Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndimasangalala Kuti Ndine M’busa

Ndimasangalala Kuti Ndine M’busa

Ndimasangalala Kuti Ndine M’busa

Yosimbidwa ndi Alymbek Bekmanov

Nditakwanitsa zaka zitatu, ndinayamba kuweta nkhosa ndipo ndinkakonda kwambiri kusamalira nkhosazi. Pamene ndimafika zaka 17 n’kuti ndili m’busa wodziwa kuweta nkhosa. Koma patapita nthawi ndinasintha n’kukhala m’busa wauzimu. Dikirani ndikufotokozereni chifukwa chake ndimasangalala ndi ntchitoyi.

N DINABADWA mu 1972 m’banja lalikulu la makolo a mtundu wa Kigizi. Tinkakhala m’mudzi wotchedwa Chyrpykty, pafupi ndi nyanja yokongola ya Issyk Kul. Alendo ambiri amene amabwera m’dziko la Kyrgyzstan amakonda kudzaona nyanjayi. Kale dziko la Kyrgyzstan linali m’gulu la mayiko amene ankadziwika kuti Soviet Union. Panopa ine ndi mkazi wanga, Gulmira, timakhala ku Bishkek, lomwe ndi likulu la dziko la Kyrgyzstan. Mzindawu uli pa mtunda wa makilomita 200 kuchokera kudera kumene ndinakulira.

M’busa ndi Nkhosa Zake

Ndimakumbukira kuti ndili mwana, nyengo yozizira ikangotha tinkapita ndi nkhosa kuphiri lalitali kukazidyetsa. Tinkakwera phiri lalitali mamita 3,000 ndipo tinkayenda masiku ambiri tisanafike. Abusa ena ankadzera njira yachidule n’cholinga choti akafike mwachangu kudera kumene kunali msipu wambiri. Koma njira imene ankadutsa inali m’mphepete mwa ziphedi ndi zigwembe ndipo nkhosa zikangosochera pang’ono zinkavulala kapena kufa kumene.

M’njira zimenezo munkakhala mimbulu imene inkaopseza ndi kugwira nkhosa. Nthawi zambiri mimbuluyo inkalekanitsa nkhosa zingapo pa gulu la nkhosa, n’kuzipha. Choncho amalume anga ankakonda kudzera njira imene inali yosaopsa kwambiri komanso yosavuta kuyendamo, ngakhale kuti munthu akadutsa njira imeneyi ankachedwerapo ndi tsiku limodzi kapena masiku angapo. Nthawi zina ndinkafuna kuyenda mofulumira koma amalume anga ankandibweza. Ankandiuza kuti: “Alymbek, usamangoganizira za iweyo. Uziganiziranso nkhosazi.”

Pamwamba pa phiri pankakhala pokongola kwambiri komanso pankakhala msipu wambiri. Tikafikapo tinkamanga makola oti nkhosazo zizigonamo usiku. Abusa ena ankadzuka mochedwa ndipo ankatulutsa nkhosa zawo mochedwa kwambiri, dzuwa litakwera kale. Nkhosazo zikamayamba kudya msipu, kunja kunkakhala kutatentha kale.

Nkhosa zawo zinkaima pamodzi zitaweramitsa mitu komanso zikupuma movutikira. Chifukwa chomva kutentha komanso kutopa, nkhosazi zinkalephera kudya mokwanira ndipo zinkakhala zofooka komanso zowonda. Koma amalume anga ankadzuka m’mawa kwambiri dzuwa lisanatuluke. Nthawi ikamakwana 4 koloko m’mawa ankakhala atadzuka kale. Dzuwa likamatuluka ankakhala atafika kale kumalo odyetsera nkhosa. Choncho nkhosazo zinkakhala ndi nthawi yokwanira yodya msipu kunja kusanayambe kutentha. Choncho panali mawu akuti: “Ngati ukufuna kudziwa kuti m’busa ndi wotani, yang’ana mmene nkhosa zake zikuonekera.”

Nthawi yabwino yoti m’busa afufuze ngati nkhosa zake zili ndi vuto linalake komanso nthawi yozisamalira, ndi pamene zikupuma. Vuto lalikulu limene nkhosa zathu zinkakumana nalo linali la ntchentche zimene zimaikira mazira pamchombo wa nkhosa. Mazirawa amachititsa kuti mchombowo utupe. Ngati m’busa satulukira vutolo mwachangu, nkhosazo zimamva ululu kwambiri ndipo nthawi zina zimachoka pagulu la anzake n’kupita kutchire kukafa. Tsiku lililonse tinkafufuza kuti tione ngati nkhosa zathu zili ndi mazirawo n’cholinga choti tizipatse mankhwala. Ngakhale kuti zimenezi zinkafuna khama komanso zinkatenga nthawi, phindu lake linali lakuti nkhosa zathu zinkakhala zathanzi komanso zosangalala.

