Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chiyani Chimachititsa Anthu Kuti Azikhulupirira Zamatsenga?

Kodi N’chiyani Chimachititsa Anthu Kuti Azikhulupirira Zamatsenga?

 Kodi N’chiyani Chimachititsa Anthu Kuti Azikhulupirira Zamatsenga?

YANKHO la funso limeneli lingadalire kumene mumakhala, chipembedzo chanu, komanso chikhalidwe chanu. M’madera ena, zinthu zili m’munsizi n’zimene zimachititsa anthu kuti azikhulupirira zamatsenga.

Chidwi Anthu ambiri amakopeka ndi zinthu zamatsenga chifukwa chakuti mwachibadwa, anthu amakhala ndi chidwi chofuna kudziwa zinthu zosamvetsetseka. Choncho ena amakhala ndi chidwi chofuna kudziwa kuti mphamvu imene anthu ochita zamatsenga amagwiritsa ntchito imachokera kuti. Ena amakawombeza kwa asing’anga kuti adziwe amene akuwalodza ndipo ena akaona wina akuchita zamatsenga pamalo enaake amathamangirapo kuti akaone zimene zikuchitika. Enanso amapita kwa anthu amene amati angawathandize kulankhula ndi abale awo amene anamwalira.

Zimawasangalatsa Masiku ano kuli zinthu zambiri zimene anthu ambiri amasangalala nazo monga mabuku, mafilimu ndi masewera a pakompyuta zokhudzana ndi zamatsenga kapena zinthu zachikunja. Zina mwa zinthu zimenezi zimasonyezanso zachiwawa komanso anthu akugonana.

Kudera nkhawa za mawa Baibulo linaneneratu kuti “masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Masiku athu ano ndi nthawidi yovuta, ndipo chifukwa cha mavuto, anthu ambiri amapita kwa anthu ochita zamatsenga monga asing’anga owombeza komanso abusa amene amati amalankhula ndi Mulungu, kuti akawathandize. Munthu wina amene amawombeza anati: “Ntchito imeneyi ndi imodzi mwa mabizinezi amene amayenda kwambiri anthu akakhala pa mavuto. Anthu sabwera kwa ine ngati zinthu zikuwayendera.” Mayi wina wa ku Canada amene amati amalosera zam’tsogolo anati: “Masiku ano zinthu zasintha kwambiri. Panopa ndimalandira mafoni kuchokera kwa anthu amene amapanga mabizinezi akuluakulu. Anthuwa amaimba mafoniwo mwachinsinsi ali m’maofesi awo, koma ngati ali pamalo ena amagwiritsa ntchito mafoni awo a m’manja n’kumalankhula monong’ona.” Iye anapitiriza kuti: “Anthu amenewa kale sankakhulupirira anthu owombeza ndipo ankaona kuti kupita kwa anthu oterewa n’chinthu chochititsa manyazi.”

Matenda Anthu ena amene akudwala kwambiri akaona kuti sakuchira ndi mankhwala akuchipatala, amapita kwa asing’anga. Kumeneko amatha kuuzidwa kuti winawake wawalodza. Kuti achire, nthawi zina iwowo, anzawo, kapena abale awo amatha kuuzidwa ndi sing’angayo kuti alipire ndalama zambirimbiri.

Kudziteteza kapena kupewa tsoka M’mayiko ena a mu Africa, anthu amaitanitsa sing’anga kapena m’busa kuti achotse mizimu yoipa m’mudzi mwawo. Sing’anga kapena m’busayo amatha kumwetsa anthuwo mchape kapena “madzi oyera.” Anthu enanso amapita kwa asing’anga kuti akawapatse mankhwala otsirikira nyumba kapena manda.

Kuteteza ana Ku Papua New Guinea, azimayi ena amakana kutuluka panja usiku ndi mwana wawo wongobadwa kumene, poopa kuti mizimu yoipa ingaphe mwanayo. Ku Uganda ndi m’mayiko ena a ku Africa, azimayi amamangirira mwana wawo mkuzi wokhala ndi mikanda kapena tizigoba ta nkhono m’miyendo ndi m’manja n’cholinga choteteza mwanayo ku mizimu yoipa.

Imfa ya wachibale Munthu wina wolemba mabuku wa ku Britain, dzina lake Sir Arthur Conan Doyle, anakumana ndi mavuto aakulu. Mwana wake wamwamuna, mchimwene wake, mlamu wake ndi mwana wa achemwali ake anaphedwa pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Chifukwa cha chisoni, iye ndi mkazi wake ankapita kwa munthu wina wa zamizimu kuti akawathandize kulankhulana ndi mwana wawo amene anafayo. Masiku anonso, anthu ambiri amapita kwa asing’anga amizimu kuti akawathandize kulankhulana ndi achibale awo amene anafa. M’mayiko ena, zipembedzo zamakolo ndi zipembedzo zina zachikhristu zimaphunzitsa kuti munthu amatha kumwalira chifukwa chakuti mizimu yakwiya. Anthu amachita sadaka ndi miyambo ina yofuna ndalama zambiri n’cholinga choti  asangalatse mizimu. Iwo amakhulupirira kuti ngati sachita zimenezi anthu azingofa pamudzipo.

Kuopa akufa Chifukwa cha zikhulupiriro zimene anthu amakhala nazo zokhudza imfa, anthu ambiri amakhala ndi mantha kwambiri wachibale wawo akamwalira. Mantha amenewa amachititsa anthu m’mayiko ambiri kupanga miyambo yosiyanasiyana monga sadaka ndiponso kudzitematema n’cholinga chosangalatsa wakufayo kapena kuti asonyeze kuti amamukonda. M’madera ena mayi kapena bambo wamasiye amauzidwa kuti avale zovala zakuda ndipo alire maliro kwa miyezi ingapo. Iye amauzidwa kuti pa nthawi imeneyi asatuluke m’nyumba ndiponso asadye zakudya zimene munthu womwalirayo ankazikonda. Munthu amene amauzidwa zimenezi akhoza kuyamba kuvutika maganizo, kudwala chifukwa cha njala, ngakhalenso kufa kumene.

M’nkhaniyi taona kuti pali zinthu zambirimbiri zimene zimachititsa anthu kukopeka ndi zamatsenga. Choncho, n’zofunika kwambiri kufufuza kuti ndi ndani amene amachititsa anthu kukhulupirira zamatsenga. Baibulo ndi buku lokhalo limene lingatithandize kudziwa zoona pa nkhani imeneyi.