Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chikhulupiriro ndi Kuganiza Mwakuya Zimayenderana?

Kodi Chikhulupiriro ndi Kuganiza Mwakuya Zimayenderana?

 Zimene Baibulo Limanena

Kodi Chikhulupiriro ndi Kuganiza Mwakuya Zimayenderana?

MUNTHU wina wophunzira kwambiri wa ku Britain, dzina lake A. C. Grayling, anati: “Chikhulupiriro ndi kuganiza siziyenderana ngakhale pang’ono.” Zimene Grayling ananenazi n’zimenenso anthu ena ambirimbiri olemba mabuku komanso ophunzira akhala akunena kwa zaka zambiri.

N’zoonadi kuti zinthu zina zimene anthu achipembedzo amakhulupirira n’zosalondola ndipo zilibe maziko ngakhale pang’ono. Koma taganizirani izi: Mfundo zina za sayansi zimene anthu ankazikhulupirira kwambiri m’mbuyomo, m’kupita kwa nthawi zinapezeka kuti n’zosalondola. Ndiye kodi zimenezi zikutanthauza kuti mfundo zonse za sayansi ndi zosalondola komanso siziyenderana ndi kuganiza mwakuya? Ayi. N’chimodzimodzinso ndi chikhulupiriro. Ndipotu mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, n’zosatheka munthu kukhala ndi chikhulupiriro popanda kudziwa zinthu molondola ndiponso kuganiza mwakuya. Pamene mukuwerenga mfundo zili m’munsizi muona kuti chikhulupiriro ndi kuganiza mwakuya zimayenderana.

Chikhulupiriro Chenicheni Chimayenderana ndi Kuganiza Mwakuya

Baibulo limanena kuti ngati tikufuna kuti kulambira kwathu kukhale ‘kovomerezeka kwa Mulungu,’ tiyenera ‘kugwiritsa ntchito luntha lathu la kuganiza,’ kapena kuti tiyenera kulambira Mulungu monga anthu oganiza. (Aroma 12:1) Choncho chikhulupiriro chimene Baibulo limafotokoza sichitanthauza kumangotsatira zilizonse mwachimbulimbuli kapena kumangonena ndi pakamwa. M’malomwake ndi chikhulupiriro chimene munthu amakhala nacho pambuyo poti wafufuza ndiponso kuganizira mwakuya mfundo zinazake n’kuyamba kukhulupirira Mulungu ndi Mawu ake.

Komabe kuti munthu aziganiza bwino, amafunika kuphunzira zinthu zolondola. N’chimodzimodzi ndi kompyuta. Mukompyuta mukaikamo zinthu zabwino, nayonso imatulutsa zinthu zabwino koma mukaikamo zolakwika, imatulutsanso zolakwika. Choncho, mtundu wa chikhulupiriro chanu umadalira kwambiri zinthu zimene mwamva kapena kuphunzira. Ngati mwamva kapena kuphunzitsidwa zinthu zolakwika, chikhulupiriro chanunso chimakhala cholakwika. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti “munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva.”—Aroma 10:17.

Kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro chenicheni ayenera ‘kudziwa choonadi molondola.’ (1 Timoteyo 2:4) Malinga ndi zimene Baibulo limanena, ndi “choonadi” chokha chimene ‘chingamumasule’ munthu kuti asamakhulupirire zinthu zolakwika, kaya zinthuzo zikhale za sayansi kapena zachipembedzo. (Yohane 8:32) Baibulo limatichenjeza kuti ‘tisamakhulupirire mawu alionse.’ (Miyambo 14:15) M’malomwake limatilangiza kuti ‘tizitsimikizira zinthu zonse,’ kapena kuti kuunika bwinobwino zinthu zimene tamva, tisanayambe kuzikhulupirira. (1 Atesalonika 5:21) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi? Chifukwa kukhulupirira zinthu zolakwika n’koopsa. Anthu ena okonda kuphunzira a mumzinda wakale wa Bereya ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yokhala ndi chikhulupiriro chenicheni. Ngakhale kuti anthu amenewa ankafunitsitsa kukhulupirira zimene amishonale achikhristu ankawaphunzitsa, iwo “tsiku ndi tsiku anali kufufuza Malemba mosamala kuti atsimikizire ngati zimene anamvazo zinalidi zoona.”—Machitidwe 17:11.

