Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Ochita Zamatsenga Mphamvu Zake Amazitenga Kuti?

Kodi Anthu Ochita Zamatsenga Mphamvu Zake Amazitenga Kuti?

 Kodi Anthu Ochita Zamatsenga Mphamvu Zake Amazitenga Kuti?

PONENA za Mlengi wathu, Baibulo limati: “Mulungu ndiye kuwala ndipo mwa iye mulibe mdima ngakhale pang’ono.” (1 Yohane 1:5) Zimenezi n’zoona makamaka tikamanena za kuwala kwauzimu. Choncho, kodi zingatheke kuti Mulungu woona azipatsa anthu mphamvu yochitira zamatsenga? Nanga ngati mphamvu zimenezi sizichokera kwa Mulungu, kodi zimachokera kuti?

Anthu ochita zamatsenga nthawi zambiri amakhulupirira mizimu komanso amalosera za m’tsogolo. Ena mwa anthuwa amakhulupirira nyenyezi, amakhulupirira kuti manambala enaake amabweretsa mwayi kapena tsoka, amakhulupirira kuti angathe kudziwa zam’tsogolo poyang’ana zikhatho, amakhulupirira zaufiti, amakhulupirira kuti angathe kulankhula ndi anthu amene anamwalira, komanso amakhulupirira kuti n’zotheka kulodza munthu wina. Zikhulupiriro zimenezi zinayamba kalekale ndipo zambiri zinayambira ku Babulo. Mabwinja a mzinda umenewu masiku ano amapezeka ku Iraq. (Yesaya 47:1, 12, 13) Kenako zamatsengazi zinafalikira padziko lonse ndipo anthu azikhalidwe zosiyanasiyana anayamba kuzikhulupirira kwambiri.

Taganizirani zimene zinachitika mumzinda wa Filipi ku Makedoniya. Kumeneko, mtumwi Paulo ndi mnzake Luka yemwe anali dokotala,  ndiponso Akhristu ena, anakumana ndi mtsikana wina amene ankatha kulosera zam’tsogolo. Kodi mphamvu yochitira zimenezi ankaitenga kuti? Onani zimene Luka analemba. Iye anati: “Tinakumana ndi mtsikana wina wantchito wogwidwa ndi mzimu, chiwanda cholosera zam’tsogolo. Iye anali kupezera mabwana ake phindu lochuluka mwa kumachita zoloserazo.”—Machitidwe 16:16-18.

Apa tikuona kuti Yehova, Mulungu woona, sindiye ankapatsa mtsikanayo mphamvu zolosera zam’tsogolo. M’malomwake, mphamvuzo zinkachokera ku chiwanda chinachake, kapena kuti mzimu woipa. N’chifukwa chake Paulo ndi anzake sanafune kumumvetsera mtsikanayo ngakhale pang’ono. Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi ziwanda n’chiyani? Nanga zinachokera kuti?’ Onani zimene Baibulo limanena pa nkhani zimenezi.

Kodi Ziwanda N’chiyani?

Kale kwambiri, Yehova asanalenge anthu, analenga angelo omwe amadziwikanso kuti ‘ana a Mulungu.’ (Yobu 38:4, 7) Mofanana ndi anthu, Yehova anapatsa angelo ufulu wodzisankhira zochita ndipo kwa zaka zambiri angelo onse anali okhulupirika kwa Mulungu. Koma kenako zinthu zinasokonekera. Kodi chinachitika n’chiyani?

Mulungu atalenga anthu, mngelo wina anayamba kulakalaka chinthu chimene sichinali chake. Iye ankalakalaka kuti anthu azimulambira iyeyo m’malo molambira Mulungu. Mngelo woipayu anagwiritsa ntchito njoka ponyengerera mkazi woyamba, Hava, kuti aphwanye lamulo limene Mlengi wake anamupatsa. (Genesis 3:1-6) Baibulo limatchula mngelo wopandukayo kuti “njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana.” (Chivumbulutso 12:9) Yesu anafotokoza kuti Satana ndi “wopha anthu” yemwe “sanakhazikike m’choonadi.” Anafotokozanso kuti “pamene [Satana] akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.”—Yohane 8:44.

