Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Sandilola Kupita Kokasangalala?

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Sandilola Kupita Kokasangalala?

 Zimene Achinyamata Amadzifunsa

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Sandilola Kupita Kokasangalala?

Allison * ndi mtsikana wazaka 17 yemwe amakhala ku Australia. Iye amaona kuti Lolemba lililonse limamutopetsa kwambiri akapita kusukulu.

Iye anati: “Aliyense amangokhalira kunena zimene anachita Loweruka ndi Lamlungu. Iwo amanena zinthu zosonyeza kuti anasangalala kwambiri monga za maphwando osiyanasiyana amene anapitako, anyamata osiyanasiyana amene anakisana nawo, ngakhalenso mmene anathamangitsirana ndi apolisi . . . Zimamveka zochititsa mantha koma zosangalatsa. Amafika panyumba 5 koloko m’mawa koma makolo awo sakhala nazo ntchito. Koma ineyo ndimafunika kupita kokagona iwo asanapite n’komwe kokasangalala.

“Anzangawo amati akamaliza kundiuza zinthu zosangalatsa zimene anachita Loweruka ndi Lamlungu, amandifunsa ineyo kuti ndifotokoze zimene ndinachita. Koma ndimasowa chowauza chifukwa chakuti Loweruka ndi Lamlungu ndimangopita kumisonkhano ya mpingo ndiponso kokalalikira. Ndimaona kuti ndinamanidwa zinthu zambiri zosangalatsa. Choncho, nthawi zambiri ndimangowauza kuti palibe chimene ndinachita. Ndiyeno amafuna kudziwa kuti nanga n’chifukwa chiyani sindinapite nawo.

“Lolemba likatha, ndimayembekezera kuti mwina zinthu zikhalako bwino. Koma sizikhala choncho. Pofika Lachiwiri, aliyense amakhala atayamba kunena za zimene achite Loweruka ndi Lamlungu likubweralo. Nthawi zambiri ndimangokhala phee n’kumawamvetsera. Ndimaona kuti ndine wotsalira kwambiri.”

KODI inunso mumakumana ndi zofanana ndi zimenezi Lolemba kusukulu? Mungamaone ngati kuti makolo anu akutsekerani m’nyumba kuti musatuluke pamene anzanu akusangalala panja. Kapenanso mungamaone ngati mwapita kumalo kwinakwake kokasangalala koma simukuloledwa kuchita nawo masewera alionse. Mwina cholinga chanu si kuchita zonse zimene anzanu amachita, koma mumangofuna kusangalalako nthawi zina. Mwachitsanzo, kodi ndi zinthu ziti zimene mungafune kuchita Loweruka ndi Lamlungu likubwerali?

kuvina

kupita kukaonerera oimba

kukaonera filimu

kupita kuphwando

zina ․․․․․

Kuchita zinazake kuti musangalale n’kofunika. (Mlaliki 3:1, 4) Ndipotu Mlengi wanu amafuna kuti muzisangalala ndi unyamata wanu. (Mlaliki 11:9) Makolo anunso amafuna kuti muzisangalala, ngakhale kuti nthawi zina mungakayikire zimenezi. Komabe, makolo anu angafune kudziwa zinthu ziwiri zofunika izi: (1) Muzikachita chiyani? (2) Mupitako ndi ndani?

Bwanji ngati mwaitanidwa kupita kokasangalala ndi anzanu koma mukukayikira ngati makolo anu angakuloleni? Ngati mukufunika kusankha zochita, Baibulo limalimbikitsa kuti muziganizira za ubwino ndi kuipa kwa zimene mukufuna kuchitazo. (Deuteronomo 32:29; Miyambo 7:6-23)  Ngati anzanu akuitanani, kodi mungasankhe kutsatira njira iti?

NJIRA YOYAMBA: OSAPEMPHA, KUNGOPITA.

Cholinga chanu: Kugometsa anzanu powasonyeza kuti palibe aliyense amene amakuuzani zochita. Mukuona kuti mumadziwa zambiri kuposa makolo anu, ndipo mumaona kuti makolo anu saganiza bwino.—Miyambo 15:5.

