Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

 Zochitika Padzikoli

Ku Tanzania, dokotala mmodzi amasamalira odwala pafupifupi 64,000.—THE CITIZEN, TANZANIA.

‘Padziko lonse pali anthu osauka oposa 1 biliyoni amene akudwala chifukwa chosowa zakudya, ndipo zimene bungwe la UN linakonza zoti pofika chaka cha 2015 njala idzakhale itachepa kwambiri, sizidzatheka.’—SCIENCE, U.S.A.

“Mu 2008, mayiko 100 amene amapanga kwambiri zida zankhondo padziko lonse, anapeza ndalama zokwana madola 385 biliyoni, zomwe ndi zopitirira ndi madola 39 biliyoni kuposa zimene anapeza m’chaka cha 2007.—STOCKHOLM INTERNATIONAL PEACE RESEARCH INSTITUTE, SWEDEN.

Akuti Majelemusi ndi Abwino Nthawi Zina

Mphunzitsi wina wa payunivesite ya Northwestern, ku Illinois, m’dziko la United States, dzina lake Thomas McDade, anati: “Titafufuza tapeza kuti munthu akamakhala malo aukhondo kwambiri ali mwana, akakula amadzadwaladwala.” Pa kafukufuku wina amene anayerekezera ana a ku Philippines ndi a ku America, anapeza kuti ana ambiri a ku Philippines ankadwala pafupipafupi ali ana. Komabe, mosiyana ndi zimene ochita kafukufukuwo ankayembekezera, achinyamata a ku Philippines anapezeka kuti magazi awo amasonyeza kuti sadwaladwala. Chifukwa cha zimenezi, ochita kafukufukuwo anati thupi la munthu likamalimbana ndi majelemusi ambiri ali mwana, zimamuthandiza kuti akadzakula asamadzadwaledwale.

Akuseweretsa Ntchito

Mabwana ambiri ku Finland akudabwa kwambiri kuti anthu amene akuwalemba ntchito masiku ano akuoneka kuti alibe chidwi chosamala ntchito ngakhale pang’ono. Anne Mikkola, mkulu wa malo enaake odyera, atafunsidwa ndi mtolankhani wa wailesi ya boma ku Finland, anati: “Anthuwa amaganiza kuti akhoza kubwera kuntchito ndiponso kuweruka nthawi iliyonse imene akufuna.” Mavuto enanso akukhudza khalidwe ndiponso kavalidwe. Chifukwa chakuti antchito ambiri savala bwino, nthawi zina mabwana amachita kuwauza zovala zoyenera kuvala. Chinanso chimene chikusonyeza kuti anthu sakuona kusiyana pakati pa malo a ntchito ndi kunyumba kwawo n’chakuti azinzawo amabwera kudzacheza nawo kuntchitoko nthawi iliyonse.

Chilengedwe Chathetsa Mkangano wa Malo

Mkangano womwe wakhalapo kwa nthawi yaitali pakati pa dziko la Bangladesh ndi India wolimbirana kachilumba kenakake kamene kali pafupi ndi gombe la Bengal watha. Mkanganowu watha kachilumbako katamira chifukwa cha kuchuluka kwa madzi m’nyanja. Pachilumbachi sipakhala anthu. Anthu a ku India amachitcha kuti New Moore, pamene a ku Bangladesh amachitcha kuti South Talpatti. Chilumbachi chinali pamalo otsika kwambiri osakwana mamita 1.9 kuchoka pamwamba pa nyanja kupita m’mwamba. Koma zithunzi zaposachedwapa zojambulidwa ndi masetilaiti zikusonyeza kuti chamira. Pulofesa Sugata Hazra wapayunivesite ya Jadavpur mumzinda wa Calcutta ku India, yomwe imaphunzitsa zinthu zokhudzana ndi nyanja, anati: “Mkangano umene mayiko awiriwa analephera kuuthetsa pambuyo pokambirana kwa zaka zambiri watha chifukwa cha kusintha kwa nyengo.”