Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yogonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yogonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

 Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yogonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

Pamwambo winawake wopereka mphoto, anthu anadabwa kwambiri ataona akazi awiri omwe ndi akatswiri a zisudzo akupsompsonana mwachikondi. Kenako anthuwo anayamba kuwombera m’manja komanso kukuwa mosangalala. Anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha ankaona kuti zimenezi n’zonyaditsa koma anthu ena ankaona kuti anthuwo akungofuna kuchita zinthu zoti atchukirepo. Kwa masiku angapo zithunzi zosonyeza akatswiriwa akupsompsonana zinaonetsedwa maulendo ambirimbiri pa TV komanso anthu mamiliyoni ambiri anaziona pa Intaneti.

MONGA mmene nkhaniyi ikusonyezera, munthu wotchuka akanena poyera kuti amagonana ndi amuna kapena akazi anzake, imakhala nkhani yaikulu pa TV, m’mawailesi komanso m’manyuzipepala. Anthu ena amawatamanda anthu amenewa kuti ndi olimba mtima, pamene ena amaona kuti limeneli ndi khalidwe lochititsa manyazi. Kuwonjezera pa magulu awiriwa, pali anthu enanso ambiri amene amaona kuti kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha ndi nkhani ya makonda chabe. Mnyamata wina wazaka 21, dzina lake Daniel, anati: “Ndili kusukulu, ngakhale ana amene sachita nawo khalidwe logonana amuna kapena akazi okhaokha, ankaona kuti ngati umadana ndi khalidwe limeneli ndiye kuti uli ndi mtima watsankho komanso woweruza ena.” *

Maganizo a anthu pa nkhani za kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha amasiyanasiyana mogwirizana ndi nthawi komanso dera limene anthu akukhala. Koma Akhristu ‘satengeka kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso.’ (Aefeso 4:14) Iwo amayesetsa kutsatira zimene Baibulo limanena.

Ndiye kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha? Ndipo ngati mumatsatira zimene Baibulo limanena pa nkhani ya makhalidwe abwino, kodi mungawayankhe bwanji anthu amene anganene kuti ndinu watsankho, wokonda kuweruza ena, kapena mumadana ndi anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha? Taganizirani zimene mungayankhe mutafunsidwa mafunso otsatirawa.

Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani yogonana amuna kapena akazi okhaokha? Baibulo limanena momveka bwino kuti Mulungu amafuna kuti kugonana kuzichitika pakati pa mwamuna ndi mkazi omwenso ndi okwatirana. (Genesis 1:27, 28; Levitiko 18:22; Miyambo 5:18, 19) Baibulo likamaletsa dama, limatanthauza kugonana kwa pakati pa mwamuna ndi mkazi amene sanakwatirane komanso kwa amuna kapena akazi okhaokha. *Agalatiya 5:19-21.

 Ngati wina atakufunsani kuti: “Kodi maganizo anu ndi otani pa nkhani yogonana amuna kapena akazi okhaokha?”

Mungayankhe kuti: “Si kuti ndimadana ndi anthu amene amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo, koma ndimadana ndi khalidwe lawolo.”

✔ Kumbukirani izi: Inuyo muli ndi ufulu wosankha kutsatira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo ndipo palibe angakuletseni kuchita zimenezo. (Yoswa 24:15) Musamachite manyazi kufotokoza maganizo anu.—Salimo 119:46.

Akhristu ayenera kulemekeza anthu onse, ngakhale amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha. Si choncho? Inde ndi zoona. Baibulo limati: “Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.” (1 Petulo 2:17) Choncho, Akhristu sadana ndi anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha. Iwo amachitira zabwino anthu onse, kuphatikizapo anthu oterewa.—Mateyu 7:12.

Ngati wina atakufunsani kuti: “Popeza mumaona kuti n’kulakwa kugonana amuna kapena akazi okhaokha, kodi zimenezi sizingakuchititseni kuti muziwasala?”

Mungayakhe kuti: “Ayi. Ndimangodana ndi khalidwelo, osati anthuwo.”

✔ Mwinanso mungawonjezere kuti: “Mwachitsanzo, ineyo sindisuta. Ndipo ndimadana kwambiri ndi fodya. Koma tiyerekezere kuti inuyo mumasuta ndipo mumaona kuti fodya ndi wabwino. Sindingadane nanu chifukwa chokhala ndi maganizo amenewo komanso ndikukhulupirira kuti inuyo simungadane nane chifukwa choona kuti fodya ndi woipa, si choncho? N’chimodzimodzinso pa nkhani ya anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha.”