Zotsatira zake: Anzanu angaone kuti inuyo mumachita zinthu mwachiphamaso. Angaone kuti ngati mumapusitsa makolo anu, ndiye kuti mutha kuwapusitsanso iwowo. Ngati makolo anu atadziwa, angakhumudwe kwambiri ndipo angaone kuti mwawapusitsa. Mosakayikiranso, akhoza kukupatsani chilango. Kungopita kokasangalala kumene inuyo mukufuna osauza makolo anu, si nzeru ngakhale pang’ono.—Miyambo 12:15.

NJIRA YACHIWIRI: OSAPEMPHA, OSAPITA.

Cholinga chanu: Mukuganizira zimene anzanu akupemphani kuti mukachite ndipo mukuona kuti sizikugwirizana ndi mfundo zimene mumayendera, kapena mukuona kuti anthu ena amene aitanidwa si amakhalidwe abwino. (1 Akorinto 15:33; Afilipi 4:8) Kapena mukufuna kupita, koma mukuopa kupempha makolo anu.

Zotsatira zake: Ngati simukufuna kupita chifukwa chakuti mukuona kuti si bwino kutero, mungawayankhe anzanuwo molimba mtima. Koma ngati simukufuna kupita chifukwa chakuti mukuopa kupempha makolo anu, mukhoza kungokhala ndwii panyumba n’kumadzimvera chisoni kuti anzanu onse akusangalala kupatulapo inu nokha.

NJIRA YACHITATU: KUPEMPHA N’KUONA ZOMWE AYANKHE.

Cholinga chanu: Mukudziwa kuti makolo anu ali ndi udindo wokuuzani zochita ndipo mumaona kuti zimene amanena n’zothandiza. (Akolose 3:20) Mumakonda makolo anu ndipo simukufuna kuwakhumudwitsa pochita zinthu mwamseri. (Miyambo 10:1) Komanso kupempha kumakupatsani mpata wofotokoza bwinobwino maganizo anu.

Zotsatira zake: Makolo anu amaona kuti mumawakonda komanso mumawalemekeza. Ngati ataona kuti pempho lanu ndi lomveka, akhoza kukulolezani kupita.

N’chifukwa Chiyani Makolo Angakukanizeni?

Nanga bwanji ngati makolo anu atakuletsani? Mwina mukhoza kukhumudwa kwambiri. Komabe, ngati mutamvetsa mmene iwowo akuionera nkhaniyo zingakuthandizeni kumvera. Mwachitsanzo, iwo akhoza kukukanizani pa chifukwa chimodzi kapena zingapo zimene zili m’munsizi.

Akudziwa zambiri komanso aona zambiri m’moyo. Mutakhala kuti mukusambira m’nyanja, mwachidziwikire mungakonde kusambira pamalo pamene pali anthu amene amateteza anthu omwe akusambira. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti pamene inuyo mukusangalala m’madzi simungathe kuona bwino ngati kukubwera zinazake zoopsa. Koma oteteza anthu aja amakhala pamalo oti akhoza kuona bwinobwino chilichonse chimene chikuchitika.

Mofanana ndi zimenezi, makolo anu akhoza kuona zoopsa zimene inuyo simungathe kuziona, chifukwa chakuti amadziwa zambiri komanso aona zambiri m’moyo. Mofanana ndi oteteza anthu amene akusambira aja, cholinga cha makolo anu n’chongokuthandizani kupewa zinthu zoopsa, osati kukuletsani kusangalala ndi moyo.

Amakukondani. Makolo anu amafunitsitsa kukutetezani. Iwo amakulolezani kapena kukukanizani kuchita zinthu zina chifukwa cha chikondi. Mukawapempha chinachake, iwo amayamba kaye adzifunsa ngati kukulolezani kuchita chinthucho sikungakubweretsereni mavuto enaake pambuyo pake. Choncho, iwo angakulolezeni pokhapokha ngati atatsimikizira kuti zimene mwapemphazo sizikuikani pa mavuto.

 Chifukwa sakudziwa zonse. Makolo achikondi angaletse mwana wawo kuchita zinthu zina zabwinobwino pofuna kumuteteza. Choncho, ngati makolo anu sanamvetse zimene mukuwapempha, kapena ngati akuona kuti mukubisa zinazake, n’zovuta kuti akulolezeni.

Zimene Zingathandize Kuti Makolo Anu Asakukanizeni

Pali zinthu zinayi zimene zingathandize.

