Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Choonadi cha m’Baibulo Chinawamasula

Choonadi cha m’Baibulo Chinawamasula

Choonadi cha m’Baibulo Chinawamasula

YESU KHRISTU anauza anthu enaake amene ankamumvetsera, kuti: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Monga momwe zitsanzo zotsatirazi zikusonyezera, choonadi chimamasulanso anthu ku ziwanda, zomwe zimanamiza ndiponso kupusitsa anthu pogwiritsa ntchito matsenga.—Yohane 8:44.

Chitsanzo chilichonse chotsatira chikusonyeza mphamvu yomasula anthu imene choonadi cha m’Baibulo chili nayo. Inde, Baibulo lokha ndi limene limamasuladi anthu. Tikukupemphani kuti muliphunzire mofatsa, ndipo silidzakukhumudwitsani.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 8]]

Zithunzizi n’zongoyerekezera, si za anthu amene tawafotokoza m’nkhaniyi

Susanna anali wansembe wapakachisi ku Brazil. Iye ankachita zinthu zamatsenga kuti athandize anthu ovutika. Komanso, ankakonda “kulankhula ndi mayi ake amene anamwalira.” Koma patapita nthawi, amene ankaganiza kuti ndi mayi akewo anam’pempha kuti adziphe n’cholinga choti akakhale nawo limodzi kumalo amizimu. Zimenezi zinkamuvutitsa kwambiri maganizo Susanna ndipo ankakhalira kulota zinthu zoopsa. Kenako iye ndi mwamuna wake anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iwo anachita khama kwambiri kuti athe ‘kutsutsana ndi Mdyerekezi,’ ndipo pamapeto pake iye ‘anawathawa.’ (Yakobo 4:7) Panopa iwo savutitsidwanso ndi ziwanda ndipo Susanna anasiya kulota zinthu zoopsa. Iye analemba kuti: “Ndimathokoza Yehova kuti wandichitira zinthu zambiri, koma chimene ndimamuthokoza nacho kwambiri n’chakuti anatichotsa mu mdima wauzimu.”

[Bokosi/Chithunzi patsamba 8]

Timothy, yemwe amakhala ku West Africa, ndi wogontha komanso wosalankhula. * Iye anayesa kupita kuzipatala zosiyanasiyana kuti amuthandize koma zinakanika. Kenako anapita kwa abusa osiyanasiyana kuti akamupempherere, koma sizinathandizenso. Iye analemba kuti: “Ndinakhumudwa kwambiri chifukwa cha chinyengo cha abusawo.” Kenako Timothy anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iwo anamuuza kuti Mulungu ali ndi cholinga chothetsa matenda ndi kulumala kwamtundu uliwonse padzikoli. Timothy anati: “Ndimayembekezera mwachidwi dziko latsopano la Mulungu chifukwa ndimadziwa kuti m’dziko limeneli ‘maso a anthu akhungu adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva. . . . Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.’” (Yesaya 35:1-6) Masiku ano, iye amakonda kugwiritsa ntchito wailesi yam’manja ya DVD pophunzitsa anthu ogontha choonadi cha m’Baibulo, ndipo zimenezi zikuthandiza kuti iwonso amasuke.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Tasintha mayina ena.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

Evelyn yemwe amakhala ku Estonia ankakonda kwambiri kuchita zamatsenga. Iye ankafuna kuti azichiritsa anthu monga mmene ankachitira Yesu. Ankalakalaka kwambiri atachiritsa mayi ake amene anali ndi matenda enaake aakulu. Choncho, iye anaphunzira kuchita maula kuti azitha kutulukira matenda akuluakulu komanso kuwachiza. Patapita nthawi, Evelyn anayamba kuphunzira Baibulo. Zimenezi zinamuthandiza kwambiri. Iye anati: “Ndinafika pozindikira kuti ndakhala ndikupusitsidwa kwambiri. Choncho, ndinawotcha mabuku anga onse a zamatsenga ndi zinthu zina zochitira maula.” Panopa nayenso amaphunzitsa anthu Baibulo n’cholinga chakuti nawonso amasuke.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

Mary anakulira pachilumba chinachake cha ku Papua New Guinea kumene anthu ambiri amaopa akufa. M’mudzi mwawo mukachitika maliro, Mary ankagona pansi pa bedi la munthu wina, poopa kuti akagona yekha mzimu wa munthu wakufayo uzimuvutitsa. Kenako iye anaphunzira kuchokera m’Baibulo kuti munthu akafa amakhala ngati ali m’tulo ndiponso kuti amapita kumanda komwe amayembekezera kuukitsidwa n’kudzakhala ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi. (Luka 23:43; Yohane 11:11-14) Chifukwa chophunzira zimenezi iye saopanso anthu akufa.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

Alicia, yemwe amakhala ku United States anakulira m’banja la Mboni za Yehova koma ankakonda kuwerenga mabuku komanso kuonera mafilimu a zamatsenga. Kenako anayamba kuganizira mofatsa za choonadi cha m’Baibulo chimene anaphunzira. Atazindikira kuti iye wakhala ‘akudya patebulo la Yehova komanso patebulo la ziwanda,’ anasiya kukhulupirira zinthu zamatsenga ndipo panopa ali ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu.—1 Akorinto 10:21.