Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kudzizunza Kungakuthandizeni Kuti Muyandikirane ndi Mulungu?

Kodi Kudzizunza Kungakuthandizeni Kuti Muyandikirane ndi Mulungu?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kudzizunza Kungakuthandizeni Kuti Muyandikirane ndi Mulungu?

ANTHU ambiri amavutika kumvetsa akamva zoti anthu ena amadzizunza n’cholinga chofuna kukondweretsa Mulungu. Komabe, anthu ena opemphera amaona kuti kudzizunza ndi umboni wakuti amaopa Mulungu. Iwo amasala kudya kwa nthawi yaitali, kudzimenyamenya, kapena kuvala malaya a ubweya woyabwa kwambiri. Mungaganize kuti zimenezi n’zachikale, koma dziwani kuti zikuchitika ndithu masiku ano. Malinga ndi zimene manyuzipepala ena anena posachedwapa, ngakhale atsogoleri ena achipembedzo otchuka kwambiri a masiku ano amadzimenyamenya popemphera.

Kodi n’chiyani chimachititsa anthu kuti azipemphera mwanjira imeneyi? Mneneri wa gulu lina lachikhristu anati: “Kulolera kuzunzika ndi njira imodzi yodzigwirizanitsira ndi Yesu Khristu komanso ndi mavuto amene iye analolera kukumana nawo kuti atiwombole ku machimo.” Popanda kuganizira zimene atsogoleri azipembedzo amanena, kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani imeneyi?

Muzikonda Thupi Lanu

Baibulo sililola kapena kulimbikitsa kuti anthu azidzizunza popemphera. M’malomwake, limalimbikitsa anthu oopa Mulungu kuti azikonda thupi lawo. Taonani zimene limanena zokhudza chikondi chimene mwamuna ndi mkazi wake ayenera kusonyezana. Poganizira mmene mwamuna amasamalira thupi lake, Baibulo limati: “Amuna akonde akazi awo monga matupi awo. . . . Palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda, mmenenso Khristu amachitira ndi mpingo.”—Aefeso 5:28, 29.

Kodi malangizo akuti mwamuna azikonda mkazi wake ngati thupi lake angakhale ndi tanthauzo lililonse ngati anthu amafunika kuti azizunza thupi lawo popemphera? N’zoonekeratu kuti anthu amene amayesetsa kutsatira Malemba amafunika kusamalira komanso kukonda matupi awo ndipo chikondi chimenechi ayeneranso kuchisonyeza kwa akazi awo.

M’Baibulo muli malemba ambiri amene amalimbikitsa anthu kuti azisamalira thupi lawo. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti kuchita masewera olimbitsa thupi n’kothandiza. (1 Timoteyo 4:8) Limafotokozanso kuti zakudya zina zimathandiza kuchiza matenda pamene zina zikhoza kuyambitsa matenda. (Miyambo 23:20, 21; 1 Timoteyo 5:23) Malemba amalimbikitsa anthu kuchita zinthu zimene zingawathandize kukhala ndi thanzi labwino n’cholinga choti azitha kugwira ntchito mwamphamvu. (Mlaliki 9:4) Ngati Baibulo limalimbikitsa anthu kusamalira thupi lawo mwanjira zimenezi, ndiye kodi zingakhale zomveka kuti liziwalimbikitsanso kuti azidzizunza?—2 Akorinto 7:1.

Kodi Akhristu Ayenera Kudzizunza Poyerekezera Mmene Yesu Anazunzikira?

Matchalitchi ena amalimbikitsa anthu awo kuti azidzizunza potengera mmene Yesu ndi otsatira ake anazunzikira. Koma masautso amene atumiki a Mulungu anawalemba m’Baibulo, sankakumana nawo mwadala. Pamene Akhristu omwe analemba Baibulo ankanena za kuvutika kwa Khristu, cholinga chawo chinali kulimbikitsa Akhristu anzawo kuti azipirira akamazunzidwa, osati kuti azidzizunza okha. Choncho anthu amene amadzizunza sakutsatira Yesu Khristu.

