Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndakhala ndi Moyo Wopindulitsa Kwambiri

Ndakhala ndi Moyo Wopindulitsa Kwambiri

 Ndakhala ndi Moyo Wopindulitsa Kwambiri

Yosimbidwa ndi Herawati Neuhardt

Ndinabadwira mumzinda wa Cirebon, m’dziko la Indonesia. Mzinda umenewu umatchuka chifukwa cha nsalu zinazake zokongola zimene zimapangidwa ndi anthu akumeneko. Nsaluzi zimakhala za mitundu yosiyanasiyana yowala kwambiri ndipo amajambulapo maluwa okongola. Moyo wanga monga mmishonale ndingauyerekezere ndi nsalu zimenezi, chifukwa ndakhala ndi moyo wosangalatsa kwambiri polalikira kwa anthu azikhalidwe zosiyanasiyana a kum’mwera chakum’mawa kwa Asia ndiponso kum’mwera kwa nyanja ya Pacific. Dikirani ndikufotokozereni zambiri.

M’CHAKA cha 1962, pamene ndinali ndi zaka 10, mayi anga anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Patapita nthawi, mayi ndi bambo anga, omwe ndi Matchaina obadwira ku Indonesia, limodzi ndi ana awo asanu, kuphatikizapo ineyo, tinakhala Mboni za Yehova.

Amishonale ndiponso oyang’anira oyendayenda akabwera kudzalimbikitsa mpingo wathu mwauzimu, nthawi zambiri ankakhala kunyumba kwathu. Chitsanzo chawo chabwino komanso zinthu zabwino zimene ankanena zinandilimbikitsa kwambiri. Nditakwanitsa zaka 19, ndinayamba ntchito yolalikira nthawi zonse. Chaka chotsatira, ndinakwatiwa ndi Josef Neuhardt, mmishonale wochokera ku Germany amene anabwera ku Indonesia m’chaka cha 1968. Titangokwatirana, tinasamukira ku Sumatra, chomwe ndi chilumba chachiwiri pa zilumba zikuluzikulu ku Indonesia. Ku Indonesia kuli zilumba zoposa 17,000. Titafika kumeneko ndinayamba kuyenda limodzi ndi mwamuna wanga pa ntchito yake monga woyang’anira woyendayenda, ndipo tinkayendera mipingo yosiyanasiyana ya Mboni za Yehova.

Kulalikira ku Sumatra

Tinkayendera dera lalikulu kwambiri kuyambira kumzinda wa Padang, womwe unali kumadzulo kwa Sumatra. Mzindawu unali wotentha komanso unali ndi anthu ambirimbiri. Dera lomwe tinkayendera linkafika mpaka kunyanja yaikulu komanso yokongola kwambiri ya Toba. Nyanjayi ili m’dera lamapiri la kumpoto kwa Sumatra, ndipo inapangika chifukwa cha kuphulika kwa nthaka. Kenako tinayambanso kuyendera dera lakum’mwera kwa chilumbachi. Nthawi zonse tinkangokhalira kuyenda, ndipo tinkagwiritsa ntchito galimoto yathu yakutha komanso yakale kwambiri ya mtundu wa Volkswagen Beetle. Tinkayenda m’misewu yokumbikakumbika ya m’nkhalango, kuwoloka milatho yosalimba yopangidwa ndi mitengo ya kokonati, ndiponso kuyenda m’misewu yokhotakhota ya m’mapiri akuluakulu. Nthawi zina ena mwa mapiri amenewa ankaphulika n’kumatulutsa ziphalaphala za pansi pa nthaka. Usiku tinkagona pansi m’nyumba zakumudzi zopanda magetsi, madzi kapena zimbudzi zogejemula. Tikafuna kusamba kapena kuchapa, tinkapita kunyanja kapena kumtsinje. Kunena zoona, tinkakhala moyo wosalira zambiri. Tinkakondanso kwambiri  anthu amene tinkakumana nawo m’derali. Anthuwo ankatilandira bwino kwambiri m’makomo mwawo, ankatipatsa chakudya ndipo ambiri anali ndi chidwi chophunzira Baibulo.

Ku Padang, anthu a mtundu wa Minangkabau, omwe ambiri anali a chipembedzo cha Chisilamu, ankadabwa kwambiri komanso ankasangalala kwambiri tikawawerengera zimene Baibulo limanena zakuti Mulungu ndi mmodzi, osati Utatu ngati mmene matchalitchi ambiri amaphunzitsira. (Deuteronomo 6:4) Anthu ambiri ankakonda kulandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndipo anthu ena anapita patsogolo kwambiri mwauzimu. Ambiri mwa anthu a mtundu wa Batak, omwe amakhala pafupi ndi nyanja ya Toba, ali m’zipembedzo zachikhristu ndipo amadziwa dzina la Mulungu lakuti Yehova, chifukwa dzinali limapezeka m’Baibulo lachibataki. (Salimo 83:18) Komabe, anthuwa ankafunika kuthandizidwa kuti amudziwe bwinobwino Mulungu, komanso adziwe zimene wakonzera anthu m’tsogolo. Ambiri anayamba kuphunzira Baibulo n’kukhala alaliki achangu a uthenga wa m’Baibulo.

