Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Makolo—Muziyang’anira Ana Anu

Makolo—Muziyang’anira Ana Anu

Makolo​—Muziyang’anira Ana Anu

“Kale vuto limene linalipo linali kuonera TV nthawi yaitali basi. Koma masiku ano kulinso mavidiyo, makompyuta, ndiponso mafoni am’manja. Zinthu zimenezi zimakhudza kwambiri ana ndipo amazizolowera kwambiri moti satha kukhala popanda zipangizozi . . . Ubongo wawo umazolowera kumvetsera ndiponso kuonerera zinthu pa zipangizozi, moti pakakhala kuti alibe zipangizozi amasowa chochita.”—Anatero Dr. Mali Mann.

ACHINYAMATA ambiri masiku ano sangathe kuyenda popanda kukhala ndi kachipangizo komvetsera kapena foni. Ambiri akukonda zipangizo zimenezi chifukwa chakuti n’zotsika mtengo komanso zikupangidwa mwaluso kwambiri. Kufala kwa zipangizozi kukuchititsa kuti zizikhala zovuta kwa makolo kuyang’anira, kuphunzitsa ndiponso kulangiza ana awo.

Mavuto amenewa angathetsedwe ngati makolo atachita zinthu ziwiri zofunikira kwambiri. Choyamba, makolo ayenera kuzindikira kuti mawu opezeka m’Baibulo palemba la Miyambo 22:15 ndi oona. Lembali limati: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yom’langira idzauingitsira kutali.” Chachiwiri, dziwani kuti zipangizo zamakono zingathandize ana anu komanso zingawasokoneze, ndipo muyenera kuyesetsa kuwathandiza kuti zisawasokoneze.

Yambani Mwamsanga

M’mabanja ambiri, ana amayamba kuonera TV ali aang’ono kwambiri, ndipo masiku ano TV yangosanduka cholerera ana. Koma madokotala ena amanena kuti si bwino kuti ana azionera kwambiri TV chifukwa zingawalepheretse kuchita masewera olimbitsa thupi, zingawasokoneze maganizo, ndiponso angamalephere kusiyanitsa zinthu zenizeni ndi zongoyerekezera. Zingawachititsenso kuti akadzayamba sukulu azidzalephera m’kalasi. Dr. Mali Mann ananenanso kuti ana ena amene amaonera kwambiri TV “amasonyeza zizindikiro za matenda amene amachititsa ana kuti azilephera kukhazikika ndiponso kumvetsera kapenanso ochititsa kuti azisangalala kwambiri komanso kukwiya kwambiri, pamene kwenikweni amakhala kuti alibe matendawa.” Chifukwa cha zimenezi, akatswiri ena amaona kuti si bwino kuti ana osakwanitsa zaka ziwiri azionera TV.

Dr Kenneth Ginsburg, yemwe ndi mneneri wa bungwe lina la madokotala a ana ku America, anati: “Chinthu chofunika kwambiri pa zaka zoyambirira za mwana ndi chakuti azolowerane kwambiri ndi makolo ake. Kuti zimenezi zitheke, makolowo ayenera kulankhula nawo, kusewera nawo ndiponso kuwawerengera mabuku. Makolo ambiri amadziwa kuti kuwerengera ana mabuku osiyanasiyana n’kofunika kwambiri chifukwa kumawathandiza kuti azidzakonda kuwerenga.

N’zoona kuti kudziwa kugwiritsa ntchito kompyuta komanso zipangizo zina zamakono n’kothandiza kwa ana ambiri. Koma ngati mutaona kuti ana anu ayamba kukonda kwambiri kompyuta, kuchita masewera a pa kompyuta ndiponso kugwiritsa ntchito Intaneti, mungachite bwino kuwathandiza kupeza zochita zina. Kodi mungawapezere zochita zotani? Mungawaphunzitse ntchito inayake yamanja, kapena luso loimba monga kugwiritsa ntchito gitala ndi zinthu zina zomwe angamasangalale nazo kwambiri.

Kupezera ana anu zochita zabwino kungawathandizenso kuti akhale oleza mtima, opirira, odziletsa komanso aluso. Makhalidwe amenewa ndi ofunika kwambiri pamoyo wawo kuti ana anu azitha kuthana ndi mavuto amene sangathetsedwe ndi zipangizo zamakono.

‘Nzeru ndi Kulingalira’ N’zofunika kwa Ana

Baibulo limalimbikitsa akulu ndi ana omwe kukhala ndi “luntha la kulingalira.” (Aroma 12:1; Miy. 1:8, 9; 3:21) Luntha limeneli limawathandiza kusiyanitsa zinthu zabwino ndi zoipa, zanzeru ndi zopanda nzeru. Mwachitsanzo, si kulakwa kuchita masewera a pa kompyuta kapena kuonera TV, koma kodi ndi bwino kuwonongera nthawi yaitali pa zimenezi? Komanso si kulakwa kugula zipangizo zamakono ndiponso mapulogalamu a pa kompyuta amene angotuluka kumene, koma kodi ndi bwino kuwononga ndalama zambiri pogula zinthu zimenezi? Ndiyeno kodi mungathandize bwanji ana anu kusankha zinthu mwanzeru pa nkhani imeneyi?