Yesu ananena kuti tizikhala ololera. Kodi zimenezi si zikutanthauza kuti Akhristu ayenera kungowasiya anthu ena kuti azigonana amuna kapena akazi okhaokha ngati akufuna? Yesu sanalimbikitse otsatira ake kuti azingololera khalidwe lililonse. M’malomwake, iye anawaphunzitsa kuti “aliyense wokhulupirira iye” adzapulumuka. (Yohane 3:16) Kukhulupirira Yesu kumaphatikizapo kutsatira malamulo a Mulungu okhudza makhalidwe abwino. Lina mwa malamulowo ndi loletsa kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha.—Aroma 1:26, 27.

Ngati wina atanena kuti: “Anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha sangasinthe chifukwa ndi chibadwa chawo.”

Mungayankhe kuti: “Zoti kaya anthu ena amabadwa ndi chikhumbo chofuna kugona ndi amuna kapena akazi anzawo, Baibulo silinena. Komabe limavomereza kuti makhalidwe ena ndi ovuta kuwasiya. (2 Akorinto 10:4, 5) Kaya anthu ena amakhala ndi chilakolako chofuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzawo, mfundo ndi yakuti Baibulo limalimbikitsa Akhristu kupewa makhalidwe amenewa.

✔ Mfundo yothandiza: M’malo molimbana ndi kufotokoza kuti n’chiyani chimachititsa kuti anthu ena azikhala ndi chilakolako chofuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzawo, tsindikani mfundo yakuti Baibulo limaletsa khalidwe logonana amuna kapena akazi okhaokha. Mungayerekezere chonchi: “Ambiri amanena kuti anthu ena amene amachita zachiwawa amachita zimenezi chifukwa chakuti ndi mmene anabadwira ndipo ngakhale atayesetsa bwanji sangasinthe. (Miyambo 29:22) Kaya zimenezi ndi zoona kapena ayi, koma mwina mukudziwa kuti Baibulo limaletsa kupsa mtima. (Salimo 37:8; Aefeso 4:31) Koma kodi tinganene kuti Baibulo limalakwa kuletsa anthu kuchita zoipa monga chiwawa, popeza kuti anthu ena mwachibadwa sachedwa kupsa mtima?”

Kodi si nkhanza kuti Mulungu amuletse munthu amene mwachibadwa amafuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzake? Anthu amakhala ndi maganizo olakwika amenewa chifukwa chokhulupirira kuti anthu ayenera kumangotsatira chilichonse chimene mtima wawo wawauza pa nkhani ya kugonana. Koma Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anawalemekeza anthu powapatsa ufulu wosankha. Ngati atafuna, iwo akhoza kusankha kupewa kutsatira zilakolako zawo zolakwika zokhudza kugonana.—Akolose 3:5.

Ngati wina atanena kuti: “Ngakhale kuti simugona ndi amuna kapena akazi anzanu, ndikuona kuti  muyenera kusintha mmene mumaonera anthu oterewa.”

Mungayankhe kuti: “Tiyerekeze kuti ineyo ndimadana ndi juga koma inuyo mumaona kuti juga ndi yabwino. Kodi inuyo mungandikakamize kusintha maganizo anga chifukwa chakuti anthu ambirimbiri amakonda juga?”

✔ Kumbukirani izi: Anthu ambiri (kuphatikizapo ogonana amuna kapena akazi okhaokha) amakhala ndi mfundo zabwino zimene amayendera. Mwachitsanzo amadana ndi zinthu monga chinyengo, kupanda chilungamo komanso nkhondo. Baibulo nalonso limaletsa zinthu zimenezi, kuphatikizapo mitundu ina ya kugonana monga kugonana amuna kapena akazi okhaokha.—1 Akorinto 6:9-11.

Zimene Baibulo limanena n’zoti anthu angakwanitse kuzitsatira komanso Baibulo sililimbikitsa tsankho. Limangouza anthu onse kuti “thawani dama,” kaya akhale amene amafuna kugonana amuna kapena akazi okhaokha, kapenanso amuna ndi akazi amene amafuna kugonana asanakwatirane.—1 Akorinto 6:18.

Zoona zake n’zakuti anthu amene amakhala ndi chilakolako chofuna kugonana ndi amuna anzawo kapena akazi anzawo akhoza kudziletsa ngati akufunadi kukondweretsa Mulungu. Tikutero chifukwa pali anthu ambirimbiri amene amakhala ndi chilakolako chogonana ndi amuna kapena akazi koma amayesetsa kupewa dama chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Ena mwa anthu amenewa ndi osakwatira ndipo akusowa munthu womanga naye banja ndipo enanso ambiri ali m’banja koma mnzawoyo ali ndi vuto. Anthu amenewa amatha kukhala mosangalala, ngakhale kuti pali mavuto amenewa.—Deuteronomo 30:19.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Tasintha mayina ena m’nkhaniyi.

