Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

▪ Pa kafukufuku amene anachitika wokhudza anthu 2,000 ku Germany, panapezeka kuti achinyamata azaka za pakati pa 14 ndi 19 ankaona kuti palibe vuto kuthetsa chibwenzi pa foni kapena pa Intaneti. Koma 80 peresenti ya anthu azaka zoyambira 50 kupita m’tsogolo ananena kuti zimenezi si zabwino ngakhale pang’ono.—FRANKFURTER NEUE PRESSE, GERMANY.

▪ Kafukufuku akusonyeza kuti m’chaka cha 2008 anthu anatumiza mauthenga a pa foni okwana pafupifupi 2.3 thililiyoni.—HITU NEWS, TAHITI.

▪ “Kodi kusuta fodya kumafupikitsa moyo ndi zaka zingati? Kumafupikitsa ndi zaka 5 mpaka 10.”—UC BERKELEY WELLNESS LETTER, U.S.A.

Kafukufuku akusonyeza kuti makompyuta 60 pa 100 alionse a m’ma ofesi ku United States amakhala osathimitsa usiku wonse. Zimenezi zimachititsa kuti chaka chilichonse, makompyutawa atulutse mpweya woipa wokwana matani 14.4 miliyoni.—WORLD WATCH, U.S.A.

Mabasi Akulimbikitsa Kusakhulupirira Mulungu

“N’kutheka kuti kulibe Mulungu. Choncho lekani kudandaula n’kumasangalala ndi moyo.” Nyuzipepala ina inanena kuti mawu amenewa analembedwa pa mabasi 200 omwe amayenda mu mzinda wa London, ku England. Komanso mawuwa analembedwa pa mabasi ena 600 omwe amayenda m’madera ena ku England. Analembedwanso pa zikwangwani zikuluzikulu ziwiri zomwe zili mu msewu wa Oxford ku London. (The Guardian) Anthu amene analemba mawuwa akuti anachita zimenezi chifukwa cha zimene matchalitchi ena amanena kuti anthu osapemphera adzapsa ndi moto. Pa mawu amene anthuwa amalemba amawonjezerapo mawu akuti “n’kutheka.” Amachita zimenezi potsatira malamulo a dziko la Britain olengezera malonda, chifukwa n’zosatheka kutsimikizira kuti Mulungu kulibe. Cholinga chimodzi cha anthuwa ndi kulimbikitsa anthu amene sakhulupirira Mulungu kuti abwere poyera n’kunena maganizo awo.

Si Bwino Kubereketsa Mayi Masiku Asanakwane

Ku United States, amayi ambiri akusankha kubereka ana masiku awo asanakwane. Madokotala akugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana kuti achite zimenezi, kuphatikizapo opaleshoni. Komabe magazini ina inanena kuti “milungu yomalizira ya mayi wapakati ndi yofunikira kwambiri kuposa mmene anthu ankaganizira poyamba.” (The Wall Street Journal) Kafukufuku amene anachitika pa ana 15,000 ongobadwa kumene, anasonyeza kuti mlungu uliwonse womwe mwana amakhalabe m’mimba ya mayi ake kuyambira mlungu wa 32 ndi wa 39, umathandiza kuti mwana abadwe popanda mavuto monga khunyu, matenda a chikasu, kubanika, ndiponso kukha magazi m’mitsempha ya mu ubongo. Ana amene anabadwa pakati pa mlungu wa 32 ndi 36 anawapeza ndi mavuto ena okhudza ubongo. Choncho, madokotala a pa chipatala china cha ana ndi amayi oyembekezera ku United States, amanena kuti ndi bwino amayi oyembekezera asamabereke “asanakwanitse milungu 39, pokhapokha ngati ali ndi vuto linalake.”—The Wall Street Journal.

Kukwera Masitepe N’kothandiza

“Kukwera masitepe kawirikawiri ndi njira yosavuta yothandiza kuti munthu akhale wathanzi,” inatero magazini ya ku Britain (The Lancet). Ofufuza anauza anthu 69 amene amagwira ntchito za mu ofesi kuti azigwiritsa ntchito masitepe m’malo mwa chikepi. Patatha milungu 12, mlingo wa okosijeni amene thupi lawo linkagwiritsa ntchito unawonjezereka ndi 8.6, zomwe zinawathandiza kuti achepetse ndi “15 peresenti matenda amene angachititse kuti iwo afe mwamsanga.” Anthuwo anaonanso kuti “magazi awo anayamba kuthamanga bwino, analibe mafuta ambiri m’thupi mwawo, ankalemera moyenera ndipo anali ndi thupi loongoka.”