Muziwauza kuipa kwake. Ana sachedwa kuphunzira mmene angagwiritsire ntchito zipangizo zamakono. Komabe nthawi zambiri sazindikira kuipa kwake. Choncho aphunzitseni kuti azitha kuzindikira kuipa kwake ndi mmene angazipewere. Mwachitsanzo, taganizirani malo a pa Intaneti amene anthu amaikapo zinthu zokhudza moyo wawo. N’zoona kuti malowa angathandize achinyamata kuti adziwane ndi anthu ena, koma ndi oopsa chifukwa anthu ena amagwiritsanso ntchito malo omwewa pofufuza ana oti agone nawo kapena kuchita nawo zinazake zolakwika. * (1 Akorinto 15:33) Choncho, makolo anzeru amalangiza ana awo kuti asaike zinthu zachinsinsi zokhudza moyo wawo pa malo amenewa. *

N’zoona kuti ana ali ndi ufulu wochita zinthu zina mwachinsinsi, mogwirizana ndi msinkhu wawo, koma makolo dziwani kuti Mulungu anakupatsani mphamvu ndiponso udindo wophunzitsa ndi kuyang’anira ana anu. (Miyambo 22:6; Aefeso 6:4) Ana anu angaone kuti mukuchita zimenezo chifukwa chowakonda, osati n’cholinga chowasokoneza.

Koma mwina mungafunse kuti, “Popeza kuti sindidziwa kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono zimene ana anga amagwiritsa ntchito, kodi ndingawathandize bwanji?” Ngati ndi choncho, mungachite bwino kuphunzira zina ndi zina zokhudza zipangizozo. Mwachitsanzo Melba, yemwe panopa ali ndi zaka zoposa 90, anayamba kuphunzira kugwiritsa ntchito kompyuta ali ndi zaka zoposa 80. Mayiyu anati: “Tsiku loyamba kuphunzira kompyuta zinkandivuta kwambiri moti ndinafuna kuitayira pawindo. Patapita miyezi ingapo ndinaizolowera, ndipo panopa ndimatha kutumiza uthenga pa Intaneti komanso kuchita zinthu zina mosavuta.”

Muziwaikira malire. Ngati mwana wanu amatha nthawi yaitali akuonera TV, kufufuza zinthu pa Intaneti, kapena kuchita masewera a pa kompyuta, mungachite bwino kukhazikitsa nthawi imene aliyense sayenera kugwiritsa ntchito zinthu zimenezi. Izi zingathandize mwana wanu kudziwa kufunika kwa mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Kanthu kali konse kali ndi nthawi yake.” Zimenezi zikutanthauza kuti pali nthawi yocheza ndi anthu a m’banja lawo, yocheza ndi anzawo, yochita homuweki, ya chakudya, yochita masewera olimbitsa thupi ndi yochitira zinthu zina. (Mlaliki 3:1) Kukhazikitsa malamulo oyenera oti ana anu azitsatira, ndiponso kuonetsetsa kuti malamulowo akutsatiridwa, kumathandiza kuti aliyense asamangochita zimene akufuna. Komanso ana amakhala akhalidwe labwino, oganizira ena ndiponso odziwa kucheza ndi anthu.

M’nkhani yotsatirayi, tikambirana mfundo zingapo zimene zingathandize ana ndi akulu omwe kuti azigwiritsa ntchito zipangizo zamakono moganizira ena komanso mosawononga ndalama.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Makolo mungachite bwino kuwerenga nkhani yakuti, “Ana Akamagwiritsa Ntchito Intaneti Zimene Makolo Ayenera Kudziwa,” mu Galamukani! ya October 2008. Mu Galamukani! ya December 2007 ndi JJanuary 2008, mungapeze nkhani zothandiza zokhudza zinthu zolaula, masewera a pa kompyuta ndiponso Intaneti.

^ ndime 12 Achinyamata ena amatumiza kwa anzawo pa foni zithunzi zolaula zosonyeza iwowo. Khalidwe limeneli ndi loipa ndipo limasonyeza kupanda nzeru, chifukwa kaya cholinga chawo potumizapo ndi chotani, anthu ena akhoza kuziona.

[Chithunzi patsamba 7]

Ana amafunika kuphunzira zinthu zosiyanasiyana zowathandiza kukhala anzeru, oleza mtima komanso opirira