Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mbali ya Diso Yomwe Imatithandiza Kuona

Mbali ya Diso Yomwe Imatithandiza Kuona

 Kodi Zinangochitika Zokha?

Mbali ya Diso Yomwe Imatithandiza Kuona

● Diso la munthu lili ndi mbali inayake yomwe imakhala ndi maselo pafupifupi 120 miliyoni. Maselowa amasintha kuwala kochokera ku zinthu zosiyanasiyana komwe kwalowa m’maso n’kukhala uthenga. Kenako uthengawo umatumizidwa ku ubongo, ndipo ubongo umasinthanso uthengawo n’kukhala zinthu zenizeni zoti munthu n’kuzizindikira. Anthu omwe amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha amanena kuti pamalo pamene maselowa ali m’diso la munthu ndi umboni wakuti diso silinachite kulengedwa ndi winawake.

Taganizirani izi: Mbali ya diso imene imatithandiza kuona inakhala mozondoka, zomwe zimachititsa kuti maselo amene kuwala kumafikirapo akhale kumbuyo kwenikweni kwa diso. Kuti kuwala kufike m’maselo amenewa kumadutsa m’maselo enanso ambirimbiri. Munthu wina wokhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha, dzina lake Kenneth Miller, anati: “Malo amene maselowa ali amachititsa kuti tisamaone bwinobwino.”

Choncho, anthu okhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha amanena kuti kuzondoka kwa mbali imeneyi ndi umboni wakuti diso silinapangidwe bwino, kapenanso kuti palibe analipanga. Wasayansi wina anafika ponena kuti “kuzondoka kwa mbali imeneyi n’kopanda phindu ngakhale pang’ono.” Koma anthu ena ofufuza apeza kuti malo amene maselowa ali ndi abwino kwambiri chifukwa ali pafupi ndi maselo ena amene amapereka okosijeni ndi zakudya, zomwe zimathandiza kuti tiziona bwino. Wasayansi wina, dzina lake Jerry Bergman, ndiponso dokotala wina wa maso, dzina lake Joseph Calkins, ananena kuti: “Maselo amene amapereka okosijeni ndi zakudya akanakhala kuti ali kutsogolo kwa maselo otithandiza kuona, bwenzi tikuona movutikira kwambiri.”

Kuzondoka kwa mbali ya diso imene imathandiza kuona, n’kothandiza kwambiri kwa nyama zimene zili ndi maso ang’onoang’ono. Pulofesa Ronald Kröger, wa payunivesite ya Lund, ku Sweden, anati: “Kuti diso lizitha kuona bwino, pamafunika kukhala kampata pakati pa maselo amene amalandira kuwala ndi timinofu tinatake tooneka ngati galasi, timene timakhala pamwamba pa diso. Popeza pakampata kameneka panadzaza ndi timitsempha topita ku ubongo m’malo mongokhala popanda kanthu, nyama zimene zili ndi maso ang’onoang’ono zimatha kugwiritsira ntchito bwino mpata uliwonse umene uli m’diso.”

Komanso, popeza timitsempha topita ku ubongo tochokera ku mbali ya diso imene imatithandiza kuona n’tothithikana kwambiri ndiponso tili pafupi ndi maselo amene amalandira kuwala, diso limatha kuona ndi kuzindikira zinthu mwamsanga ndiponso molondola.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi kuzondoka kwa mbali ya diso imene imatithandiza kuona kumachititsa kuti tisamaone bwino? Ndipo kodi zinangochitika zokha kuti mbali ya diso imeneyi ikhale yozondoka, kapena alipo amene anaipanga mwanjira imeneyi?

[Chithunzi patsamba 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Maselo amene amalandira kuwala

Kuwala

Maselo amene amapereka okosijeni ndi zakudya

Kuwala

Maselo otithandiza kuona

Mtsempha wopita ku ubongo