Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kamchira ka Bakiteriya

Kamchira ka Bakiteriya

Kodi Zinangochitika Zokha?

Kamchira ka Bakiteriya

● Ngakhale kukaunika pa chipangizo champhamvu kwambiri choonera zinthu zing’onozing’ono, kamchira ka bakiteriya kamaoneka kakang’ono zedi komanso kachabechabe. Asayansi ena amayerekezera kamchira kameneka ndi mota yamphamvu kwambiri ya boti. Kamchira ka bakiteriya kamaphunziridwa kwambiri ndi asayansi. Kodi kamchira kameneka kamatani kwenikweni?

Kamchiraka kanalumikizidwa kunja kwa khungu la bakiteriya ndipo kamazungulira, zomwe zimathandiza kuti bakiteriya azitha kupita kutsogolo, kumbuyo, aziima ndiponso azikhota. Akuti mwina theka la mabakiteriya onse amene akudziwika, amakhala ndi michira koma michirayo imakhala yosiyanasiyana.

Mu DNA ya bakiteriya mumakhala “malangizo” a mmene mchira wa bakiteriya udzakhalire komanso zinthu zothandiza kuti mchirawo uzidzazungulira. Mchirawo umapangidwa ndi mitundu yosiyanasiyana ya mapuloteni okwana pafupifupi 40 amene tingawayerekezere ndi mbali zosiyanasiyana za mota. Chochititsa chidwi n’chakuti zimatenga mphindi 20 zokha kuti mapuloteni amenewa asonkhanitsidwe n’kupanga mchira wozungulira mothamanga kwambiri umenewu.

Buku lina linati: “Kamchira ka bakiteriya kamakhala ndi mota imene imazungulira maulendo 6,000 mpaka 17,000 pa mphindi imodzi. Chogometsanso kwambiri n’chakuti kamatha kukhota mofulumira kwambiri, n’kuyambiranso kuzungulira maulendo 17,000 pa mphindi imodzi.” (The Evolution Controversy) Magazini ina inanena kuti kamchira ka bakiteriya ndi “chitsanzo chabwino kwambiri chosonyeza kugometsa kwa selo, ndipo n’zovuta kuti anthu asayansi apange kachipangizo kakang’ono kwambiri kogwira ntchito mogometsa ngati kamchira kameneka.”—New Scientist.

Asayansi amagoma kwambiri kuti mapuloteni 40 a kamchira ka bakiteriya amadzisonkhanitsa okha, ndipo puloteni iliyonse imafikira pamalo pake. Zimenezi zimathandiza kuti kamchiraka kazigwira ntchito bwino kwambiri.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti bakiteriya akhale ndi kamchira kameneka, kapena alipo amene anakapanga?

[Chithunzi patsamba 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Chimene chimazunguliritsa mchira

Chothandiza kuti mbali ziwiri zisamakhulane

Polumikizira

Mchira

Kamchira ka bakiteriya

[Chithunzi]

bakiteriya (tamukulitsa)

[Mawu a Chithunzi]

Bacterium inset: © Scientifica/Visuals Unlimited, Inc.; flagellum: Art source courtesy of www.arn.org