^ ndime 7 Mawu akuti dama malinga ndi mmene amagwiritsidwira ntchito m’Baibulo, samangotanthauza kugonana kwa pakati pa mkazi ndi mwamuna amene sanakwatirane. Mawuwa amatanthauzanso kuseweretsana maliseche komanso kugonana m’kamwa kapena kumbuyo.

ZOTI MUGANIZIRE

● Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu amapatsa anthu malamulo okhudza makhalidwe abwino?

● Kodi kutsatira malamulo a m’Baibulo okhudza makhalidwe abwino kuli ndi ubwino wotani?

[Bokosi patsamba 24]

BWANJI ZA AKAZI AMENE AMAGONANA NDI AMUNA KOMANSO AKAZI ANZAWO, KAPENA AMUNA AMENE AMAGONANA NDI AKAZI KOMANSO AMUNA ANZAWO?

Ngakhale kuti amuna ndi akazi amachita zimenezi, zikuoneka kuti akazi amene amagona ndi amuna komanso akazi anzawo ndi amene alipo ambiri ndipo chiwerengero chawo chikuchulukirachulukira. Taganizirani zifukwa zina zimene zikuchititsa zimenezi.

● Kufuna kukondedwa

“Anyamata ena amachita kunena poyera kuti amakonda akazi amene amagonana ndi akazi anzawo. Atsikana amene amadziona kuti ndi otsika amalolera kuchita chilichonse kuti mnyamata awakonde.”—Anatero Jessica, wazaka 16.

● Kufuna kuona kuti zimakhala bwanji

“Atsikana akaona atsikana okhaokha akupsompsonana m’mafilimu kapena pa TV, kapenanso akamvetsera nyimbo yofotokoza zimenezi, amafuna kuyesa kuti aone kuti zimakhala bwanji, makamaka ngati akuona kuti kuchita zimenezi sikulakwa.”—Anatero Lisa, wazaka 26.

● Kukopeka ndi munthu wina

“Nthawi ina nditapita kuphwando ndinakumana ndi atsikana awiri amene amagonana ndi amuna komanso akazi anzawo. Ndiyeno mnzanga wina anandiuza kuti atsikanawo akundifuna. Kenako tinayamba kutumizirana mauthenga a pafoni ndi mmodzi wa atsikanawo ndipo ndinayamba kukopeka naye.”—Anatero Vicky, wazaka 13.

Ngati mukufuna kusangalatsa Mulungu, simuyenera kuyesa dala zinthu zimene Baibulo limanena kuti n’zodetsedwa. (Aefeso 4:19; 5:11) Koma bwanji ngati mumakopeka kwambiri ndi amuna komanso akazi? Ambiri angakuuzeni kuti muyenera kungovomereza kuti ndinu wotere ndiponso kuti musamabise zimenezi. Koma choti mudziwe n’chakuti nthawi zambiri, kukopeka ndi amuna kapena akazi anzako kumangochitika kwa nthawi yochepa pa moyo wa munthu. Lisette, yemwe ali ndi zaka 16, anazindikiranso zimenezi. Iye anati: “Nditauza makolo anga mmene ndinkamvera, iwo anandikhazika mtima pansi. Komanso kusukulu, pa phunziro la sayansi, ndinaphunzira kuti pakati pa zaka 13 ndi 19, thupi la achinyamata limakhala likusinthasintha. Ndikukhulupirira kuti achinyamata ambiri akanakhala kuti amamvetsa zimene zikuchitika m’thupi mwawo, bwenzi akudziwa kuti kukopeka ndi mkazi kapena mwamuna mnzako nthawi zina kumangochitika kwa kanthawi basi. Akanadziwa zimenezi, si bwenzi akumaganiza kuti ali m’gulu la anthu amene amakopeka ndi amuna kapena akazi anzawo.”

Ngakhale ngati kwa nthawi yaitali mwakhala mukukopeka kwambiri ndi amuna kapena akazi anzanu, dziwani kuti Baibulo limanena kuti pali zimene mungachite polimbana ndi vutoli. Mukhoza kusankha kuti musachite zinthu zolakwika zimene mtima wanu umalakalaka. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 42 Ngati mukufuna kudziwa zambiri pa nkhani imeneyi, onani nkhani yakuti “Kodi Ndingapewe Bwanji Mtima Wofuna Kugonana ndi Amuna Kapena Akazi Anzanga?” m’mutu 28 wa buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 23]

Akhristu amapewa zinthu zolakwika ngakhale ngati anthu ambiri akuziona kuti n’zabwinobwino