Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mavu Obowola Mtengo

Mavu Obowola Mtengo

Kodi Zinangochitika Zokha?

Mavu Obowola Mtengo

● Pali mavu enaake amene amabowola mitengo ya paini n’kuikiramo mazira. Zimene mavu amenewa amachita pobowola mitengoyo zachititsa chidwi asayansi moti apanga tizipangizo tabwino kwambiri tochitira opaleshoni ya mu ubongo.

Taganizirani izi: Mavuwa amabowola mitengo ya paini ndi kansonga ka mchira wake, umene umaoneka ngati chubu. Chakumapeto kwenikweni kwa mchirawo, kuli nthambi ziwiri ndipo nthambi iliyonse ili ndi mano oloza kumbuyo. Mavuwa akamabowola mtengo, mano a nthambi imodzi ya mchirawo amagwira mtengo pamene nthambi inayo imalowa pang’ono mkati mwa mtengowo. Kenako mano a nthambi imene inalowa mkati ija amagwira mtengowo kuti nthambi ina ija ilowenso mkati. Nthambizi zimasinthanasinthana mofulumira kwambiri pobowola mtengowo moti mavuwa amatha kubowola mosavuta bowo lakuya mamilimita 20 popanda kupinda kapena kuthyola nthambi za mchirazo.

Potengera mmene mavuwa amabowolera mitengo, asayansi apanga kachipangizo kamene panopa akukayeserera komwe akuganiza kuti kadzathandiza kwambiri popanga opaleshoni. Kunsonga kwa kachipangizoka kuli nthambi ziwiri zokhala ndi timano ting’onoting’ono, zimene zingathe kulowa mkati mwa ubongo mosavuta komanso popanda kuwononga kwambiri ubongowo. Kachipangizoka kadzakhala ndi chinthu china chatsopano chomwe zipangizo zimene zikugwiritsidwa ntchito panopa zilibe. Magazini ya New Scientist inati: “Mosiyana ndi zipangizo zomwe zilipo panopa, kachipangizoka kadzakhala kofewa moti kazidzatha kukhota pochita opaleshoni n’kudutsa m’njira yabwino kwambiri mu ubongo kuti kasawononge zinthu zina mu ubongomo.” Kachipangizo kameneka kadzathandizanso kuti anthu ochita opaleshoni asamacheke malo ambirimbiri akafuna kuchita opaleshoni malo ovuta kuwafikira mu ubongo.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti mavu amene takambiranawa azitha kubowola mtengo mwaukatswiri chonchi, kapena alipo amene anawapanga mwanjira imeneyi?

[Chithunzi patsamba 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Nthambi imodzi imalowa mkati mwa mtengo n’kumacheka, pamene nthambi inayo ikutuluka

Mtengo

Kusinthana kwa nthambi

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Wasp: David R. Lance, USDA APHIS PPQ, Bugwood.org; diagram: J. F. V. Vincent and M. J. King, (1996). The mechanism of drilling by wood wasp ovipositors. Biomimetics, 3: 187-201