pozichekenira.

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Ekisodo 28:9-12, 33, 36, 37.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

4. Kodi chithunzi cholondola n’chiti, chimene chili kumanja kapena kumanzere?

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi mawu akuti “chiyero” amatanthauza chiyani? N’chifukwa chiyani anthu olambira Yehova ayenera kukhala oyera? Kodi mungasonyeze bwanji kuti mukuyesetsa kukhala oyera?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Akorinto 7:1.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Munthu aliyense m’banja mwanu afufuze zinthu zosiyanasiyana zokhudzana ndi udindo wa mkulu wa ansembe ku Isiraeli. Kenako mukumane pamodzi n’kukambirana zimene mwapeza. Mwachitsanzo, kodi ntchito zina za mkulu wa ansembe zinali zotani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Levitiko 9:7; Deuteronomo 17:9-11.

Kodi Yesu Khristu amasonyeza bwanji kuti ndiye Mkulu wa Ansembe wabwino kwambiri?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Aheberi 4:14-16; 7:26-28; 9:11-14.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 3 RUTE

MAFUNSO

A. Malizitsani mawu amene Rute ananena kwa Naomi: “Anthu a mtundu wanu adzakhala . . . ”

B. N’chifukwa chiyani Rute ali chitsanzo chabwino kwa anthu amene akusamalira anthu odwala ndi okalamba?

C. Lembani mawu amene akusowekapo. Rute anakwatiwa ndi ․․․․․ ndipo anakhala kholo la ․․․․․ ndi ․․․․․ .

[Tchati]

4026 B.C.E. 1 C.E. 98 C.E.

Kulengedwa kwa Adamu Anakhala ndi moyo Baibulo linamalizidwa

cha m’ma 1200 B.C.E. kulembedwa

[Mapu]

Anachoka ku Mowabu Kupita ku Betelehemu

MOWABU

Betelehemu

RUTE

ANALI NDANI?

Iye anali mkazi wamasiye wa ku Mowabu amene anathandiza kwambiri apongozi ake okalamba a Naomi. Rute analimba mtima kuchoka kwawo n’kupita ku Betelehemu chifukwa chakuti ankakonda kwambiri Naomi komanso ankafunitsitsa kulambira Yehova. Anthu ena anauza Naomi kuti: “Mpongozi wako . . . ndi woposa ana aamuna 7.”—Rute 4:14, 15.

MAYANKHO

A. . . . “anthu a mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.”—Rute 1:16.

B. Rute anasonyeza kuti anali wofunitsitsa kuvutikira ena komanso wolimbikira ntchito.—Rute 2:7, 10-12, 17; 3:11.

C. Boazi, Mfumu Davide, Yesu Khristu.—Mateyu 1:5, 6, 16.

Anthu ndi Mayiko

5. Dzina langa ndi Shaé. Ndimakhala ku Britain. Dzikoli lili pafupi ndi ku Ulaya. Kodi mukuganiza kuti ku Britain kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi zilipo pafupifupi 13,300, 133,000, kapena 333,000?

6. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ndimakhala? Jambulani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Britain.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magaziniyi. Fotokozani chimene chikuchitika pachithunzi chilichonse.

● Mayankho a mafunso a patsamba 30 ndi 31 ali patsamba 7

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31

1. Mawu a panduwira.

2. Miyala ya onekisi ya pamapewa.

3. Mabelu a m’munsi mwa chovala.

4. Chakumanzere.

5. 133,000.

6. B.