Patapita nthawi, angelo enanso anapandukira Mulungu. (Genesis 6:1, 2) Angelo amenewa anayamba kudziwika kuti “angelo amene anachimwa” komanso “angelo amene sanasunge malo awo oyambirira koma anasiya malo awo okhala,” akumwamba. (2 Petulo 2:4; Yuda 6) Kenako anayamba kudziwika kuti ziwanda. (Yakobo 2:19) Ziwandazi zikuyesetsa mwakhama kusocheretsa anthu ambiri kuti asiye kulambira Mulungu, ngati mmene zinasocheretsera Aisiraeli ambiri kalelo. (Deuteronomo 32:16, 17) Mofanana ndi mmene ankachitira kale, masiku anonso Satana ndi ziwanda zake amagwiritsa ntchito zipembedzo kuti ziziphunzitsa anthu mabodza.—2 Akorinto 11:14, 15.

Dzitetezeni

Ngakhale kuti ziwanda n’zamphamvu kwambiri kuposa anthu, mothandizidwa ndi Mulungu tingathe ‘kulimbana nazo’ n’kuzigonjetsa. (1 Petulo 5:9) Komabe kuti Mulungu atithandize, tiyenera kuphunzira zimene iye amafuna ndi kuyesetsa kuzikwaniritsa. Ponena za Akhristu a m’nthawi yake, mtumwi Paulo analemba kuti: “Sitinaleke kukupemphererani. Takhala tikupemphanso kuti mukhale odziwa molondola chifuniro chake, ndiponso kuti mukhale ndi nzeru zonse komanso muzimvetsetsa zinthu zauzimu. Tikupemphereranso kuti muziyenda mogwirizana ndi zimene Yehova amafuna, kuti muzimukondweretsa pa chilichonse.”—Akolose 1:9, 10.

Ena mwa anthu amene ‘anadziwa zinthu molondolawa’ anali ochita zamatsenga a mumzinda wa Efeso. Iwo ataphunzira choonadi, anasintha kwambiri. Baibulo limati: “Ambiri ndithu amene anali kuchita zamatsenga anasonkhanitsa  mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse.” Mabukuwa anali a ndalama zambiri chifukwa ankakwana “ndalama zasiliva zokwana 50,000.” (Machitidwe 19:17-19) Nkhani imeneyi inalembedwa m’Baibulo n’cholinga choti itipindulitse.—2 Timoteyo 3:16.

Mfundo Zimene Zingatiteteze

Palinso zinthu zina zimene tingachite kuti tidziteteze ku ziwanda. Mwachitsanzo, malangizo a m’Baibulo otsatirawa angatithandize kwambiri.

“Musamakhulupirire mawu alionse ouziridwa, koma muziyesa mawu ouziridwawo kuti muone ngati ali ochokeradi kwa Mulungu.” (1 Yohane 4:1) Zina zimene anthu okhulupirira nyenyezi, asing’anga amizimu komanso anthu owombeza anganene zingakhale zoona. Mwachitsanzo, mtsikana amene anagwidwa ndi ziwanda ku Filipi uja, ananena zoona kuti Paulo ndi anzake anali “akapolo a Mulungu Wam’mwambamwamba, ndipo akulengeza njira ya chipulumutso.” (Machitidwe 16:17) Komabe, Paulo ndi anzake sanalole kuti azichitira zinthu limodzi ndi mtsikanayo. M’malomwake, Paulo analamula kuti mzimu woipawo umuchokere. Choncho, muziyerekezera zimene anthu amaphunzitsa m’matchalitchi osiyanasiyana ndi zimene Baibulo limanena, kuti muone ngati zili zolondola.—Machitidwe 17:11.

