Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chitani Zinthu Zokuthandizani Kukhala ndi Thanzi Labwino

Chitani Zinthu Zokuthandizani Kukhala ndi Thanzi Labwino

Chitani Zinthu Zokuthandizani Kukhala ndi Thanzi Labwino

KODI mukumukumbukira Ram, yemwe tinamutchula m’nkhani yoyambirira ija? Mofanana ndi anthu ambiri padzikoli, iye sankadziwa kufunika kodya zakudya zoyenera komanso kuchita tsiku ndi tsiku zinthu zothandiza kuti akhale ndi thanzi labwino. Iye anati: “Nkhani yomwe inali mu Galamukani! ya May 8, 2002, yamutu wakuti ‘Chakudya Chopatsa Thanzi N’chosasoŵa,’ inandithandiza kudziwa kuti kudya zakudya zoyenera n’kofunika kwambiri.”

Ram ananenanso kuti: “Banja lathu linayesetsa kutsatira zimene tinaphunzira m’nkhani imeneyi. Pasanapite nthawi yaitali, tinaona kuti chitetezo cha thupi lathu cholimbana ndi matenda chinakula. Tisanayambe kusamala ndi zakudya, tinkadwaladwala chimfine, koma masiku ano sitidwaladwalanso. Tinaphunziranso njira zosavuta komanso zosawonongetsa ndalama zopezera madzi abwino akumwa, kuchokera m’nkhani yakuti, ‘Njira Zisanu ndi Imodzi Zosamalira Thanzi Lanu,’ yomwe inatuluka mu Galamukani! ya October 8, 2003.”

“Nkhani ina ya mu Galamukani! inandithandiza kuonetsetsa kuti banja langa lili ndi thanzi labwino. Nkhaniyi inali ya mutu wakuti, ‘Sopo ndi “Katemera Amene Mungadzipatse Nokha,”’ ndipo inatuluka mu Galamukani! ya December 8, 2003. Titangoiwerenga, tinayamba kutsatira mfundo zimene zinali m’nkhani imeneyi. Panopa sitidwalanso maso ngati mmene tinkachitira kale.

“M’dera lomwe timakhala, udzudzu ndi ntchentche zimangoti ng’waa! paliponse, koma anthu siziwakhudza n’komwe. Banja lathu litaonera vidiyo yakuti, The Bible—Its Power in Your Life, * linaphunzira kuti tiyenera kupewa tizilombo timeneti. Kutsatira zimenezi kumatithandizanso kukhala ndi thanzi labwino.”

Musataye mtima Ngati pali zinthu zimene mukuyenera kusintha, mungachite bwino kuyamba pang’onopang’ono ndipo muyenera kupewa kudziikira zolinga zomwe simungazikwanitse. Mwachitsanzo, mungayambe n’kuchepetsa zakudya zonenepetsa, m’malo mongozisiyiratu. Mungayesenso kugona nthawi yabwinopo ndiponso kuchitako pang’ono masewera olimbitsa thupi. Ndi bwino kuchita kenakake m’malo mosachitiratu chilichonse. Nthawi zambiri zimatenga nthawi ndithu, mwina milungu kapena miyezi ingapo, kuti muzolowere kuchita zinthu zatsopano zokuthandizani. Pa nthawi imeneyi ngati mukuona kuti khama lanulo silikukupindulitsani m’njira iliyonse, musataye mtima. Ngati mutapitirizabe ngakhale patakhala zinthu zina zokubwezani m’mbuyo, m’kupita kwa nthawi mudzaona kuti mwayamba kukhala ndi thanzi labwino.

M’dziko lovutali, n’zosatheka kukhala ndi thanzi labwino kwambiri. Nthawi zina timadwala chifukwa chakuti matupi athu ndi opanda ungwiro, osati chifukwa choti tinanyalanyaza zinthu zinazake. Choncho musalole kuti nkhawa yokhudza thanzi lanu kapena zinthu zina izikuvutitsani kwambiri. Yesu anafunsa kuti: “Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?” (Luka 12:25) M’malomwake, muzingoyesetsa kupewa zinthu zimene zingakudulireni moyo kapena kuupangitsa kukhala wosasangalatsa. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti mukhale ndi thanzi labwino mogwirizana ndi zimene mungakwanitse panopa, podikira dziko latsopano la Mulungu. Pa nthawi imeneyo, “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.