Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

 Zochitika Padzikoli

Pa anthu a ku Germany osakwana zaka 40, anthu osakwana 25 pa 100 alionse ndi amene amaona kuti kupemphera ndi ana awo tsiku lililonse n’kofunika, ndipo pakati pa anthu amene amapita kutchalitchi, anthu anayi okha pa anthu 10 alionse ndi amene amaona kuti kupemphera ndi ana n’kofunika.—APOTHEKEN UMSCHAU, GERMANY.

Mwamuna wina yemwe anali ndi matenda a mtima ochita kubadwa nawo, anapereka umuna wake kuchipatala. Pa nthawiyo matendawo anali asanadziwike, ndipo iye anapatsira matendawa kwa ana 9 pa ana 24 amene akudziwika kuti ndi ake. Pa ana amenewa, mmodzi anamwalira ndi matenda a mtima ali ndi zaka ziwiri.—JAMA, U.S.A.

“Anthu oposa theka la anthu onse a ku Russia amakhulupirira kuti katangale ndi chinthu chosapeweka ndipo sadzatha.”—RIA NOVOSTI, RUSSIA.

Ali ndi Anzawo Apamtima Ochepa Kwambiri

Nyuzipepala ya Daily Telegraph ya ku London inanena kuti “anthu ambiri a ku Britain amakhala ndi anzawo apamtima atatu okha amene angawadalire.” Pa kafukufuku wina, anapeza kuti “munthu mmodzi amakhala ndi anzake 36 pa moyo wake, omwe kenako amadzapezeka kuti sakucheza nawonso.” Zina mwa zifukwa zimene zimachititsa zimenezi ndi monga “kukhala ndi moyo wotanganidwa kwambiri, kapena ‘kungopezeka kuti asiya kuchezerana.’” Anthu 43 pa anthu 100 alionse amene anafunsidwa mafunso pa kafukufukuyu anati anasiya kucheza ndi anzawo chifukwa chakuti “anayambana nawo . . . ndipo safunanso kuwalankhula.” Pafupifupi munthu mmodzi pa anthu asanu alionse amauza mavuto ake mnzake wa kuntchito, chifukwa “alibenso wina aliyense woti angamuuze za kukhosi kwake.” Munthu wina woimira anthu amene anachita kafukufukuyo anati: “Kuti anthu afike pokukhulupirira komanso kukudalira, pamafunika kuyesetsa kwambiri.”

Maboti Ozembetsera Mankhwala Osokoneza Bongo

Anthu ogulitsa mankhwala osokoneza bongo a ku Colombia, masiku ano akugwiritsa ntchito njira zotsogola kwambiri pofuna kulowetsa mankhwalawa ku Central America, ku Mexico, ndi ku United States. Kuyambira mu 1993, akuluakulu a boma la Colombia agwira maboti oposa 42 ozembetsera mankhwala osokoneza bongo. Iwo atulukiranso malo angapo kumene amapangirako maboti amenewa. Ngakhale kuti maboti amenewa, omwe amayendera dizilo, sangathe kuyenda pansi pa madzi, amakhala ovuta kwambiri kuwaona pa makina ounikira zinthu zimene zili panyanja. Ena mwa mabotiwa akhoza kuyenda ulendo wokwana makilomita 3,200, ndipo amatha kunyamula mankhwala osokoneza bongo a mtundu wa kokeni okwana matani 6 mpaka 10. Mwina pamafunika ndalama zokwana madola 1 miliyoni kuti apange boti limodzi.

Ubwino Wodyera Pamodzi

Posachedwapa achinyamata a ku Finland azaka za pakati pa 14 ndi 16 anafunsidwapo mafunso pa kafukufuku winawake wofuna kudziwa kuti ndi achinyamata angati amene amadyera pamodzi ndi mabanja awo. Pa achinyamata amene anafunsidwawo, osakwana theka ndi amene amadya chakudya pamodzi ndi mabanja awo. Pa kafukufukuyo anapeza kuti m’makomo ambiri saphika n’komwe chakudya chilichonse. Komabe, achinyamata amafuna kwambiri atamadya chakudya pamodzi ndi mabanja awo nthawi zonse chifukwa nthawi yachakudya imakhala nthawi yopuma komanso yosangalatsa. Achinyamatawa atafunsidwa zimene amafuna kuti makolo awo azichita, ambiri mwa iwo anati amafuna “kudya zakudya zotentha, kudyera pamodzi ndi mabanja awo, ndiponso kukhala ndi winawake woti azimvetsera mwatcheru iwo akamalankhula,” inatero nyuzipepala ya Helsingin Sanomat. Kudya chakudya pamodzi ndi anthu a m’banja mwawo kumathandiza kwambiri achinyamata kuti akhale anthu oganiza bwino. Malinga ndi nkhani ya m’nyuzipepala ija, “achinyamata amene amadyera pamodzi ndi mabanja awo, nthawi zambiri amakhoza bwino kusukulu, sasuta fodya, samwa mowa, sasuta chamba, ndipo nthawi zambiri sadwala matenda ovutika maganizo.”