Madzulo alionse tikachoka kubusa, tinkawerenga nkhosa zathu kuti titsimikizire kuti zonse zilipo. Zinkalowa m’kholamo zitatuzitatu kapena zinayizinayi podutsa pakakhomo kakang’ono. Ngakhale kuti nkhosa zathu zinachuluka kwambiri, ifeyo tinakhala akatswiri odziwa kuwerenga moti tinkatha kuwerenga nkhosa 800 m’mphindi 15 kapena 20 zokha. Kuti munthu afike potha kuchita zimenezi amafunika kuzolowera.

Tikazindikira kuti nkhosa ina yasowa, amalume anga ankatenga mfuti ndi ndodo n’kupita kukaifunafuna. Ankachita zimenezi ngakhale ngati kunja kukugwa mvula kapena kuli mdima. Iwo ankaitana nkhosayo mokuwa kwambiri. Mawu awo ankachititsa mantha nyama zakutchire. Koma nkhosa ikamva mawuwo, inkachita kuoneka kuti ikumva kuti ndi yotetezeka.

Nkhosa iliyonse tinkaipatsa dzina logwirizana ndi mmene inkaonekera kapena zochita zake. Pa gulu lililonse la nkhosa, sipankalephera kukhala nkhosa zinazake zofuntha, zomwe sizinkafuna kumvera m’busa wawo. Nthawi zina nkhosa zina zinkatsatira nkhosa zosamverazo. Choncho m’busa ankaphunzitsa ndiponso kulanga nkhosa zosamverazo. Mwachitsanzo, nkhosa yotero ankatha kuitsekera m’khola yokhayokha. Pakapita nthawi, nkhosa zoterozo zinkasintha n’kumamvera m’busa wawo. Nkhosa zimene zinkalephera kusintha, tinkangozipanga ndiwo basi.

Ndinakhala M’busa Wamtundu Wina

Mu 1989, ndinaphunzira karati ndipo ndinali waluso kwambiri. Chaka chotsatira ndinalembedwa ntchito yausilikali m’gulu la asilikali a dziko la Soviet Union. Ndikugwira ntchito ku Russia, anzanga amene ndinkachita nawo karati anapanga gulu la zigawenga. Nditabwerera kwathu ku Kyrgyzstan, anandinyengerera kuti ndikalowa gulu lawo, zinthu zizindiyendera bwino kwambiri. Koma pa nthawi yomweyi ndinadziwana ndi Mboni za Yehova.

Anthu a Mboniwo anandiyankha mafunso amene ankandivutitsa kuyambira ndili mwana, monga lakuti, N’chifukwa chiyani anthu amafa? Kuchokera pa zimene tinkakambirana, ndinamvetsa mfundo yakuti anthu amafa chifukwa cha tchimo la munthu woyamba, Adamu. (Aroma 5:12) Ndinaphunziranso kuchokera m’Baibulo kuti Yehova, Mulungu woona, anatumiza Mwana wake Yesu kuti adzatiwombole ndiponso kuti tikakhulupirira Yehova ndi Yesu, machimo athu angathe kuphimbidwa. Kenako tingadzakhale ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi, mogwirizana ndi cholinga chimene Mulungu anali nacho polenga anthu.—Salimo 37:11, 29; 83:18; Yohane 3:16, 36; 17:1-5; Chivumbulutso 21:3, 4.

Mayankho a m’Baibulo amene anthu a Mboniwo ankandipatsa anali omveka bwino moti ndinafika ponena kuti, “Choonadi koma chimenechi!” Sindinkafunanso kucheza ndi anzanga amakhalidwe oipa aja. Nthawi zingapo iwo ankandinyengerera kuti ndiyambirenso kucheza nawo. Koma ineyo ndinkafunitsitsa kuphunzira mfundo za m’Baibulo n’kumazitsatira. Choncho, sindinakopeke ndi zimene ankandilonjeza ndipo m’kupita kwa nthawi ndinakhala m’busa wauzimu wa nkhosa.

Chapanthawi yomweyi, mayi winawake wotchuka kwambiri m’dera lathu amene ankati amachiritsa anthu powapempherera, ankabwera kunyumba kwathu kudzacheza ndi mayi anga. Tsiku lina nditafika panyumba, mayiyo anayamba kuchita zamizimu n’kumati akulankhula ndi anthu akufa. Iye anandiuza kuti ineyo ndili ndi mphatso yapadera ndipo anandilimbikitsa kuti ndipite kumzikiti ndikalandire chithumwa, pondiyengerera kuti chithumwacho chindithandiza kwambiri. Ndinatsala pang’ono kukhulupirira zimene ankanena zoti ndikachita zimenezi ndilandira mphatso yochiritsa anthu odwala.