“Gonjerani Mulungu, koma tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.” (Yakobo 4:7) Dziwani kuti ziwanda ndi mdani wa Mulungu komanso ndi mdani wanu. Musayese ngakhale pang’ono kuchita chidwi ndi zinthu zoipa zimene ziwanda zimachita. M’malomwake, muzigonjera Mulungu posunga malamulo ake achikondi, omwe ndi osalemetsa. (1 Yohane 5:3) Mwachitsanzo, Mulungu anauza Aisiraeli kuti: “Pakati panu pasapezeke munthu . . . wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa. Pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova.” (Deuteronomo 18:10-12) Mulungu sanasinthe mmene amaonera nkhani imeneyi.—Agalatiya 5:19, 20.

‘Palibe amene angalodze [atumiki a Yehova].’ (Numeri 23:23) Munthu aliyense amene akuyesetsa kusangalatsa Mulungu sayenera kuopa ziwanda. Ndipotu ziwanda “zimanjenjemera” pamaso pa Mulungu chifukwa zimadziwa kuti iye ndi wamphamvu kwambiri ndipo adzagwiritsa ntchito mphamvu zimenezo powononga ziwandazo. (Yakobo 2:19) Mulungu ‘amaonetsa mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye’ ndipo “sadzalola kuti wolungama agwedezeke.”—2 Mbiri 16:9; Salimo 55:22.

“Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Mawu a Mulungu amaphunzitsa kuti munthu akafa, wafa basi. Choncho, palibe chifukwa choopera anthu akufa, chifukwa sangatichite chilichonse choipa. (Yesaya 26:14) Pofuna kunyenga anthu, ziwanda nthawi zina zimayerekezera kukhala mizimu ya anthu akufa. N’chifukwa chake nthawi zina chinthu chimene anthu amati ndi mzimu wa munthu winawake wabwino amene anafa, chimachita zinthu zankhanza zosiyana ndi zimene munthuyo ankachita.

“Sizingatheke kuti muzidya ‘patebulo la Yehova’ komanso patebulo la ziwanda.” (1 Akorinto 10:21, 22) Anthu onse amene amakonda Yehova, ayenera kupewa asing’anga amene amachita zamatsenga, komanso mabuku, mafilimu, ndi masewera a pa kompyuta onena zamatsenga, kapena amene amalimbikitsa kuchita komanso kukhulupirira zamatsenga. * Lemba la Salimo 101:3 limati: “Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chopanda pake.” Komanso, zosangalatsa zosonyeza zamatsenga nthawi zambiri zimasonyezanso zinthu zachiwawa ndi zachiwerewere, zimene anthu “okonda Yehova” ayenera kudana nazo.—Salimo 97:10.

Kuyambira kalekale, ziwanda zakhala zikuyesetsa kudzibisa kuti anthu asazidziwe bwinobwino, koma sikuti zakwanitsa kupusitsa munthu aliyense. Yehova wagwiritsa ntchito Baibulo pothandiza anthu kudziwa kuti ziwanda n’zabodza kwambiri komanso zimadana kwambiri ndi anthu. Ziwandazi n’zosiyana kwambiri ndi Mlengi wathu, Yehova Mulungu. Monga momwe nkhani yotsatirayi ikusonyezera, iye amatikonda, amatiuza zoona nthawi zonse ndipo amafuna kuti tidzakhale ndi moyo wosangalala kwamuyaya.—Yohane 3:16; 17:17.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Chikumbumtima cha anthu chimasiyana mogwirizana ndi chipembedzo chimene anakulira komanso kumvetsa kwawo zinthu zauzimu. Chofunika kwambiri n’chakuti munthuyo akhale ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu komanso asakhumudwitse chikumbumtima cha ena, kuphatikizapo cha anthu a m’banja lake. Lemba la Aroma 14:10, 12 limati: “Tonse tidzaimirira patsogolo pa mpando woweruzira milandu wa Mulungu.”