Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zipembedzo Zidzachititsa Kuti Anthu Azikhala Mogwirizana?

Kodi Zipembedzo Zidzachititsa Kuti Anthu Azikhala Mogwirizana?

 Kodi Zipembedzo Zidzachititsa Kuti Anthu Azikhala Mogwirizana?

“TIYENI tiyesetse kuti dzikoli likhale malo abwino. Tiyeni tithetse zipembedzo.” Izi n’zimene munthu wina wotchuka wa ku Holland dzina lake Floris van den Berg ananena mu nkhani imene anafalitsa ya mutu wakuti, “Mmene Tingathetsere Zipembedzo Komanso Chifukwa Chake Tiyenera Kuchita Zimenezi.” Padziko lonse, akatswiri osiyanasiyana akulimbikitsanso mfundo yomweyi yoti padzikoli pasakhalenso zipembedzo.

Wasayansi wina amene anapatsidwapo mphoto ya Nobel, dzina lake Steven Weinberg, anati: “Anthu padzikoli ayenera kusiya kukhulupirira zinthu zopanda pake zimene zipembedzo zakhala zikuphunzitsa kwa nthawi yaitali.” M’zaka zaposachedwapa, anthu ambiri akhala akunena mwamphamvu kuti mavuto ambiri padzikoli akhoza kutha ngati zipembedzo zitatha. Komanso palembedwa mabuku ambiri odana ndi zipembedzo amene anthu ambiri akuwakonda.

Akatswiri osiyanasiyana a sayansi akhala akukumana kuti akambirane za mmene angathetsere chipembedzo, ndipo akuona kuti zimenezi ziyenera kuchitika mwamsanga. Komanso anthu okhulupirira kuti kulibe Mulungu akhala akufalitsa nkhani zambiri zosapita m’mbali zosonyeza kuti amadana kwambiri ndi chipembedzo. Kodi anthu anzeru komanso olemekezedwa amenewa akuganiza bwino?

Kodi Palibe Chipembedzo Choona?

Mfundo yofuna kuthetsa zipembedzo padzikoli ingakhale yomveka zitakhala kuti zipembedzo zonse n’zabodza ndiponso kuti kulibe Mulungu. Koma bwanji ngati kuli Mulungu? Komanso bwanji ngati padzikoli pali gulu la anthu amene amachita zimene Mulungu amafuna?

Tikafufuza bwinobwino mbiri ya zipembedzo, timaona kuti pali chipembedzo chimodzi chosiyana kwambiri ndi zipembedzo zonse. Ndipo ndi anthu ochepa amene ali m’chipembedzo chimenechi. Chipembedzochi chinakhazikitsidwa ndi Yesu Khristu ndi atumwi ake koma n’chosiyana kwambiri ndi Matchalitchi Achikhristu.

Kodi chimasiyana bwanji ndi Matchalitchi Achikhristu? Chimasiyana nawo m’njira zambiri koma tiyeni tione njira imodzi yokha.

Amatsatira Ufumu Umene “Suli Mbali ya Dziko Lino”

Akhristu oyambirira sankalowerera ndale. Iwo ankachita zimenezi chifukwa chotsatira Yesu, yemwenso sankalowerera ndale. Baibulo limati Yesu kawiri konse anakana mwamphamvu atapemphedwa kuti akhale mtsogoleri wa ndale. (Mateyu 4:8-10; Yohane 6:15) Ndipo Yesu anadzudzula ophunzira ake chifukwa chakuti iwo ankafuna kuchita zinthu zachiwawa kuti amuteteze kuti asamangidwe.—Mateyu 26:51, 52; Luka 22:49-51; Yohane 18:10, 11.

Bwanamkubwa wa Roma yemwe ankalamulira ku Yudeya atafunsa Yesu ngati anali ndi malingaliro alionse oti akhale wandale, Yesu anamuyankha mosapita m’mbali kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino. Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.” (Yohane 18:36) Apa zikuonekeratu kuti Yesu sankalowerera ndale kapena nkhondo m’nthawi yake.