Kulalikira kwa Anthu a ku Java

Mu 1973, ine ndi Josef tinatumizidwa kuchilumba cha Java. Chilumbachi chili ndi anthu oposa 80 miliyoni ndipo kukula kwake m’pafupifupi theka la dziko la Britain. * Tinkalalikira uthenga wabwino kwa Matchaina ndiponso anthu a mtundu wa Java ndi Sunda.

Chifukwa chakuti makolo anga anali Matchaina komanso ndinakulira ku Indonesia, ndinkalankhula zinenero zambiri, kuphatikizapo, Chijava, Chisunda, Chiindonesia, komanso Chingelezi. Chifukwa chodziwa zinenero zambiri, ndinkatha kukambirana nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo ndi anthu ambiri m’zinenero zawo.

Mumzinda wa Jakarta, womwe ndi likulu la dziko la Indonesia ndipo uli pachilumba cha Java, ndinalalikira mtsikana wina wa zaka 19. Mtsikanayu ankaoneka wosasangalala ndipo ndinamuuza zimene Baibulo limanena zoti anthu adzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Nditamuwerengera Baibulo, iye anayamba kulira. Kenako anandiuza mwaulemu komanso mwachikondi kuti, “Zikomo kwambiri amayi pondiuza zinthu zimenezi. Kutereku mawa ndimafunika kupeza ndalama zina zokwana madola 160 zokalipirira ku yunivesite. Ndiyeno ndimaganiza zochita zachiwerewere kuti ndipeze ndalamazo, ngakhale kuti sindinagonepo ndi mwamuna. Tisanakumane, ndakhala ndikupemphera kuti ndidziwe chochita. Panopa, ndikuona kuti pemphero langa layankhidwa. Ndikuona kuti m’malo mochita chiwerewere, ndi bwino kuti ndidikire kaye zopita ku yunivesitezo.” Mtsikanayu anapitirizabe kuphunzira zinthu za m’Baibulo, ndipo ankasangalala nazo kwambiri.

Kuyambira nthawi imeneyi, anthu enanso ambiri a mtundu wa Chijava, Chisunda ndi Chitchaina, asintha moyo wawo kuti zochita zawo zizigwirizana ndi mfundo zabwino zimene Baibulo limaphunzitsa. Mogwirizana ndi zimene Mulungu analonjeza, zimenezi zawathandizanso kukhala ndi mtendere wamumtima komanso kukhala osangalala.—Yesaya 48:17, 18.

 Tinalalikiranso ku Kalimantan, Kwawo kwa Anthu a Fuko la Dayak

Kenako ine ndi Josef tinachoka ku Java n’kupita ku Kalimantan. Chimenechi ndi chigawo chomwe chili pachilumba cha Borneo, m’dziko la Indonesia. Borneo ndi chilumba chachitatu pa zilumba zikuluzikulu padziko lonse (chachikulu kwambiri ndi Greenland, kenako New Guinea). Chilumba cha Borneo chili ndi nkhalango zowirira, mapiri ataliatali ndi mitsinje ikuluikulu. Pachilumbachi pamakhala Matchaina, Asilamu ochokera ku Malaysia, ndi anthu a mtundu wa Dayak omwe ndi mbadwa za pachilumbachi. Anthu a mtundu wa Dayak amakonda kukhala m’mphepete mwa mtsinje ndipo kale akuti ankapha anthu n’kumawadula mitu.

Kuti tikafike kwa anthu a mtundu wa Dayak, tinkayenda m’mitsinje ya m’nkhalango pa bwato. Tikamayenda m’mitsinje imeneyi, tinkaona ng’ona zitadziyanika padzuwa m’mphepete mwa mtsinje, anyani akudumphadumpha m’mitengo, ndiponso mbalame zokongola zosiyanasiyana zikuuluka. Umishonale unkasangalatsa kwambiri kudera limeneli.

Anthu ambiri a mtundu wa Dayak ankamanga nyumba za mitengo ndi udzu, ndipo ankazimanga pathandala mumtsinje. Nyumba zina zinkakhala zazing’ono ndipo zina zinkakhala midadada italiitali, yokhala mabanja angapo. Anthu ambiri anali asanaonepo mzungu, choncho ankachita chidwi kwambiri ndi Josef. Ana a m’mudzi ankamuthamangira n’kumakuwa kuti, “Abusa! Abusa!” Kenako anthu ambirimbiri ankakhamukira kwa ife kuti adzamvetsere uthenga umene m’busa wachizunguyo wawabweretsera. Josef akamalankhula, Mboni za kuderako zinkamasulira ndipo zinkakonza zoti ziziphunzitsa Baibulo anthu ambirimbiri amene anali ndi chidwi.

Tinasamukira ku Papua New Guinea

Chifukwa chokakamizidwa ndi zipembedzo zodana ndi Mboni za Yehova, boma la Indonesia linaletsa chipembedzo cha Mboni za Yehova mu December 1976. Choncho ine ndi Josef tinatumizidwa ku Papua New Guinea.