Tsiku lotsatira, ndinapita kwa a Mboni amene ankandiphunzitsa Baibulo aja ndipo ndinawafotokozera za mayiyo. Iwo anandiwerengera malemba a m’Baibulo osonyeza kuti Yehova amadana ndi zamizimu zamtundu uliwonse, chifukwa n’zokhudzana ndi ziwanda. (Deuteronomo 18:9-13) Kwa masiku angapo, ndinkalephera kugona usiku chifukwa ziwanda zinkandivutitsa. A Mboni za Yehova aja atandiphunzitsa mmene ndingapempherere mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova, ndinaleka kulota zoopsa. Ndinazindikira kuti ndapeza M’busa wabwino kwambiri, Yehova.

Ndinaphunziranso kuti Davide, yemwe analemba masalimo ambiri a m’Baibulo, nayenso ali mwana anali m’busa. Iye ankatchula Yehova kuti “M’busa wanga” ndipo ndinakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene iye ankanena zokhudza Yehova. (Salimo 23:1-6) Ndinkafunitsitsanso kutsanzira Yesu, Mwana wa Yehova, yemwe amatchedwa ‘m’busa wa nkhosa.’ (Aheberi 13:20) Pa msonkhano umene unachitikira ku Bishkek, chakumayambiriro kwa chaka cha 1993, ndinabatizidwa m’madzi posonyeza kudzipereka kwanga kwa Yehova.

Msonkhano Wofunika Kwambiri

Achibale anga ambiri komanso anthu amene tinayandikana nawo nyumba, anayamba kukumana pamodzi n’kumaphunzira Baibulo. Anthu okwana pafupifupi 70 a m’mudzi mwathu ankasonkhana pafupi ndi nyanja ya Issyk Kul. Wachibale wanga winanso amene anali mkulu wa pamudzi pathu analinso ndi chidwi chofuna kuphunzira Baibulo. Iye ananena kuti aitanitsa msonkhano waukulu n’cholinga choti adzafotokozere anthu za chikhulupiriro chathu chatsopanochi. Koma atsogoleri a zipembedzo zina anayamba kukopa anthu kuti azikana a Mboni akabwera kudzawalalikira. Iwo anagwirizana zoti adzatiukire pa msonkhano umenewu.

Pa tsiku la msonkhano uja, panafika anthu okwana pafupifupi 1,000 ndipo ena anali ochokera m’midzi ina itatu yapafupi. Panabwera a Mboni za Yehova angapo, ndipo mmodzi anayamba kufotokoza mfundo za m’Baibulo zimene timakhulupirira. Pasanathe mphindi zisanu, munthu wina anaimirira ndi kuyamba kufunsa mafunso ongofuna kusokoneza zinthu. Anthuwo anayamba kutinyoza ndi kutiopseza ndipo gululo linkafuna kuyambitsa chiwawa.

Kenako mkulu wanga wina, amene anali atangoyamba kumene kuphunzira Baibulo, anaimirira n’kuyamba kutiikira kumbuyo. Aliyense ankamuopa chifukwa anali wodziwa kumenya. Iye analimba mtima n’kuima pakati, mbali imodzi kunali anthu achiwawawo ndipo mbali inayo kunali a Mboniwo. Zimenezi zinachititsa kuti tichokepo bwinobwino popanda chiwawa chilichonse. Patapita zaka zingapo, ambiri amene anali pa msonkhano umenewu anakhala a Mboni za Yehova. Panopa, anthu oposa 50 pa anthu 1,000 a m’mudzi mwathu ndi a Mboni za Yehova.

Ndinakopeka ndi Mwana wa M’busa

Mu August 1993, ku Moscow, m’dziko la Russia, kunali msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova. Kutatsala miyezi yochepa kuti msonkhanowu uchitike, ndinadziwana ndi mtsikana wa Mboni wochokera m’mudzi wa anthu a mtundu wa Kigizi, dzina lake Gulmira. Makolo akenso ankaweta nkhosa. Mu 1988, pamene ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa ku Soviet Union, mayi ake a Gulmira anayamba kuphunzira Baibulo ndi munthu wina wa Mboni za Yehova, dzina lake Aksamy. Iye anakhala wa Mboni za Yehova chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1970, ndipo anali munthu woyamba wa mtundu wa Kigizi kukhala wa Mboni za Yehova m’derali.