Ophunzira a Yesu ankachitanso chimodzimodzi. Lipoti lofufuza ngati zipembedzo zimayambitsa nkhondo kapena ayi, lomwe talitchula m’nkhani zina zam’mbuyo m’magazini ino, linati: “Akhristu oyambirira ankakhulupirira kuti si bwino kumenya nkhondo. . . . Akhristu ambiri ankakana kulowa usilikali ndipo sankamenya nkhondo.” Yesu ndi atumwi ake ankalimbikitsa anthu kuti azikonda anthu anzawo, kuphatikizapo anthu osawadziwa komanso a mtundu kapena fuko lina. (Machitidwe 10:34, 35; Yakobo 3:17) Choncho, chipembedzo chimene Yesu anayambitsa chinkathandiza anthu kuti azikhala mwamtendere.

Patapita nthawi, Chikhristu chinasokonezedwa ndi nzeru komanso miyambo ya anthu ndiponso anthu amene ankakonda kwambiri dziko lawo.  Lipoti lofufuza ngati zipembedzo zimayambitsa nkhondo limene talitchula kale lija linati: “Constantine, [Mfumu ya Roma] atalowa Chikhristu, Chikhristucho chinakhala ngati gulu la nkhondo. Anthu anayamba kuyendera mfundo za Mfumuyo zofuna kupititsa patsogolo zolinga zake zandale komanso zofuna kulanda madera ambiri, m’malo motsatira ziphunzitso za Khristu, zimene zinkalimbikitsa chifundo. Akhristu, kuphatikizapo Mfumuyo, anayamba kumenya nkhondo m’dzina la chipembedzo.” Apa m’pamene panayambira Chikhristu chonyenga.

Chipembedzo Chosiyana ndi Zipembedzo Zina

Kodi ndiye kuti n’zosathekanso kupeza chipembedzo choona padzikoli masiku ano? Masiku ano pali chipembedzo chinachake chimene chili chosiyana ndi zina. Chipembedzo chake ndi cha Mboni za Yehova. Iwo amatsatira kwambiri chitsanzo cha Akhristu oyambirira kuposa gulu lina lililonse la chipembedzo. Zochita zawo n’zosiyana kwambiri ndi za Matchalitchi Achikhristu. Buku lina lofotokoza za zipembedzo linati chipembedzo cha Mboni za Yehova ndi “chosiyana ndi chipembedzo china chilichonse” chifukwa zikhulupiriro zawo zonse “amazitenga m’Baibulo, limene amaliona kuti ziphunzitso zake n’zapamwamba kwambiri kuposa ziphunzitso zilizonse za anthu.”—The Encyclopedia of Religion.

Mofanana ndi Akhristu oyambirira, Mboni za Yehova sizilowerera pa mikangano ya ndale. Lipoti lina limene linalembedwa ndi koleji inayake ya ku Ukraine yophunzitsa za sayansi, linanena kuti Mboni za Yehova zimayesetsa kukhala mogwirizana ngakhale zikhale zochokera “m’mitundu, mayiko, zipembedzo, ndi zikhalidwe zosiyanasiyana, ndiponso kaya zikhale zolemera kapena zosauka.” Kafukufukuyu anafotokoza kuti Mboni za Yehova sizichita “zinthu zoukira boma” ndipo “zimamvera malamulo a dziko lawo.”

Pulofesa Wojciech Modzelewski wa payunivesite ya Warsaw ku Poland analemba m’buku lake kuti: “Mboni za Yehova ndi gulu lalikulu kwambiri padziko lonse limene anthu ake samenya nawo nkhondo.” Popeza Mboni za Yehova zimatsatira kwambiri chitsanzo cha Akhristu oyambirira, tinganene kuti zakwanitsa kubwezeretsa chipembedzo chimene chinakhazikitsidwa ndi Khristu limodzi ndi atumwi ake. Chikhristu chimenechi n’chimene chimathandizadi anthu kukhala mwamtendere.—Onani bokosi patsamba lotsatira.

Tiyembekezere Zinthu Zabwino

N’zoona kuti anthu ambiri amene amafuna kulambira Mulungu m’njira yovomerezeka, kuphatikizapo atsogoleri ena a chipembedzo, amaipidwa kwambiri ndi chinyengo chimene chili m’zipembedzo zawo. Ndipo tiyenera kuvomereza kuti pali anthu opembedza ambiri amene amachita zonse zimene angathe kuti padzikoli pakhale bata ndi mtendere.