Mwachitsanzo: Tiyerekezere kuti mwaona mnzanu amene mumamulemekeza akunyozedwa komanso kumenyedwa ndi gulu linalake la anthu ankhanza. Ndiye mukuona kuti mnzanuyo akupirira modekha popanda kubwezera. Iye sakuwanyoza kapena kuwamenya. Ngati mutafuna kutengera chitsanzo cha mnzanuyo, kodi mungayambe kudzinyoza ndi kudzimenya nokha? Ayi. Kuchita zimenezi kungakhale kutengera zochita za anthu ankhanzawo, osati za mnzanuyo. Choyenera kuchita ngati mutakumana ndi mavuto ofanana ndi amenewa, ndi kupewa kubwezera.

Choncho, otsatira Khristu sayenera kudzizunza okha chifukwa kuchita zimenezi kuli ngati kutengera zochita za anthu ankhanza amene anazunza komanso kupha Yesu. (Yohane 5:18; 7:1, 25; 8:40; 11:53) M’malomwake, iwo akamazunzidwa ayenera kungopirira moleza mtima osabwezera, ngati mmene Yesu anachitira.—Yohane 15:20.

N’zosagwirizana ndi Malemba

Ngakhale Chikhristu chisanayambe, Malemba amene Ayuda ankayendera pa moyo wawo komanso polambira sankawalola kudzizunza mwanjira iliyonse. Mwachitsanzo, Chilamulo chinanena mosapita m’mbali kuti Ayuda sayenera kudzichekacheka. Zikuoneka kuti pa nthawi imeneyo mitundu ina inkakonda kuchita zimenezi. (Levitiko 19:28; Deuteronomo 14:1) Ngati Mulungu sankafuna kuti anthu azicheka thupi lawo, iye sangafunenso kuti azilikwapula. Chotero zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi n’zomveka bwino: Kudzizunza mwanjira ina iliyonse n’kosavomerezeka pamaso pa Mulungu.

Monga mmene katswiri wojambula zithunzi amafunira kuti anthu azisamalira zithunzi zake, Mlengi wathu Yehova Mulungu amafunanso kuti anthu azisamalira thupi limene iye analenga. (Salimo 139:14-16) Ndipotu kudzizunza sikulimbitsa ubwenzi wa munthu ndi Mulungu. M’malomwake kumasokoneza ubwenziwo ndiponso n’kosemphana ndi zimene timawerenga m’Mauthenga Abwino.

Mtumwi Paulo analemba mouziridwa za ziphunzitso zankhanza zangati zimenezi. Iye anati: “Ndithudi, zinthu zimenezo zimaonekera pa kulambira kochita kudzipangira, podzichepetsa mwachinyengo komanso pozunza thupi, ndipo zimaonekadi ngati zanzeru, koma n’zosathandiza kwa munthu polimbana ndi zilakolako za thupi.” (Akolose 2:20-23) Zoonadi, kudzizunza sikungathandize munthu kuti ayandikirane ndi Mulungu. Koma zimene Mulungu amafuna kuti olambira ake azichita n’zotsitsimula, zosavuta kutsatira komanso zosalemetsa.—Mateyu 11:28-30.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi Mulungu amaliona bwanji thupi lathu?—Salimo 139:13-16.

● Kodi kudzizunza kungakuthandizeni kugonjetsa zilakolako zoipa?—Akolose 2:20-23.

● Kodi kulambira koona n’kolemetsa komanso kwankhanza?—Mateyu 11:28-30.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi n’zomveka bwino: Kudzizunza mwanjira ina iliyonse n’kosavomerezeka pamaso pa Mulungu

[Chithunzi patsamba 10]

Munthu akuvutika kuyenda chokwawa kuti akalowe m’tchalitchi

[Mawu a Chithunzi]

© 2010 photolibrary.com