Titafika ku Port Moresby, lomwe ndi likulu la dziko la Papua New Guinea, tinachita maphunziro a miyezi iwiri a chilankhulo cha Chihiri Motu, chomwe anthu amachigwiritsa ntchito pochita malonda m’dzikoli. Kenako tinasamukira kuchilumba chaching’ono chotchedwa Daru, chomwe chili kudera lakumudzi m’chigawo chakumadzulo kwa dzikoli. Kumeneko, ndinakumana ndi Eunice, mzimayi wonenepa, wamphamvu, komanso wansangala kwambiri. Mano ake anali othimbirira chifukwa chakuti kwa zaka zambiri ankatafuna mtedza winawake woledzeretsa. Eunice ataphunzira kuti Mulungu amafuna kuti atumiki ake azikhala oyera, a makhalidwe abwino, komanso azimulambira m’njira imene iye amafuna, anasiya chizolowezi chake chotafuna mtedza woledzeretsa uja ndipo anakhala Mkhristu wokhulupirika. (2 Akorinto 7:1) Nthawi zonse tikaona anthu odzichepetsa ngati amenewa akuyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo, tinkamvetsa bwino lemba la Salimo 34:8, lomwe limati: “Talawani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino.”

Patapita nthawi, Josef anayambiranso kuyendera mipingo ndipo tinayendera pafupifupi dera lililonse ku Papua New Guinea. M’dzikoli muli zinenero pafupifupi 820. Kuti tizitha kulankhula ndi anthu ambiri, tinaphunziranso chinenero china cha m’dzikoli powonjezera pa zinenero zimene tinkadziwa kale. Tinaphunzira Chitoku Pisini, chimene anthu a zinenero zosiyanasiyana m’dzikoli amagwiritsa ntchito kuti amvane. Popita kumatauni ndi kumidzi yosiyanasiyana m’dzikoli, tinkayenda pansi, pa galimoto, pa boti, pa bwato, ndi pa ndege zing’onozing’ono. Kuderali kunkatentha kwambiri ndiponso kunali udzudzu wambiri, choncho tinkadwaladwala malungo.

Kenako mu 1985 tinapemphedwa kuti tikakhale amishonale kudziko linanso, ku Solomon Islands, kum’mawa kwa Papua New Guinea. Kumeneko tinkagwira ntchito pa ofesi ya Mboni za Yehova ndipo tinkayendanso m’dziko lonselo kupita kumipingo yosiyanasiyana kukailimbikitsa ndiponso kukachititsa misonkhano ikuluikulu yachikhristu. Titafika m’dzikoli tinafunikanso kuphunzira chinenero china chatsopano, Chipijini cha m’dzikoli. Zimenezi zinatithandiza kuti tizisangalala kwambiri tikamacheza ndi anthu okonda Baibulo a m’dzikoli.

Nthawi Yovuta Kwambiri pa Moyo Wanga

Mu 2001, boma la Indonesia linavomerezanso chipembedzo cha Mboni za Yehova. Choncho ine ndi Josef tinabwerera ku Jakarta. Koma pasanapite nthawi yaitali, mwamuna wanga wokondedwa anayamba kudwala khansa yoipa kwambiri ya pakhungu. Chifukwa cha matendawa, tinapita kwawo ku Germany kuti akalandire chithandizo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti mu 2005, pa tsiku limene tikanakondwerera kuti takhala m’banja zaka 33, mwamuna wanga anamwalira. Panopa ali m’tulo, kudikirira nthawi yomwe adzaukitsidwe n’kukhalanso ndi moyo m’dziko latsopano la paradaiso. (Yohane 11:11-14) Iye anamwalira ali ndi zaka 62 ndipo anali atatha zaka 40 akuchita utumiki wa nthawi zonse.

Ndinapitiriza kukhala ku Jakarta, kumene ndikutumikirabe monga mmishonale. Ndimamusowa kwambiri mwamuna wanga. Koma kuphunzitsa ena choonadi chamtengo wapatali chopezeka m’Mawu a Mulungu kumandithandiza kupirira. Ntchito imeneyi imandithandiza kukhala wosangalala komanso kukhala ndi cholinga pa moyo wanga. Ndinganenedi kuchokera pansi pa mtima kuti Yehova wandithandiza kukhala ndi moyo wosangalatsa komanso wopindulitsa kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Masiku ano ku Java kuli anthu opitirira 120 miliyoni.

[Mapu patsamba 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

INDONESIA

Java

JAKARTA

Cirebon

Sumatra

Padang

Nyanja ya Toba

Borneo

PAPUA NEW GUINEA

PORT MORESBY

Daru

SOLOMON ISLANDS

[Chithunzi patsamba 26]

Herawati ali ndi anthu ena amene ankawaphunzitsa Baibulo ku Solomon Islands

[Chithunzi patsamba 26]

Ndili limodzi ndi Josef ku Holland, atangotsala pang’ono kumwalira mu 2005