Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zipembedzo Zimalakwitsa Pati?

Kodi Zipembedzo Zimalakwitsa Pati?

 Kodi Zipembedzo Zimalakwitsa Pati?

KUNENA kuti zipembedzo ndi zimene zikuchititsa kwambiri kuti anthu asamakhale mwamtendere padzikoli, n’chimodzimodzi ndi kunena kuti nkhondo zikhoza kuchepa ngati kutakhala kuti kulibe zipembedzo. Koma kodi zimenezo n’zoona? Kodi nkhondo zingathe ngati patakhala kuti palibe zipembedzo? Kaya yankho lanu ndi lotani, koma mfundo yosatsutsika ndi yakuti, zipembedzo sizinathandize kuti anthu azikhala mwamtendere. Taonani zinthu zina zimene zikusonyeza zimenezi.

Zipembedzo Zagawanitsa Anthu

Anthu padzikoli ndi ogawanika chifukwa cha kusiyana zipembedzo, ndipo zipembedzo zina zikuluzikulu zimangokhalira kulimbana. Kodi mukuganiza kuti nthawi ina m’tsogolomu zidzatheka kuti Abuda, Ahindu, Akhristu, Asilamu, ndi Ayuda azikhala limodzi mwamtendere?

Chinthu china chomvetsa chisoni n’chakuti zipembedzo zikuluzikulu zimenezi n’zogawanikanso. Mwachitsanzo, anthu ena ochita kafukufuku anapeza kuti padzikoli pali matchalitchi achikhristu okwana 30,000. Nachonso Chisilamu n’chogawanika chifukwa chili ndi magulu amene amakhulupirira zinthu zosiyana. Malinga ndi bungwe lina lofalitsa nkhani la ku Middle East, katswiri wina wa Chisilamu, dzina lake Mohsen Hojjat, posachedwapa anavomereza kuti “chifukwa chakuti Asilamu onse sakhulupirira zinthu zofanana, m’mayiko achisilamu muli mavuto ambirimbiri.” Zipembedzo zinanso zikuluzikulu monga Chibuda, Chihindu ndi Chiyuda zili ndi timagulu tambirimbiri tokhulupirira zinthu zosiyanasiyana.

Zipembedzo Zikulowerera Kwambiri Ndale

Zikuoneka kuti zipembedzo zimalowerera pafupifupi chilichonse. Magazini ina yofalitsa nkhani zachuma inanena kuti: “Anthu achipembedzo ali ndi mphamvu kwambiri pa chilichonse, kuphatikizapo nkhani za malonda. Mfundo zachipembedzo zayambanso kukhudza mmene anthu akugwiritsira ntchito ndalama zawo.” Zimenezi zikuchititsa kuti anthu azikhala ogawanika, osati ogwirizana. Koma pa zonsezi, kulowerera kwa zipembedzo pa nkhani za ndale n’kumene kwasokoneza kwambiri zinthu padzikoli.

Mu lipoti laposachedwapa limene tinalitchula mu nkhani yapita ija, akatswiri a mbiri yakale ananena kuti “nthawi zambiri zipembedzo zimayambitsa nkhondo ngati akuluakulu a zipembedzo akugwirizana kwambiri ndi akuluakulu a boma.” Zimenezi zikutifikitsanso pa mfundo ina yosatsutsika yakuti kuyambira kalekale, zipembedzo zakhala zikugwirizana kwambiri ndi atsogoleri a ndale komanso a nkhondo.

Zimayambitsa Chidani Choopsa

M’mayiko ambiri, zipembedzo zikuluzikulu zakhala ngati zizindikiro zosiyanitsira anthu a mayiko kapena mafuko osiyanasiyana. M’mayiko amenewa anthu akamadana, zimakhala zovuta kudziwa ngati akudana chifukwa chokonda kwambiri dziko lawo, kusiyana mtundu, kusiyana fuko, kapena chifukwa chosiyana zipembedzo. Zinthu zimenezi zikaphatikizana zimachititsa kuti anthu padzikoli asamagwirizane ngakhale pang’ono.

Chodabwitsa kwambiri pa nkhani imeneyi n’chakuti zipembedzo zambiri zimati zimatsogoleredwa ndi Mulungu wotchulidwa m’Baibulo, yemwe ndi Mlengi wathu. Koma kodi n’zomveka kuti Mlengi wamphamvuyonse, wanzeru zonse komanso wachikondi atsogolere zipembedzo zimene zimagawanitsa komanso kuphetsa anthu ambirimbiri?

[Chithunzi patsamba 6]

Mboni za Yehova zambirimbiri zakhala zikuikidwa m’ndende chifukwa chokana kulowerera ndale