Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pali Zimene Mungachite Kuti Mukhale ndi Thanzi Labwino

Pali Zimene Mungachite Kuti Mukhale ndi Thanzi Labwino

Pali Zimene Mungachite Kuti Mukhale ndi Thanzi Labwino

RUSTAM, yemwe amakhala ku Russia, amatanganidwa kwambiri. Kale, iye anali ndi zizolowezi zoipa koma kenako anazindikira kuti akuwononga thanzi lake. Anasiya kusuta fodya komanso kumwa mowa mwauchidakwa. Komabe, iye ankakhala nthawi yaitali akugwira ntchito pa kompyuta ndipo chifukwa cha zimenezi, ankangokhala wotopa nthawi zonse.

Ngakhale kuti Rustam ankayamba ntchito 8 koloko m’mawa, nthawi zambiri iye ankakhala asanagalamukebe mpaka 10 koloko m’mawa. Komanso ankadwaladwala. Choncho, iye anasintha zinthu zina ndi zina pa moyo wake. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Iye anati: “Pa zaka 7 zapitazi, sindinajombepo kuntchito masiku oposa awiri pa chaka chifukwa cha kudwala. Masiku ano ndimamva bwino kwambiri. Ndimakhala wogalamuka nthawi zonse ndipo ndimasangalala ndi moyo.”

Ram ndi mkazi wake komanso ana awo awiri amakhala ku Nepal. Kudera kumene amakhala ndi kwauve kwambiri ndipo kuli ntchentche ndi udzudzu wambiri. Kale Ram ndi banja lake ankadwaladwala chifuwa komanso maso. Nawonso anasintha zinthu zina ndi zina ndipo panopa ali ndi thanzi labwino.

Muziyesetsa Kusamalira Thanzi Lanu

Kaya akhale olemera kapena osauka, anthu ambiri sadziwa kuti zimene amakonda kuchita zimakhudza thanzi lawo. Iwo amaganiza kuti kukhala ndi thanzi labwino kumangochitika mwamwayi, kapena kuti palibe chimene angachite kuti akhale ndi thanzi labwino. Maganizo amenewa ndi osathandiza ndipo amalepheretsa anthu ambiri kusamalira thanzi lawo ndiponso kuchita zambiri pa moyo wawo.

Zoona zake n’zakuti kaya ndinu olemera kapena osauka, pali zinthu zimene mungachite kuti musamalire thanzi lanu ndi la banja lanu. Kodi pali phindu lililonse lochitira zimenezi? Inde lilipo. Phindu lake ndi lakuti mukhoza kukhala ndi moyo wabwino komanso wautali.

Komanso zimene makolo amanena ndi kuchita zingathandize kwambiri ana awo kuti aphunzire kuchita zinthu zimene zingawathandize kukhala ndi thanzi labwino. Nthawi ndi ndalama zimene mungawononge pochita zimenezi n’zochepa poyerekezera ndi zimene mungawononge ngati mulibe thanzi labwino. Izi zili choncho chifukwa munthu akamadwala amavutika m’njira zosiyanasiyana, amawononga nthawi imene akanakhala akugwira ntchito, ndiponso amawononga ndalama zambiri kuchipatala. Pajatu amati, “Kupewa kuposa kuchiza.”

M’nkhani zotsatirazi, tiona mfundo zisanu zimene zinathandiza anthu awiri aja, Rustam ndi Ram, komanso anthu ena ambiri, kukhala ndi thanzi labwino. Mfundo zimenezi zingathandizenso inuyo.

[Chithunzi patsamba 3]

Rustam

[Chithunzi patsamba 3]

Ram ndi banja lake amamwa madzi aukhondo