Chilungamo: Choyamba, muyenera kuganizira bwinobwino zolinga zanu. Dzifunseni kuti: ‘Kodi chifukwa chenicheni chimene ndikufuna kupitira kumeneko n’chiyani? Kodi zimene zikachitike kumeneko zimandisangalatsadi kapena ndikungofuna kusangalatsa anzanga? Kodi ndikufuna kupita chifukwa chakuti munthu wina amene amandisangalatsa apitanso?’ Kenako auzeni makolo anu zoona zokhazokha. Pa nthawi ina nawonso anali achinyamata ndipo amakudziwani bwino kwambiri. Ngakhale mutawabisira, iwo angadziwebe zolinga zanu. Choncho angasangalale ngati mutawauza chilungamo, ndipo angakuthandizeni pokuuzani zinthu zanzeru. (Miyambo 7:1, 2) Koma ngati simukuwauza chilungamo, makolo anu angaleke kukudalirani ndipo zimenezi zingachititse kuti azikukanizani zinthu zambiri.

Nthawi imene mwawauzira: Musamapemphe makolo anu zinthu akangofika kunyumba kuchokera kuntchito kapena pamene akuchita zinthu zina. Muziwapempha nthawi imene alibe zochita zambiri. Koma musamawapemphe nthawi itatha kale n’kuwaumiriza kuti akuyankheni msangamsanga. Makolo anu sangasangalale ngati simuwapatsa nthawi yokwanira yoganizira zimene mwawapemphazo. Iwo angasangalale ngati mutamawapempha zinthu nthawi idakalipo.

Muzifotokoza zinthu momveka bwino: Musawasiye m’malere. Afotokozereni bwinobwino zimene mukufuna kuchita. Mwachitsanzo, iwo sangakuloleni kuchoka ngati mutayankha kuti, “Sindikudziwa” atakufunsani mafunso otsatirawa: “Kodi kukakhala ndani ndi ndani?” “Kodi kukakhala munthu wamkulu aliyense?” kapenanso, “Kodi mukamaliza nthawi yanji?”

Musamakayikire zolinga zawo. Musamaone makolo anu ngati adani anu. M’malomwake, muziwaona kuti ali kumbali yanu, chifukwa zoona zake n’zakuti iwo alidi kumbali yanu. Mukamaona kuti makolo anu ali kumbali yanu, simungalimbane nawo ndipo iwo angamakumvetseni kwambiri. Ngati mutawapempha zinazake iwo n’kukana, muziwafunsa mwaulemu kuti akuuzeni chifukwa chake. Mwachitsanzo, ngati akuletsani kukaonerera woimba winawake, yesani kuganizira chifukwa chake. Kodi akuda nkhawa ndi amene akaimbeyo? malo ake? anthu amene apiteko? kapena kuchuluka kwa ndalama zimene mukalipire pakhomo? Musamanene mawu ngati akuti: “N’chifukwa chiyani simundikhulupirira?” “Anzanga onse akupita,” kapena “Anzanga makolo awo awalola kupita.” Asonyezeni makolo anu kuti ndinu munthu wokhwima maganizo pomvera zimene akukuuzani. Mukamawamvera, amakulemekezani ndipo tsiku lina mukadzawapemphanso, zidzakhala zosavuta kuti akulolezeni.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Dzinali talisintha.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]

Makolo anga amandikhulupirira makamaka chifukwa chakuti amaona kuti nthawi zonse ndimayesetsa kuchita zinthu mokhulupirika. Sindimawabisira chilichonse chokhudza anzanga. Komanso sindichita manyazi kusiya phwando lili mkati ngati zimene zikuchitika kumeneko sizikundisangalatsa.

[Chithunzi]

Kimberly

[Bokosi patsamba 12]

FUNSANI MAKOLO ANU

Kodi mukufuna kudziwa maganizo a makolo anu pa zinthu zimene zafotokozedwa m’nkhani ino? Palibenso njira ina imene mungadziwire kuposa kuwafunsa basi. Mukapeza nthawi yoyenera, afunseni kuti akuuzeni nkhawa zimene ali nazo pa nkhani yokulolani kupita kokasangalala. Ganizirani funso limene mungafune kuwafunsa ndipo lilembeni pansipa.

․․․․․

[Bokosi patsamba 12]

Mofanana ndi anthu oteteza anthu amene akusambira m’nyanja, makolo anu angathe kuona bwinobwino zoopsa zimene inuyo simungazione, n’kukutetezani