Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthufe Ndi Amodzi

Anthufe Ndi Amodzi

Anthufe Ndi Amodzi

KODI mumawaona bwanji anthu a mtundu kapena fuko lina? Kodi mumaona kuti anthu onse ndi ofanana? N’zomvetsa chisoni kuti ena amaona anthu a mitundu ina kuti ndi otsika? Malinga ndi buku lina lomasulira mawu, “tsankho” limatanthauza “kukhala ndi maganizo akuti mitundu ina ya anthu ndi yanzeru kuposa ina, ndipo kusiyana kumeneku n’kumene kumachititsa kuti mitundu ina izikhala yapamwamba kuposa inzake.”

Maganizo olakwikawa amayambitsa mavuto ambiri. Pulofesa Wen-Shing Tseng analemba kuti maganizo akuti mitundu ina ya anthu ndi yapamwamba kuposa ina ndi amene akhala akuchititsa kuti “anthu ena azichitiridwa nkhanza ndiponso kutengedwa ngati akapolo.” Iye ananenanso kuti maganizo amenewa achititsa kuti anthu ena “azisalidwa pankhani ya zaumoyo, zachuma, ndiponso zandale.” (Handbook of Cultural Psychiatry) N’zomvetsa chisoni kuti ngakhale masiku ano m’mayiko ambiri muli tsankho. Koma kodi maganizo akuti mitundu ina ndi yapamwamba ndi olondola? Kodi sayansi ndiponso Baibulo zimati chiyani pankhani imeneyi?

Kodi Sayansi Imati Chiyani?

Kafukufuku wasayansi amasonyeza kuti si zoona kuti mitundu ina ya anthu imakhala yanzeru kuposa ina. Akatswiriwa anafufuza anthu ochokera ku mayiko osiyanasiyana, ndipo anapeza kuti DNA yawo si yosiyana kwenikweni. * Ndipo akuti anthu amene DNA yawo inali yosiyana kwambiri anali ochokera mu mtundu umodzi pamene DNA ya anthu ochokera m’mitundu yosiyana sinali yosiyana kwenikweni.

Magazini ya Nature inanena kuti, popeza kuti “anthu si osiyana kwenikweni, kudziwa zimenezi kuyenera kutithandiza kuthetsa tsankho.”

Maganizo amenewa si achilendo. Kuyambira mu 1950 nthambi ya bungwe la United Nations yoona za maphunziro, sayansi ndi chikhalidwe inalemba mabuku ambiri omwe cholinga chake chinali kuthetsa tsankho. Mabukuwa ankalembedwa ndi akatswiri ophunzira za anthu ndi chikhalidwe chawo komanso akatswiri ophunzira za DNA. Komabe tsankho silikutha. Choncho, n’zoonekeratu kuti kungodziwa zinthu zimene zimayambitsa tsankho si kokwanira. Anthu ayenera kuchotsa maganizo aliwonse a tsankho m’mitima mwawo. Yesu Khristu anati: ‘Maganizo oipa amachokera mumtima.’—Mateyo 15:19, 20.

Zimene Baibulo Limanena

Baibulo limatha kusintha mitima ya anthu. Mwachitsanzo, kuwonjezera pa kufotokoza mfundo yomwe imagwirizana ndi sayansi yakuti ‘kuchokera mwa munthu mmodzi, Mulungu anapanga mitundu yonse ya anthu kuti akhale pa nkhope yonse ya dziko lapansi,’ Baibulo limafotokozanso kuti ‘Mulungu alibe tsankho koma amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.’ (Machitidwe 10:34, 35; 17:26) Kudziwa kuti Mulungu ndi wachilungamo kumatichititsa kuti tizimukonda kwambiri.—Deuteronomo 32:4.

Yehova Mulungu amafuna kuti tiyesetse kukhala ngati iyeyo posonyeza kuti timamukonda. Lemba la Aefeso 5:1, 2 limati: “Khalani otsanzira Mulungu, monga ana okondedwa, ndipo yendanibe m’chikondi.” “Kuyendabe m’chikondi” kumaphatikizapo kukonda anthu ngati mmene Mulungu amachitira, popanda kutengera mtundu kapena khungu lawo.—Maliko 12:31.

Mulungu safuna kuti anthu amene ali ndi mitima yoipa, kuphatikizapo atsankho, akhale atumiki ake. (1 Yohane 3:15) Ndipotu posachedwapa Mulungu adzawononga anthu onse oipa padziko lapansi pano. Anthu amene adzapulumuke ndi okhawo amene amatsatira makhalidwe ake. Panthawiyi anthu onse adzakhala banja limodzi, mwakuthupi komanso mwauzimu.—Salmo 37:29, 34, 38.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Komabe, kusiyana kochepa kumeneku kumatha kuchititsa kuti mitundu ina izidwala kwambiri matenda ena kuposa mitundu ina.

[Mawu Otsindika patsamba 23]

“Anthu si osiyana kwenikweni”