Pasanapite nthawi, Gulmira anayambanso kuphunzitsidwa Baibulo ndi Aksamy pamodzi ndi mayi ake. Gulmira ndi mayi ake anabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova mu 1990. Gulmira ankakonda kwambiri zimene ankaphunzira ndipo pasanapite nthawi anayamba kuchita utumiki wa nthawi zonse wa upainiya.

Pa zaka ziwiri zotsatira, tinkaonana mwa apo ndi apo chifukwa panali mtunda wa makilomita 160 kuchokera kwawo kukafika kwathu. Mu March 1995, ndinaganiza zoti ndidziwane bwino ndi Gulmira, choncho tsiku lina m’mawa ndinapita kunyumba kwawo ndili ndi maganizo amenewa. Sindinasangalale kumva zoti tsiku lotsatira akupita kukatumikira pa ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Russia, yomwe inali pa mtunda wa makilomita 5,633 kuchokera kumene ndimakhala.

Apa n’kuti nditayamba ntchito yolalikira nthawi zonse ndiponso nditayamba kuphunzira Chirasha, chifukwa pa nthawiyi panalibe mabuku a m’chinenero chathu cha Chikigizi. Kwa zaka zitatu, ine ndi Gulmira tinkalemberana makalata ndipo tinakonza zoti tiziwerenga malemba ofanana a m’Baibulo n’cholinga choti tizikambirana zimene tawerengazo. Pa nthawiyi ndinkatumikira mu mpingo wa Chikigizi ku Balikchi. Umenewu unali mpingo woyamba wa Chikigizi m’derali.

Kutumikira Yehova ndi Mkazi Wanga Gulmira

Mu 1998, Gulmira anatenga tchuthi n’kubwera ku Kyrgyzstan ndipo tinakwatirana. Inenso ndinaitanidwa kuti ndizikatumikira pa nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Russia. Ndinasangalala kwambiri chifukwa ndinali nditayamba kale kuphunzira Chirasha. Patapita nthawi, ndinayamba kugwira ntchito limodzi ndi anthu amene ankamasulira mabuku onena za Baibulo a Chikigizi. Imeneyi sinali ntchito yophweka, choncho ndinapempha Yehova kuti andipatse nzeru komanso mtima wodekha. Koma popeza ndinkagwira ntchitoyi limodzi ndi Gulmira, iye anandithandiza kwambiri.

Mu 2004 gulu lathu lomasulira mabuku linasamukira ku Bishkek. Kumeneko ndinasankhidwa kuti ndikhale m’komiti yoyang’anira ntchito ya Mboni za Yehova ku Kyrgyzstan. Pa nthawiyi m’dzikoli munali mipingo 7 ya Chikigizi ndiponso mipingo yopitirira 30 ya Chirasha. Panopa muli mipingo yopitirira 20 ya Chikigizi ndi magulu ambirimbiri a Chikigizi. Anthu a m’mipingo ndiponso magulu amenewa amapanga pafupifupi 40 peresenti ya Mboni zonse za ku Kyrgyzstan, zomwe zilipo zokwana 4,800.

Ine ndi Gulmira tinaganiza zoyamba kuphunzira Chingelezi, chifukwa tinkaona kuti chingatithandize pa ntchito yathu yolalikira. Zimenezi zinachititsa kuti tiitanidwe ku likulu la Mboni za Yehova ku United States m’chaka cha 2008. Kumeneko ndinachita nawo maphunziro a sukulu imene imakonzedwera anthu amene akutsogolera ntchito yolalikira m’mayiko awo.

Panopa ine ndi Gulmira timaona kuti tili ndi luso lokwanira lotithandiza kuti tizisamalira anthu mwauzimu ku Kyrgyzstan. Zimene zakhala zikutichitikira pa moyo wathu zatithandiza kuona kuti Yehova ndi m’busadi wachikondi. Ineyo pandekha ndaona kukwaniritsidwa kwa salimo la m’Baibulo, limene limati: “Yehova ndi M’busa wanga. Sindidzasowa kanthu. Amandigoneka m’mabusa a msipu wambiri. Amandiyendetsa m’malo opumira a madzi ambiri. Amatsitsimula moyo wanga. Amanditsogolera m’tinjira tachilungamo chifukwa cha dzina lake.”—Salimo 23:1-3.

[Chithunzi patsamba 23]

Nkhosa zathu zikudya msipu

[Chithunzi patsamba 23]

Tinkawerenga nkhosa zathu madzulo alionse n’cholinga chotsimikizira kuti panalibe iliyonse yosowa

[Chithunzi patsamba 24]

Ndili ndi Gulmira posachedwapa