Komabe, ngakhale anthu atayesetsa bwanji, sangathe kuthetseratu mavuto onse amene ali padzikoli. Mneneri Yeremiya analemba kuti: “Munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.

Komabe tili ndi chiyembekezo chakuti kutsogoloku, zinthu zidzayamba kuyenda bwino. Mawu a Mulungu amatiuza kuti padziko lapansi pano anthu azidzakhala mwamtendere. Anthu amenewa azidzangokhala ngati apachibale. Anthu a mitundu  yosiyanasiyana azidzakhala mogwirizana, ndipo sadzagawanikanso chifukwa cha kusiyana mayiko, mitundu, kapena zipembedzo. Iwo adzakhala ogwirizana chifukwa chakuti onse azidzalambira Yehova Mulungu.

Baibulo limanenanso kuti zipembedzo zimene sizilemekeza Mulungu zidzatha. Yesu anati: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha, ndipo mzinda uliwonse kapena nyumba yogawanika siikhalitsa.” (Mateyu 12:25) M’tsogolomu, Mulungu adzaonetsetsa kuti mawu amenewa akwaniritsidwa pa zipembedzo zonse zonyenga.

Baibulo linaneneratu kalekale kuti Mulungu “adzakhala woweruza pakati pa mitundu ndipo adzakonza zinthu.” Ulosiwu umanenanso kuti anthu “adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo. Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:4) Ulosiwu wayamba kukwaniritsidwa panopa. Chipembedzo cha Mboni za Yehova chayamba kale kuthandiza anthu kuti azikhala mwamtendere.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Chikondi n’chimene chimagwirizanitsa Mboni za Yehova

[Bokosi patsamba 9]

Kodi Mboni za Yehova Zimasiyana Bwanji ndi Zipembedzo Zina?

Anthu ambiri amadabwa akaona mmene Mboni za Yehova zimasiyanirana ndi zipembedzo zina zonse zachikhristu. M’munsimu muli zinthu zina zimene zimasiyanitsa Mboni za Yehova ndi zipembedzo zina.

MMENE GULU LAWO LILILI

● Sakhala ndi abusa omwe amaonedwa kuti ndi apamwamba kuposa anthu ena.

● Amishonale awo komanso anthu amene amatsogolera ndiponso kuphunzitsa m’mipingo mwawo salipidwa.

● Sapereka chakhumi ndipo sayendetsa mbale ya zopereka m’malo awo olambirira, amene amatchedwa Nyumba ya Ufumu.

● Ntchito yawo yonse imayendetsedwa ndi zopereka zimene anthu amapereka mosaonetsera.

● Salowerera ndale.

● Amalimbikitsa mtendere ndipo samenya nawo nkhondo.

● Padziko lonse, onse amakhulupirira zinthu zofanana zochokera m’Baibulo ndipo zimenezi zimawachititsa kuti akhale ogwirizana.

● Sasankhana chifukwa cha kusiyana chikhalidwe, mtundu, fuko, kapena kapezedwe ka ndalama.

● Iwo ndi osiyana kwambiri ndi zipembedzo zina, monga za Katolika, Orthodox, kapena Pulotesitanti.

ZIPHUNZITSO ZAWO

● Amakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi yekha woona, yemwe dzina lake ndi Yehova.

● Amatsatira zimene Yesu anaphunzitsa ndipo amamulemekeza monga Mwana wa Mulungu.

● Sakhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mulungu Wamphamvuyonse, ndipo sakhulupirira chiphunzitso cha Utatu.

● Sagwiritsira ntchito mtanda kapena mafano polambira.

● Sakhulupirira kuti anthu oipa akafa, amakapsa ndi moto.

● Amakhulupirira kuti Mulungu adzadalitsa anthu omvera powapatsa moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso.

Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti zakwanitsa kubwezeretsa Chikhristu chimene Yesu ndi atumwi anakhazikitsa.

[Chithunzi patsamba 8]

Munthu wa ku Serbia, wa ku Bosnia, ndi wa ku Croatia