Kukhulupirira Zimene Baibulo Limanena

Koma bwanji ngati mumakayikira kuti mwina zimene Baibulo limanena si zodalirika? Kodi mungatani kuti muyambe kukhulupirira kuti zimene limanena ndi zolondola? Taganizirani izi: Kodi mumatani kuti muyambe kukhulupirira anthu enaake? Choyamba mumafunika kuwadziwa bwino. Mukaona zimene akhala akuchita kwa nthawi yaitali n’kutsimikizira kuti ali ndi khalidwe labwino, mumayamba  kuwakhulupirira. Mungatsatirenso njira imeneyi kuti muyambe kukhulupirira Baibulo. *

Baibulo limati “chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa, umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” (Aheberi 11:1) Choncho, n’zoonekeratu kuti munthu amene ali ndi chikhulupiriro chenicheni samangotsatira zilizonse, koma amafufuza mwakuya zinthu zimene akuphunzira pogwiritsa ntchito mfundo zodalirika. Kuganizira mwakuya mfundo zimenezi kumachititsa munthuyo kukhulupirira kuti ngakhale zinthu zimene maso ake sangathe kuona, n’zenizeni.

Koma bwanji ngati zimene mukuphunzira zikuoneka kuti zikutsutsana ndi mfundo zimene mwakhala mukuzikhulupirira kwa nthawi yaitali? Kodi ndi bwino kungosiya osachitapo kanthu? Ayi. Ngati taphunzira zinthu zatsopano zimene zikusonyeza kuti zimene takhala tikukhulupirira kwa nthawi yaitali n’zolakwika, ndi bwino kusintha maganizo athu n’kuyamba kutsatira zinthu zatsopanozo. M’Baibulo, Mulungu analonjeza kuti adzadalitsa aliyense amene amafunitsitsa kudziwa choonadi powapatsa mtima wodziwa zinthu, wozindikira ndiponso woganiza bwino.—Miyambo 2:1-12.

Choncho, chikhulupiriro chimene maziko ake ndi Baibulo chimayenderana ndi kuganiza mwakuya. Kodi inuyo chikhulupiriro chanu n’chotani? Anthu ambiri amangotsatira chipembedzo cha makolo awo ndipo sanafufuzepo mwakuya zinthu zimene amakhulupirira kuti aone ngati zili zolondola. Koma sikulakwa kufufuza zinthu zimene mumakhulupirira kuti mutsimikizire ngati kaganizidwe kanu pa zinthu zosiyanasiyana n’kogwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu amanena. (Aroma 12:2) Baibulo limatilangiza kuti: “Muziyesa mawu ouziridwawo kuti muone ngati ali ochokeradi kwa Mulungu.” (1 Yohane 4:1) Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti ‘mukhale okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho,’ ngakhale kuti mungafunike kusiya zimene munkakhulupirira poyamba.—1 Petulo 3:15.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Ngati mukufuna kuti muthandizidwe kudziwa zinthu zolondola zokhudza Baibulo, lemberani kalata ofalitsa a magazini ino.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi n’zoona kuti Baibulo silitilimbikitsa kuganiza mwakuya?—Aroma 12:1, 2.

● Kodi mufunika kudziwa zinthu zotani kuti mukhale ndi chikhulupiriro chenicheni?—1 Timoteyo 2:4.

● Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Baibulo limanena zokhudza tanthauzo la chikhulupiriro?—Aheberi 11:1.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

Mulungu amadalitsa anthu amene amafunitsitsa kudziwa choonadi